Lero anthu ambiri amanena za ubwamuna kapena umbeta ponena za chiyero cha kugonana, koma kwenikweni, chiyero chiyenera kukhudza mtima, maganizo ndi moyo wathu wonse, osati ziwalo zina za thupi lokha. Ubwamuna kapena umbeta ndi mfundo yofunika kwambiri m’Mawu a Mulungu, omwe amati: “Koma chifukwa cha dama lililonse, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndi mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake” (1 Akorinto 7:2). Choncho, Akristu sayenera kugonana asanalowe m’banja.
Kwa ena, ubwamuna kapena umbeta ungakhale ndi tanthauzo loipa, pamene kwa ena ndi chinthu chamtengo wapatali choyenera kusamalira. Mulungu amafuna chiyero cha kugonana m’thupi, m’maganizo ndi m’mtima kuti tikhalemo moyo woyera pamaso pake.
Komabe ngati ukwatira, sukuchimwa ai. Ndipo ngati namwali akwatiwa, sakuchimwa ai. Komabe oloŵa m'banja adzakumana ndi zovuta m'moyo wao, ndipo pano ndingofuna kukupewetsani zovutazo.
Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino.
Ndipo akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna,
asakwatire mkazi wamasiye kapena mkazi wosudzulidwa, kapenanso mkazi wachiwerewere. Koma akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, amene sanadziŵeko mwamuna,
Anali namwali wosadziŵa mwamuna aliyense, wokongola kwambiri. Iye adatsikira kuchitsime kuja, natunga madzi mu mtsuko, nkutulukako.
Koma ngati bambo wake wa namwaliyo akana kuti mwana wakeyo asakwatiwe, munthuyo adzangolipirabe ndalama za chiwongo cha namwali.
“Munthu akanyenga namwali wosadziŵa mwamuna, yemwe sanatomeredwe, nagona naye, alipire chiwongo, ndipo amkwatire.
Koma ngati bambo wake wa namwaliyo akana kuti mwana wakeyo asakwatiwe, munthuyo adzangolipirabe ndalama za chiwongo cha namwali.
Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.
Mwina munthu agwidwa akugwirira mnamwali wosafunsidwa mbeta, amene sadamdziweko mwamuna, nachita naye chigololo momkakamiza.
Munthuyo alipe bambo wake wa mtsikanayo mtengo wofunsira mbeta, ndiye kuti masekeli asiliva makumi asanu, ndipo amtenge kuti akhale mkazi wake chifukwa choti adamkakamiza kuchita naye chigololo. Tsono pa moyo wake wonse sangathenso kumsudzula.
Mwina munthu angathe kukwatira mtsikana, namakhala naye ndithu, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna.
Tsono ayamba kumnenera zabodza zochititsa manyazi ndi kuipitsa mbiri yake ponena kuti, “Mkazi ameneyu sadaoneke ngati namwali wosadziŵa mwamuna pa nthaŵi yomukwatira.”
Zitatero, makolo a mkaziyo atenge zizindikiro zotsimikizira akuluakulu abwalo am'mudzimo kuti mwana waoyo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ndithu.
Pamenepo bambo wake wa mtsikanayo aŵauze abwalowo kuti, “Ndidalola mwana wanga wamkazi kuti akwatiwe ndi munthu uyu, koma tsopano akuti sakumufuna.
Wamnamizira momchititsa manyazi kuti ati sadali namwali wosadziŵa mwamuna pomkwatira. Koma pano tili ndi umboni wotsimikizira kuti mwana wangayu adaali namwali wangwiro ndithu. Onani, zizindikiro zake ndi izi.” Apo adzaonetse chovala cha mkaziyo kwa akuluakuluwo.
Tsono akuluakulu am'mudzimo amtenge mwamunayo ndi kumkwapula.
Pambuyo pake amlipitsenso masekeli asiliva makumi khumi, ndipo azipereke kwa bambo wa mtsikanayo. Alipe ndithu chifukwa choti adanyozetsa mnamwali Wachiisraele amene sadamdziŵeko mwamuna. Komanso adzakhalabe mkazi wake ndithu, ndipo pa moyo wake wonse sadzathanso kumsudzula.
Ndi ameneŵa amene ankadzisunga angwiro osadziipitsa ndi akazi. Ndi ameneŵa amene amatsata Mwanawankhosa uja kulikonse kumene akupita. Ndiwo amene adaomboledwa pakati pa anthu ena onse, kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa uja.
Ndidzakusamaliraninso inu anthu a ku Israele, motero mudzapezanso bwino. Mudzakondwanso poimba ting'oma tolira, ndipo mudzapita nawo limodzi anthu ovina mwachimwemwe.
Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo umboni wakuti mtsikanayo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ukusoŵa,
pamenepo apite naye pakhomo pa bambo wake. Pomwepo amuna amumzindamo amuphe pakumponya miyala. Mtsikanayo wachita chinthu chochititsa manyazi pakati pa mtundu wathu wa Israele pochita zadama m'nyumba ya bambo wake. Motero mudzachotsa choipa pakati pa inu.
Tiyese kuti mwagwira munthu mumzinda momwemo akuchita chigololo ndi mnamwali wofunsidwa mbeta, amene sadamdziŵeko mwamuna.
Muŵatenge onsewo, mupite nawo kunja kwa mzinda, ndipo muŵaphe poŵaponya miyala. Mtsikanayo aphedwe chifukwa ngakhale anali m'mudzi, sadakuwe kuti anthu adzamthandize. Mwamunayo aphedwe chifukwa wachimwa ndi mtsikana wofunsidwa mbeta ndi mnzake. Motero mudzachotsa choipa pakati panu.
Iye adamuuzanso bambo wakeyo kuti, “Mundichitire ichi chokha. Bandilekani miyezi iŵiri ndizikayendayenda ku mapiri, kuti ndizikalira pamodzi ndi anzanga kuti ndikufa ndili namwali.”
Bambo wakeyo adamuuza kuti, “Pita.” Adamulola kuti apite pa miyezi iŵiri. Choncho mtsikanayo adachoka pamodzi ndi anzake kunka ku mapiri, namakalira kuti akukafa osakwatiwa, opanda mwana.
Pakati pa anthu a ku Yabesi-Giliyadi adapeza anamwali 400 amene sadadziŵepo amuna. Amenewo adabwera nawo ku zithando ku Silo, mzinda umene uli m'dziko la Kanani.
Nthaŵi imeneyo Tamara adaavala deresi lalitali, la manja aatali, monga momwe ankavalira ana achinamwali a mfumu, amene sadadziŵeko amuna. Tsono mnyamata wa Aminoni uja adatulutsa Tamara, napiringidza chitseko mkaziyo atatuluka.
Nchifukwa chake nduna zake zidamuuza kuti, “Inu amfumu, tikupezereni namwali woti azikusungani ndi kumakusamalani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti inu amfumu muzifundidwa.”
Mwakuti tsopano, mbuyanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muŵauze munthu amene adzakhale pa mpando wanu waufumu, m'malo mwanu.
Mukapanda kutero, zidzachitike nzakuti inu mbuyanga mutatisiya, kulondola kumene kudapita makolo anu, ine pamodzi ndi mwana wanga Solomoni adzatiyesa ogalukira mfumu.”
Tsono Batesebayo akulankhula ndi mfumu, mneneri Natani adaloŵa.
Anthu adauza mfumu kuti, “Kwafika mneneri Natani.” Tsono iye atafika pamaso pa mfumu, adaŵeramitsa mutu wake pansi.
Ndipo adafunsa mfumu kuti, “Mbuyanga mfumu, kodi inu mudalengeza zoti Adoniya ndiye adzakhale mfumu ndi kukhala pampando panu?
Pakuti lero lomwe lino wakapha ng'ombe, anaang'ombe onenepa, ndi nkhosa zambiri, kuperekera nsembe. Ndipo waitana ana anu onse pamodzi ndi Yowabu mkulu wa ankhondo, ndi wansembe Abiyatara. Onsewo akudya ndi kumwa naye Adoniyayo tsopano lino, ndipo akunena kuti, ‘Adzachite kufa ndi ukalamba mfumu Adoniya.’
Koma ine mtumiki wanu, wansembe Zadoki ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso Solomoni mwana wanu, tonsefe sadatiitaneko.
Kodi zimenezi mwalamula ndinu mbuyanga mfumu? Bwanji nanga simudauze anthu anu za mwana amene adzakhale pa mpando wanu waufumu m'malo mwanu?”
Apo mfumu Davide adati, “Mundiitanire Bateseba, abwere kuno.” Bateseba adaloŵa, nakaimirira pamaso pa mfumu.
Ndipo mfumu idalumbira kuti, “Pali Chauta wamoyo, amene adapulumutsa moyo wanga ku mavuto onse,
Choncho adafunafuna namwali wokongola m'dziko lonse la Israele, ndipo adapeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.
monga momwe ndidaakulonjezera molumbira m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, kuti mwana wako Solomoni ndiye amene adzaloŵe ufumu ndi kukhala pa mpando wanga, m'malo mwanga, ndikubwerezanso zomwezo lero.”
Pomwepo Bateseba adaŵeramitsa mutu wake pansi nalambira mfumu, nati, “Mbuyanga mfumu Davide akhale ndi moyo mpaka muyaya!”
Pamenepo mfumu Davide adati, “Mundiitanire wansembe Zadoki, mneneri Natani, ndi Benaya mwana wa Yehoyada.” Onsewo adafika pamaso pa mfumu.
Tsono mfumu idaŵauza kuti, “Tengani anthu anga, ndipo mukweze Solomoni mwana wanga pa bulu wanga, mupite naye ku Gihoni.
Kumeneko wansembe Zadoki ndi mneneri Natani akamdzoze kuti akhale mfumu yolamulira Israele. Kenaka mukalize lipenga, ndi kufuula kuti, ‘Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni.’
Tsono inu muzikamtsata pambuyo pobwerera kuno, kudzakhala pa mpando wanga waufumu. Iyeyo ndiye akhale mfumu m'malo mwanga. Ndamsankha iyeyo kuti akhale wolamulira Israele ndi Yuda.”
Apo Benaya mwana wa Yehoyada adayankha kuti, “Indedi, zichitikedi motero. Chauta, Mulungu wa mbuyanga mfumu, akwaniritse zimenezi.
Monga momwe Chauta wakhalira nanu mbuyanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni, ndipo ufumu wake aukweze ndithu, ngakhale kupambana ufumu wanu, mbuyanga mfumu Davide.”
Tsono wansembe Zadoki, mneneri Natani ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso Akereti ndi Apeleti oteteza mfumu aja, adapita nakamkweza Solomoni pa bulu wa mfumu Davide, kupita naye ku Gihoni.
Kumeneko wansembe Zadoki adatenga nsupa ya mafuta ya ku hema la Chauta, nadzoza Solomoni. Pomwepo adaliza lipenga, ndipo anthu onsewo adafuula kuti, “Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni!”
Namwaliyo anali wokongola kwambiri. Tsono adakhala wosamala mfumu ndi kumaitumikira. Koma mfumuyo sidakhale naye malo amodzi namwaliyo.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako.
Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse.
Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.
Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali.
Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu.
Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa.
Nchifukwa chake Ambuye omwe adzakupatsani inu chizindikiro. Onani, namwali uja watenga pathupi ndipo adzabala mwana wamwamuna, mwanayo adzamutcha dzina lake Imanuele.
Monga mnyamata amakwatira namwali, chonchonso mmisiri wodzakumanganso adzakukwatira. Monganso mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi, chonchonso Mulungu adzasangalala nawe.
Kodi namwali amaiŵala zokongoletsera zake, kapena mkwati kuiŵala zovala zake zaukwati? Komabe anthu anga andiiŵala Ine masiku osaŵerengeka.
“Mudziikire zizindikiro, mudziikire zikwangwani. Muuyang'anitsitse mseuwo, mseu umene mudaadzera popita. Bwerera namwaliwe Israele, bwerera ku mizinda yako ija.
Asakwatire mkazi wamasiye wamba kapena mkazi wosudzulidwa. Azikwatira namwali wosadziŵa mwamuna, ŵa fuko la Israele, kapena mkazi wamasiye wa wansembe mnzake.
Inu anthu, lirani kwambiri ngati namwali wovala chiguduli. Wolira chifukwa cha imfa ya mnyamata wofuna kumkwatira.
Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanaloŵane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera.
“Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.”
“Pa nthaŵi imeneyo za Ufumu wakumwamba zidzafanafana ndi zimene zidaachitikira anamwali khumi. Iwowo adaatenga nyale zao nkumakachingamira mkwati.
Pamene ankakagula, mkwati adafika. Amene anali okonzekeratu aja adaloŵa naye pamodzi m'nyumba yaphwando; pambuyo pake adatseka chitseko.
“Kenaka m'mbuyomwalendo anamwali ena aja nawonso adabwera nati, ‘Bwana, Bwana, titsekulireni!’
Koma mkwatiyo adati, ‘Pepani, sindikukudziŵani!’ ”
Pomaliza Yesu adati, “Ndiyetu inu, muzikhala maso, poti simudziŵa tsiku lake kapena nthaŵi yake.”
Elizabeti ali ndi pathupi pa miyezi isanu ndi umodzi, Mulungu adatuma mngelo Gabriele ku mudzi wina wa ku Galileya, dzina lake Nazarete.
Adamtuma kwa namwali wina wosadziŵa mwamuna amene anali atafunsidwa mbeta ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la mfumu Davide. Namwaliyo dzina lake anali Maria.
Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziŵiri zokha,
pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya.
Inu mukuchita zimene tate wanu amachita.” Iwo adamuuza kuti, “Ife ndiye sindife ana am'chigololotu ai. Tili ndi Tate mmodzi yekha, ndiye Mulungu.”
Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.
Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe?
Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
Tsopano ndiyankhe zimene mudandifunsa m'kalata yanu. Nkwabwino kuti munthu asakwatire,
Kwa anthu am'banja lamulo langa, limenetu kwenikweni ndi lochokera kwa Ambuye, ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake.
Koma ngati amuleka, akhale wosakwatiwanso, kapena ayanjane nayenso mwamuna wakeyo. Chimodzimodzinso mwamuna asasudzule mkazi wake.
Kwa ena mau anga, osati a Ambuye ai, ndi aŵa: Ngati mkhristu ali ndi mkazi wachikunja, ndipo mkaziyo avomera kukhala naye, mwamunayo asathetse ukwatiwo.
Momwemonso ngati mkhristu wamkazi ali ndi mwamuna wachikunja, ndipo mwamunayo avomera kukhala naye, mkaziyo asathetse ukwatiwo.
Pakuti mwamuna wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mkazi wakeyo. Nayenso mkazi wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mwamuna wakeyo. Pakadapanda apo, bwenzi ana anu atakhala akunja, koma monga zilirimu, ndi ana a Mulungu.
Koma ngati wakunja uja afuna kuleka mkhristu, amuleke. Zikatero, ndiye kuti mkhristu wamwamunayo kapena wamkaziyo ali ndi ufulu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale ndi moyo wamtendere.
Kodi iwe, mkazi wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzampulumutsa mwamuna wako? Kapenanso iwe, mwamuna wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzapulumutsa mkazi wako?
Aliyense atsate moyo umene Ambuye adamkonzera, moyo umene Mulungu adamuitanira. Ndizo zimene ndimaŵalamula anthu onse amumpingo.
Ngati wina Mulungu adamuitana ali woumbalidwa, asavutike nkubisa kuumbala kwakeko. Chimodzimodzi ngati wina adamuitana ali wosaumbalidwa, asaumbalidwe.
Kuumbala si kanthu ai, kusaumbala si kanthunso. Kanthu nkutsata malamulo a Mulungu.
koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.
Kwenikweni ndikadakonda kuti anthu onse akhale ngati ine, koma Mulungu adapatsa munthu aliyense mphatso yakeyake, wina mphatso yakuti, winanso yakuti.
Kwa amene sali pa banja, ndiponso kwa azimai amasiye, mau anga ndi aŵa: Nkwabwino kuti iwo akhalebe paokha choncho ngati ineyo.
Koma ngati sangathe kudziletsa, aloŵe m'banja, pakuti nkwabwino kuloŵa m'banja kupambana kupsa ndi moto wa zilakolako.
Kunena za amene sali pa banja, ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye. Koma ndikuuzani maganizo anga, ngati munthu amene Ambuye adandichitira chifundo kuti ndikhale wokhulupirika.
Chifukwa cha masautso a nthaŵi ino, ndiyesa nkwabwino kuti munthu akhale monga momwe aliri.
Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye.
Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake.
Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake.
Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai.
Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino.
Ndiye kuti, munthu wokwatira namwali amene adamtomera, akuchita bwino, koma woleka osamkwatira, akuchita bwino koposa.
Nsanje imene ndikukuchitirani ndi yonga ya Mulungu. Pakuti ndidakupalitsani ubwenzi ndi mwamuna mmodzi yekha, ngati namwali wangwiro ndi woyera mtima, kuti mukhale akeake a Khristu.
Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo.
Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake.
Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu.
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.
Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama.
Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa.
Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni.
Usafulumire kumsanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa uchimo wao. Iwe usunge bwino kuyera mtima kwako.
Tsono munthu akadziyeretsa nkusiya zotsikazi, adzakhala ngati chiŵiya cha ntchito zolemerera. Adzakhala wopatulika ndi wofunika zedi kwa Ambuye ake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
Aŵaphunzitse kukhala a maganizo anzeru, opanda dama, osamala bwino zapabanja, ndi omvera amuna ao. Pamenepo anthu sanganyoze mau a Mulungu.
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.
Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse.
Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali.
Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.
Miriyamu, mneneri wamkazi, mlongo wa Aroni, adatenga kang'oma, ndipo akazi onse adamtsata pambuyo akuimba ting'oma, ndi kumavina.
Motero Hana adaima, ndipo adabala mwana wamwamuna namutcha dzina loti Samuele, kunena kuti, “Ndidachita kumpempha kwa Chauta.”
Tsono Elikana ndi banja lake lonse adapitanso kukatsira nsembe ya chaka ndi chaka kwa Chauta, ndi kukakwaniritsa lonjezo lake.
Koma Hana sadapite nao chifukwa adaauza mwamuna wake kuti, “Malinga mwanayu akaleka kuyamwa, ndidzapita naye kuti ndikampereke kwa Chauta, ndipo adzakhala komweko moyo wake wonse.”
Udzakhala ngati chisoti chaufumu chokongola m'manja mwa Chauta, ngati nsangamutu yaulemerero m'manja mwa Mulungu wako.
Sudzatchedwanso “Wosiyidwa,” dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.” Dzina lako latsopanolo lidzakhala “Ndikukondwera naye.” Dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa mwachimwemwe,” chifukwa choti Chauta akukondwera nawe, ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
Monga mnyamata amakwatira namwali, chonchonso mmisiri wodzakumanganso adzakukwatira. Monganso mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi, chonchonso Mulungu adzasangalala nawe.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, uli ngati munda wopiringidza, ngati munda wopiringidza, ngati kasupe wochingidwa.
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Akazi
Ine ndili ngati khoma, ndipo maŵere anga ali ngati nsanja zake. Tsono m'maso mwa wokondedwa wanga ndili ngati wodzetsa mtendere. Mwamuna
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.
Komatu pachiyambi paja, pamene Mulungu adalenga zonse, adaŵalenga anthu, wina wamwamuna wina wamkazi.
Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ndi amai, nakaphatikizana ndi mkazi wake,
ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi. Choncho tsopano salinso aŵiri, koma thupi limodzi.
Tsono zimene Mulungu wazilumikiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.
Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.
Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.
Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino.
Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje.
Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.
Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.”
Nchifukwa chake Ambuye akuti, “Tulukani pakati pao, ndi kudzipatula. Musakhudze kanthu kosayera, ndipo ndidzakulandirani.
Ndidzakhala Atate anu, inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye Mphambe.”
Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga.
Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano.
Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.
Mwayeretsa mitima yanu pakumvera choona, kotero kuti muzikondana ndi akhristu anzanu mosanyenga. Nchifukwa chake muzikondana ndi mtima wonse, mosafookera.
Pakuti mwa mwachita kubadwanso, moyo wake si wochokera m'mbeu yotha kuwonongeka, koma m'mbeu yosatha kuwonongeka. Mbeuyi ndi mau a Mulungu, mau amoyo ndi okhala mpakampaka.
Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.
Choncho, pa nthaŵi yatsala yoti mukhale pansi pano, simudzatsatanso zilakolako za anthu, koma mudzatsata kufuna kwa Mulungu.
Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.
Choncho inu okondedwa, popeza kuti mukudikira zimenezi, muzichita changu kuti Ambuye adzakupezeni muli opanda banga kapena chilema ndiponso muli pa mtendere ndi Ambuyewo.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Munthu aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi pa Khristu, amadzisandutsa woyera monga momwe Khristuyo ali woyera.
Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze.
Tikondwere ndi kusangalala, ndi kumtamanda, pakuti nthaŵi ya ukwati wa Mwanawankhosa uja yafika, mkwati wake wamkazi waukonzekera ukwatiwo.
Iye waloledwa kuvala zovala za nsalu yabafuta, yoŵala, yoombedwa bwino.” (Zovala zabafutazo zikutanthauza ntchito zabwino za anthu a Mulungu.)
Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake.
Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo.
Ngodala amene amachapa mikanjo yao, kuti aloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyo, ndiponso kuloŵa mu mzinda kudzera pa zipata zija.
Abisalomu mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola, dzina lake Tamara. Aminoni, mwana wina wa Davide, ankakonda Tamara.
Tsono Aminoni adauza Tamara kuti, “Bwera nacho chakudya chija m'chipinda muno kuti ndidzadyere m'manja mwako.” Tamara adatenga makeke amene adaaphikawo, napita nawo kwa Aminoni, mbale wake, m'chipindamo.
Koma atafika nacho chakudyacho pafupi ndi Aminoni kuti adye, Aminoni adamgwira Tamara, namuuza kuti, “Bwera ugone nane, iwe Tamara.”
Koma Tamarayo adayankha kuti, “Iyai, mlongo wanga, usandikakamize. Zimenezi sizidachitikepo nkale lonse ku Israele. Usachite zauchitsiru zotere.
Kodi ine sindidzachita manyazi poyenda pakati pa anthu? Ndipo iwe udzakhala mmodzi mwa zitsiru pakati pa Aisraele. Nchifukwa chake tsono, chonde, ndapota nawe, ulankhule ndi amfumu, poti iwowo sadzandikaniza kuti ndikwatiwe nawe.”
Koma Aminoni sadamve zimene ankanena Tamarazo. Ndipo popeza kuti anali ndi mphamvu zoposa Tamara, Aminoniyo adamkakamiza Tamarayo nagona naye.
Pambuyo pake Aminoni adayamba kudana naye kwabasi Tamarayo, kotero kuti chidani chake ndi Tamara chidakula kwambiri kuposa chikondi chimene adaamkonda nacho. Ndipo Aminoniyo adauza Tamara kuti, “Dzuka, kazipita.”
Koma Tamarayo adati, “Iyai, mlongo wanga, kundipirikitsa chotere nkulakwa koposa zimene wandichitazi.” Koma Aminoni sadafune kumva zimene ankanena Tamarazo.
Pomwepo Aminoniyo adaitana mnyamata amene ankamtumikira, namuuza kuti, “Mtulutse mkaziyu, achoke pano, ndisamuwonenso, ndipo upiringidze chitseko iyeyo akatuluka.”
Nthaŵi imeneyo Tamara adaavala deresi lalitali, la manja aatali, monga momwe ankavalira ana achinamwali a mfumu, amene sadadziŵeko amuna. Tsono mnyamata wa Aminoni uja adatulutsa Tamara, napiringidza chitseko mkaziyo atatuluka.
Ndipo Tamara adadzithira phulusa kumutu, nang'amba chovala chake chachitali chimene adaavala. Ndipo adagwirira manja kumutu, namapita akulira mokweza njira yonse.
Iye sankagona tulo chifukwa cha Tamara mlongo wake, mpaka kuchita kudwala. Tamarayo anali namwali wosadziŵa mwamuna, ndipo kunkaoneka kuti chinali chosatheka kuti Aminoniyo amchite chilichonse.
Mafuta ako odzola ngonunkhira bwino, dzina lako likundikumbutsa za mafuta otsanyukako. Nchifukwa chaketu, atsikana sangaleke kukukonda.
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, pali mphoyo ndi nswala zakuthengo, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Mkazi
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, pali mphoyo ndi nswala zakuthengo, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Mkazi
“ ‘Nditabweranso, ndidaona kuti nthaŵi yako yomanga banja idakwana. Tsono ndidakufunditsa mwinjiro wanga ndi kubisa maliseche ako. Ndidachita nawe chipangano chaukwati, ndipo udasanduka wanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
koma sadamdziŵe mpaka adabala mwana wamwamuna. Pambuyo pake Yosefe adatcha mwanayo dzina loti Yesu.
Mkwati wamkazi mwini wake ndi mkwati wamwamuna. Koma bwenzi la mkwati wamwamuna limaimirira pafupi, nkumamvetsera. Limakondwa kwakukulu likamva mau a mkwati wamwamunayo. Momwemonso ine ndakondwa kwakukulu.
Iyeyo anali ndi ana aakazi anai osakwatiwa, amene ankalalika uthenga wa Mulungu.
Koma alipo angapo pakati panu ku Sardi amene sadadetse zovala zao. Iwowo adzayenda nane pamodzi atavala zoyera, pakuti ndi oyeneradi.