Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 18:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangoŵaona, adanyamuka mwamsanga kukaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tsono Abrahamu atakweza maso ake patali anangoona anthu atatu atayima cha potero. Atawaona, ananyamuka mofulumira kuti awachingamire. Atafika anaweramitsa mutu pansi mwa ulemu nati,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 18:2
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Mulungu ananena naye kuti,


Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.


Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova.


Mbuyanga, ngatitu ndi ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu;


Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.


Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo.


Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m'dzikomo, ana a Hiti.


Ndipo Isaki anatuluka kulingalira m'munda madzulo; ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taona, ngamira zinalinkudza.


Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakucha.


Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.


Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.


Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.


Yudanso ndi abale ake anadza kunyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake.


Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa maondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi.


Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pake, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwake.


Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.


Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.


Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?


mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:


Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.


Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa