M’mawu a Mulungu, amanena kuti chigololo chimachitika munthu wokwatira kapena wokwatiwa akagonana ndi munthu wosakhala mkazi kapena mwamuna wake. Ichi ndi tchimo chomwe chimatsutsana ndi kuyera kwa ukwati ndi thupi lathu, ndipo Mulungu adzachiweruza.
Masiku ano, kusakhulupirika m’banja kwafala kwambiri, ngakhale pakati pa Akhristu, ndipo izi zikuwononga mabanja ambiri. Ndikofunika kuti tonse, tisunge mitima yathu yoyera ndikukhala maso kuti tisagwere m’misampha ya dziko lapansi, lomwe limayesa kutipangitsa kuona ngati zinthu izi ndi zachibadwa.
Ndikofunikanso kuti tisalole achinyamata athu kuonera kapena kumva uthenga wokhudza kusakhulupirika, chinyengo, uhule, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, ndi zinthu zina zonyansa, chifukwa zinthu zimenezi zingawabweretsere mavuto aakulu m’miyoyo yawo ndikuwasokoneza pa cholinga cha Mulungu pa miyoyo yawo. M’malo mwake, tiwalimbikitse kuti azikonda ndi kusamalira mabanja awo amene Mulungu wawapatsa, ndipo akamayesedwa, azithamangira kwa Khristu kuti akapemphe thandizo.
Pajatu malamulo amene amati, “Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire”, ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m'lamulo ili lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi.
Tsono ndikunenetsa kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, nakwatira wina, akuchita chigololo.”
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, akumchititsa chigololo mkaziyo ngati akwatiwanso. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.
Maso ao ndi adama, osafuna kuleka kuchimwa. Amanyengerera anthu a mtima wosakhazikika. Ali ndi mtima wozoloŵera kuumirira chuma. Anthu otembereredwa!
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana,
Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.”
Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.
Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”
Yesu adaŵayankha kuti, “Mose adaakulolani kusudzula akazi anu chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pa chiyambi sizinali choncho ai.
Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu.
“Aliyense amene asudzula mkazi wake, nakwatira wina, akuchita chigololo. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.”
Malamulo ukuŵadziŵa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.”
“Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usachite chigololo.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.
Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.
“Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo onsewo aphedwe.
Akulumbira monama, kunena zabodza, kupha, kuba ndi kuchita chigololo. Machimo achita kunyanya, ndipo akungophanaphana.
Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama. Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa. Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.
Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndimadana ndi kusudzulana. Ndimadana ndi munthu wochita zankhalwe zotere kwa mkazi wake. Choncho chenjerani, musakhale osakhulupirika. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
Iye adaŵauza kuti, “Aliyense amene asudzula mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo.
Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja. Ngati ndichita zimene sindizifuna, sindinenso amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine. Motero ndimaona kuti chimene chimachitika nchakuti pamene ndifuna kuchita zabwino, zoipa zili nane pomwepo. Mtima wanga umakondwa ndi Malamulo a Mulungu, koma m'kati mwanga ndimaona lamulo lina lolimbana ndi lamulo limene mtima wanga wavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa kapolo wa lamulo la uchimo lokhala m'kati mwanga. Kalanga ine! Ndani adzandipulumutsa ku khalidwe langa lino londidzetsera imfa? Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Motero ineyo, ndi mtima wanga ndimatumikira Malamulo a Mulungu, chonsecho ndi khalidwe langa lokonda zoipa, ndimatumikira lamulo la uchimo. Nchifukwa chake ngati adzipereka kwa mwamuna wina, pamene mwamuna wake ali moyo, mkaziyo amati ngwachigololo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi uja wamasuka ku malamulo a ukwati, kotero kuti sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
Tiyese kuti munthu wakwatira mkazi, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna, chifukwa choti wampeza cholakwa. Alembe kalata yachisudzulo, ndi kumpatsa mkaziyo pamanja, namchotsa pakhomo pake.
Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo.
Kani simudziŵa kuti anthu osalungama sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu? Musadzinyenge: anthu adama, opembedza mafano, achigololo, ochimwa ndi amuna anzao,
Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
Munthu akagwidwa akuchita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, aphedwe onsewo, mwamuna ndi mkazi yemwe. Choncho mudzachotsa choipa pakati pa inu.
Zidangochitika kuti tsiku lina chakumadzulo, Davide adadzuka pabedi pake, namayenda pamwamba pa denga la nyumba yake yaufumu. Ali padengapo, adaona mkazi wina akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwabasi. tsono ngati mfumu ikapse mtima, nikakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mudapita kufupi ndi mzinda kuti mukamenye nkhondo? Kodi simunkadziŵa kuti adzakulasani kuchokera m'kati mwa linga? Kodi Abimeleki mwana wa Gideoni adamupha ndani? Kodi adamupha si mkazi, pomkunkhunizira mwalawamphero kuchokera pa linga, kotero kuti adafera ku Tebezi? Chifukwa chiyani mudakafika pafupi ndi khoma?’ Pamenepo iweyo ukanene kuti, ‘Wankhondo wanu, Uriya Muhiti uja, nayenso adaphedwa.’ ” Wamthenga uja adapita, nakafika kwa Davide, nakamuuza zonse zimene Yowabu adamuuza kuti akanene. Adauza Davide kuti, “Adani athu adaatipambana, ndipo adaatuluka kukalimbana nafe ku thengo. Koma ife tidaŵabweza mpaka ku khomo lakuchipata. Tsono anthu oponya mivi ankalasa ankhondo anu kuchokera m'linga. Ndipo ankhondo ena mwa ankhondo a inu mfumu adaphedwa. Wankhondo wanu uja, Uriya Muhiti, nayenso adaphedwa.” Apo Davide adauza wamthenga uja kuti, “Kamuuze Yowabu kuti, ‘Zimenezi usavutike nazo, poti wakufa sadziŵika. Ulimbike polimbana ndi mzindawo, ndi kuugonjetsa.’ Choncho ukamlimbitse mtima Yowabuyo.” Pamene mkazi wa Uriya adamva kuti mwamuna wake Uriya adaphedwa, adalira, kulira mwamuna wake. Mkaziyo atatha kulira malirowo, Davide adatuma munthu nakamtenga, nkubwera naye kunyumba kwa mfumu, ndipo Davide adamukwatira. Mkaziyo adambalira mwana wamwamuna. Koma zimene adachita Davidezi zidaipira Chauta. Pomwepo Davide adatuma munthu kuti akafunsitse za mkaziyo. Ndipo munthuyo adamuuza kuti, “Mkazi ujatu ndi Bateseba, mwana wa Eliyamu, mwamuna wake ndi Uriya Muhiti.” Apo Davide adatuma amithenga kuti akamtenge mkaziyo. Iwo adabwera naye kwa Davide, ndipo Davideyo adagona naye. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo atangomaliza kusamba. Pambuyo pake mkazi uja adabwerera kunyumba kwake.
“Ndidachimwira Chauta.” Natani adati, “Chauta wakukhululukirani machimo anu, simufa. Komabe, popeza kuti pochita zimenezi mwanyoza Chauta kotheratu, mwana amene akubalireniyo adzafa.”
Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake.
Paja mkazi wadama ali ndi pakamwa pokoma ngati uchi, mau ake ndi osalala koposa mafuta. Koma kotsiriza kwake ngwoŵaŵa ngati chivumulo, ngwolasa ngati lupanga lakuthwa konsekonse. Mapazi ake ndi oloza ku imfa, poyenda amaloŵera njira yakumanda.
Iwe, uzimwera m'chitsime chakochako, ndiye kuti khala wokhulupirika kwa mkazi wako. Kodi ana ako azingoti mbwee ponseponse ngati madzi ongoyenda m'miseu? Anawo akhale a iwe wekha, osatinso uŵagaŵane ndi alendo. Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse. kuti uziganiza mochenjera, ndipo pakamwa pako pazilankhula zanzeru. Mwana wanga, ungakopekerenji ndi mkazi wadama, ungamkumbatire bwanji mkazi wosakhala wako?
Zimenezi zidzakupulumutsa kwa mkazi woipa, zidzakuthandiza kuti usamvere mau osalala a mkazi wachiwerewere. Mumtima mwako usamakhumbira kukongola kwake, usakopeke nawo maso ake. Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe. Kodi munthu angathe kufukata moto, zovala zake osapsa? Kodi munthu angathe kuponda makala amoto, mapazi ake osapserera? Ndizo zimamchitikira wokaloŵerera mkazi wamwini. Aliyense wokhudza mkazi wotero adzalangidwa.
Amamkopa mnyamatayo ndi mau onyengerera, amamkakamiza ndi mau ake oshashalika. Pamenepo mnyamatayo amatsatira mkaziyo monga momwe ng'ombe imapitira kokaphedwa, kapena monga momwe mbaŵala imakodwera mu msampha, mpaka muvi kuilasa m'mimba mwake. Amakhala ngati mbalame yothamangira m'khwekhwe, osadziŵako kuti aferapo.
“Madzi akuba ndiwo amatsekemera, buledi wodya mobisa ndiye amakoma.” Koma mwamunayo sadziŵa kuti kumeneko kuli imfa, kuti alendo ake aloŵa kale m'manda ozama.
Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lakuya. Amene Chauta amamkwiyira adzagwamo.
Mkazi wadama ali ngati dzenje lakuya, mkazi wachiwerewere ali ngati chitsime chophaphatiza. Amabisalira ngati mbala yachifwamba, ndipo chifukwa cha iyeyo amuna ambiri amasanduka osakhulupirika.
M'mene amachitira mkazi akachita chigololo amatere: amati akadya nkupukuta pakamwa, namanena kuti, “Palibe chimene ndalakwa.”
Ndidapeza china choŵaŵa kupambana imfa. Chinthucho ndi mkazi amene ali ngati msampha, amene mtima wake uli ngati ukonde, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu wokondweretsa Mulungu amamthaŵa mkaziyo, koma wochimwa amalolera kukhala kapolo wake.
Taonanitu! Mzinda umene kale udaali wokhulupirika ndi wachilungamo, tsopano ukuchita zadama. Mzinda umene kale udaali ndi anthu aungwiro, tsopano wadzaza ndi anthu opha anzao.
Chauta akuti, “Munthu akasudzula mkazi wake, mkaziyo nkuchoka, nakakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamuna woyambayo angathe kumtenganso mkaziyo? Kodi atachita zotero, sindiye kuti dzikolo laipitsidwa kwambiri? Tsono iwe Israele, wachita zadama ndi abwenzi ambiri. Kodi ungabwererenso kwa Ine?
Adaona kuti Israele wosakhulupirika uja ndidamsudzula ndi kumpirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda, mbale wake, sadaope. Iyenso adakhala wosakhulupirika, adapita kukachita zadama. Dama la Israele linali lochititsa manyazi, kotero kuti potsiriza pake adaipitsa dziko. Adachita chigololo popembedza mafano amiyala ndi amitengo.
Chauta akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji pa zonsezi? Ana anu adandisiya Ine, ndipo adapembedza milungu imene siili milungu konse. Ine ndidaŵapatsa zonse zimene ankasoŵa, komabe adakonda kumachita chigololo, namapita ku nyumba za akazi adama. Aliyense ankathamangira mkazi wa mnzake, monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa.
Mumaba, mumapha, mumachita zigololo, mumalumbira zonama, mumapereka nsembe zopsereza kwa Baala, mumatsata milungu ina imene kale simunkaidziŵa.
Dziko lino ladzaza ndi anthu achigololo. Chifukwa cha temberero la Chauta m'dziko mwagwa chilala, mabusa akuchipululu auma. Amene amangothamangira zoipa, amalimbikira kuchita zosalungama.
Zoonadi makhalidwe ao ku Israele analidi oipa, ankachita chigololo ndi akazi a eniake, ankalosa zabodza m'dzina langa, Ine osaŵalamula. Ine ndikuzidziŵa, ndingathe kuzichitira umboni zimenezi,” akuterotu Chauta.
Adachita chigololo, ndipo adapha anthu. Adachita chigololo popembedza mafano ao, ndipo ana anga amene adandibalira, adaŵapereka kwa mafanowo ngati chakudya chao.
“Mudzudzule mai wanu, mumdzudzule pakuti salinso mkazi wanga, ndipo ine sindinenso mwamuna wake. Mumdzudzule kuti aleke kuchita chigololo, zibwenzi zake azichotse pachifuwa pake.
Amapereka nsembe pa mapiri, amafukiza lubani pa zitunda, patsinde pa mitengo yogudira monga thundu, mnjale ndi mkundi, chifukwa amati mithunzi yake njabwino. “Nchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere, ndipo akamwana anu akuchita zigololo. Koma sindidzaŵalanga ana anu aakazi chifukwa chochita zachiwerewere, sindidzaŵalanga akamwana anu chifukwa cha zigololo zao. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi adama akuchipembedzo. Anthu opanda nzeru chitere adzaonongeka.
Onsewo ndi osakhulupirika, udani wao ndi wonyeka ngati moto wamuuvuni, umene mphikabuledi sasonkhezera kuyambira pamene akukanyanga mtanda wa buledi mpaka utafufuma.
Musakondwere Aisraele inu! Musakhale ndi chisangalalo chonga cha mitundu ina ya anthu. Mwasiya Mulungu wanu monga amachitira mkazi wosakhulupirika. Mwadzigulitsa kwa Baala ngati mkazi wadama, kuti mukalandireko zokolola zambiri.
Mumafunsa kuti, “Chifukwa chake nchiyani?” Chifukwa chake nchakuti Chauta anali mboni ya chipangano chimene udachita ndi mkazi wako woyamba. Sudakhulupirike kwa iye, ngakhale iyeyo ndiye mnzako ndi mkazi wako potsata chipanganocho. Kodi suja Mulungu adakulenga, iwe ndi mkazi wako, kukhala mmodzi, thupi ndi mzimu womwe? Nanga pakutero Mulunguyo ankafuna chiyani? Ankafunatu ana ompembedza Iye. Motero samala moyo wako ndipo khala wokhulupirika kwa mkazi wako woyamba. Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndimadana ndi kusudzulana. Ndimadana ndi munthu wochita zankhalwe zotere kwa mkazi wake. Choncho chenjerani, musakhale osakhulupirika. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.
Iye adati, “Malamulo ake oti?” Yesu adayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama,
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana, zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”
Iye adaŵauza kuti, “Aliyense amene asudzula mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo. Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.”
Aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adabwera ndi mai amene adaamugwira akuchita chigololo, nkumukhalitsa pakati pao. Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, anthu ambiri adamkhulupirira. Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziŵa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu.” Iwo adati, “Ife ndife ana a Abrahamu, ndipo chikhalire chathu sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Nanga bwanji ukuti, ‘Mudzasanduka aufulu?’ ” Yesu adaŵayankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. Kapolo sakhala nao m'banja nthaŵi zonse, koma mwana. Tsono ngati Mwana akumasulani, mudzakhaladi mfulu. Ndikudziŵa kuti ndinu ana a Abrahamu, komabe mukufuna kundipha, chifukwa simukuvomereza mau anga m'mitima mwanu. Ine ndimalankhula zimene ndidaziwona kwa Atate anga, koma inu mumachita zimene mudamva kwa atate anu.” Iwo adati, “Ifetu atate athu ndi Abrahamu.” Yesu adaŵauza kuti, “Mukadakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zimene Abrahamuyo ankachita. Tsono adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mai uyu wagwidwa ali m'kati mochita chigololo. Koma tsopano mukufuna kundipha Ine, amene ndakuuzani zoona zimene ndidamva kwa Mulungu. Abrahamu sadachite zotere. Inu mukuchita zimene tate wanu amachita.” Iwo adamuuza kuti, “Ife ndiye sindife ana am'chigololotu ai. Tili ndi Tate mmodzi yekha, ndiye Mulungu.” Yesu adati, “Mulungu akadakhaladi Atate anu, bwenzi mutandikonda Ine, chifukwa ndidafumira kwa Mulungu, ndipo tsopano ndili kuno. Sindidabwere ndi ulamuliro wa Ine ndekha ai, koma Iyeyo adachita kundituma. Nanga chifukwa chiyani simukumvetsa zimene ndikunena? Chifukwa chake nchakuti simungakonde konse kumva mau anga. Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mukufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka. Iye uja chikhalire ngwopha anthu. Sadakhazikike m'zoona, chifukwa mwa iye mulibe zoona. Kunena bodza ndiye khalidwe lake, pakuti ngwabodza, nkukhalanso chimake cha mabodza onse. Koma Ine ndimalankhula zoona, nchifukwa chake simundikhulupirira. Kodi ndani mwa inu anganditsimikize kuti ndine wochimwa? Nanga ngati ndikunena zoona, mukulekeranji kundikhulupirira? Munthu wochokera kwa Mulungu amatchera khutu ku mau a Mulungu. Koma inu simuchokera kwa Mulungu ai, nchifukwa chake simutchera khutu.” Ayuda aja pomuyankha Yesu, adati, “Kodi ife sitikunena zoona kuti Iwe ndiwe Msamariya, ndipo kuti ndiwe wogwidwa ndi mizimu yoipa?” Yesu adati, “Ine sindidagwidwe ndi mizimu yoipa. Ndimalemekeza Atate anga, koma inu mumandipeputsa. Paja m'buku la Malamulo Mose adatilamula kuti munthu wotere tizipha pakumponya miyala. Nanga Inuyo mukuti chiyani pamenepa?”
Kenaka Yesu adaŵeramuka namufunsa kuti, “Kodi mai, ali kuti anthu aja? Kodi palibe ndi mmodzi yemwe amene wakuzengani mlandu?” Maiyo adati, “Inde Ambuye, palibe.” Tsono Yesu adamuuza kuti, “Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.”]
Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi,
Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.
Kwa anthu am'banja lamulo langa, limenetu kwenikweni ndi lochokera kwa Ambuye, ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake. Koma ngati amuleka, akhale wosakwatiwanso, kapena ayanjane nayenso mwamuna wakeyo. Chimodzimodzinso mwamuna asasudzule mkazi wake.
Ndikuwopa kuti ndikadzabweranso kwanuko, mwina Mulungu wanga nkudzandinyazitsa pamaso panu, ineyo nkudzalira misozi chifukwa cha ambiri amene adachimwa kale, ndipo sadalape zonyansa zao, dama lao, ndi mayendedwe ao oipa.
Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.
Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza fano) sadzaloŵa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano. Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera.
Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa.
Nchifukwa chake nkadakonda kuti azimai amasiye a zaka zochepera azikwatiwanso, abale ana, ndipo azisamala bwino panyumba pao, kuti adani athu asapeze mpata wotisinjirira. Paja alipo kale azimai amasiye ena amene adapatukapo nkumatsata Satana.
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.
Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.
Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Koma pali zinthu zingapo zoti ndikudzudzulireni. Kwanuko muli ndi anthu ena otsata chiphunzitso cha Balamu mneneri wonama uja. Iye uja adaaphunzitsa mfumu Balaki kukopa Aisraele kuti azidya za nsembe zoperekedwa kwa mafano, ndi kumachita chigololo.
Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mumamlekerera mkazi uja Yezebele, amene amadzitcha mneneri. Iye uja amanyenga atumiki anga nkumaŵaphunzitsa kuti azichita dama ndi kumadya zansembe zoperekedwa kwa mafano. Ndidampatsa nthaŵi kuti atembenuke mtima, koma safuna kutembenuka ndi kuleka kusakhulupirika kwake. Tsono ndidzamgwetsa m'matenda, ndipo ochita naye dama lakelo, ndidzaŵagwetsa m'masautso aakulu, akapanda kutembenuka mtima ndi kuleka zoipa zonse zimene ankachita naye.
Momwe chimaonekera chipini chagolide chikakhala pa mpuno wa nkhumba, ndi momwenso kumakhalira kukongola kwa mkazi wam'kamwa.
Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe.
Pamenepo mnyamatayo amatsatira mkaziyo monga momwe ng'ombe imapitira kokaphedwa, kapena monga momwe mbaŵala imakodwera mu msampha,
Ndaona zonyansa zanu, zigololo zanu, kutchetcherera kwanu, ndi ziwerewere zanu zochitika pa mapiri, kuthengo. Tsoka kwa inu a ku Yerusalemu! Mudzakhala osayeretsedwabe pa zachipembedzo mpaka liti?”
Senderani kuno, inu anthu ochita zoipa, pakuti muli ngati zidzukulu zam'chigololo, zochokera m'zadama. Kodi inu mukuseŵera ndi yani? Kodi mukunena yani? Mukunyoza yani? Kodi ochimwa sindinu? Onyenga sindinu? Mumapembedza mafano pa mitengo ya thundu, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse. Mumapereka ana anu ngati nsembe m'zigwa, m'ming'alu yam'mathanthwe.
“Tsono Ine ndidati, ‘Mkazi ameneyu ndi wotheratu ndi chigololo. Koma onani, anthu akutsatabe zadama zake zomwezo. Choncho adapita kwa iye monga m'mene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Ndimo adapitira kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama.
Mafano ake onse ndidzaŵaphwanyaphwanya, ndipo mitulo yake yonse idzatenthedwa m'moto. Zithunzi zonse za milungu yake ndidzaziwononga. Mphatso zake adazilandira kuchokera ku malipiro a akazi adama, choncho enanso adzazigwiritsa ntchito ngati malipiro a akazi adama.”
Kubzolera pamenepo adayambitsa akachisi opembedzerako mafano ku dziko lamapiri la ku Yuda, ndipo adatsogolera anthu a ku Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, nasokeza anthu a ku Yuda.
Munthu wachigololo amadikira chisisira, namanena kuti, ‘Palibe woti angandiwone,’ ndipo amadzizimbaitsa nkhope.
Zitatha zaka makumi asanu ndi aŵiri, Chauta adzachitapo kanthu pa Tiro. Mzindawo udzabwerera ku ganyu wake wakale uja. Ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu a dziko lonse lapansi.
Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo, ndipo amaombeza ndi ndodo yao. Mzimu wonyansa waasokeretsa, motero posiya Mulungu wao, akhala osakhulupirika.
Koma Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ndi oipa ndi osakhulupirika, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija.
Mbiri yawanda ponseponse yonena kuti pakati panu pali dama. Ndipo damalo ndi la mtundu wakuti ndi anthu akunja omwe sachita. Ndamva ndithu kuti munthu wina akukhala ndi mkazi wa bambo wake.
Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake. Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.
Ndithu, monga momwe mkazi wosakhulupirika amasiyira mwamuna wake, iwenso Israele wakhala wosakhulupirika kwa Ine,” akuterotu Chauta.
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Pitanso, ukakonde mkazi wachigololo amene ali ndi chibwenzi chake. Umkonde monga momwe Ine Chauta ndimakondera Israele, ngakhale iyeyo amapembedza milungu ina, ndipo amakonda kuitsirira nsembe za mphesa zabwino zoumika.”
Ambuye Chauta akunena kuti, “Mtima wako ndi wofooka kwambiri chifukwa udachita zonsezo monga ngati mkazi wadama wopanda manyazi.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.