Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:7 - Buku Lopatulika

7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chauta, Mulungu Wakumwamba, adanditenga kwathu m'banja mwa bambo wanga ndi m'dziko limene ndidabadwira, ndipo adandilonjeza molumbira kuti, ‘Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako.’ Chautayo adzatuma mngelo wake wokutsogolera, ndipo kumeneko udzamutengera mkazi mwana wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehova Mulungu wakumwamba amene ananditenga kwa makolo anga nanditulutsa mʼdziko lobadwira, ameneyo anayankhula nane molumbira kuti, ‘Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko ili.’ Iyeyu adzatumiza mngelo wake kuti akutsogolere kumeneko kukapezera mwana wanga mkazi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:7
39 Mawu Ofanana  

chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.


Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:


Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa panjira ya ku Suri.


Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.


Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.


Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano.


ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.


Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga;


Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, chifukwa kuti Ine ndili ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa mbeu zako, chifukwa cha Abrahamu kapolo wanga.


Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo mu Yuda.


Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.


Yamikani Mulungu wa Kumwamba, pakuti chifundo chake nchosatha.


Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.


Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.


Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.


Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.


Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.


ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapirikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;


M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.


Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.


Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.


Kodi ndinaima nao anthu awa onse? Kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kunka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao?


Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa anthu awa m'dziko limene anawalumbirira, chifukwa chake anawapha m'chipululu.


simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.


Anthu adakwerawo kutuluka mu Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;


ndipo sanampatse cholowa chake m'menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.


Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;


Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale cholowa chao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa.


Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kuchulukitsa mbeu zake ndi kumpatsa Isaki.


Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.


Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola chipangano changa nanu ku nthawi yonse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa