Ndikufuna tikambirane nkhani yofunika kwambiri, nkhani ya chigololo. Mwina ukudziwa kuti chigololo ndi kugonana kwa anthu osakwatirana. Baibulo limatiuza momveka bwino mu 1 Akorinto 6:18 kuti, "Thawani dama. Machimo ena onse amene munthu angachite ali kunja kwa thupi lake, koma wochita dama amachimwira thupi lake lomwe."
Chigololo ndi tchimo, ndipo sichikondweretsa Mulungu. Iye akufuna kuti uzitsatira malamulo ake kuti ukhale ndi moyo wabwino, mwakuthupi komanso mwauzimu. Ugonde wosaloleka ukhoza kubweretsa mavuto aakulu, kuphatikizapo imfa.
Ngati wakhala ukuchita tchimoli, dziwa kuti sudachedwa. Ukhoza kusiya lero lomwe ndi kupempha Yesu kuti akukhululukire. Mulungu ndi wachifundo ndipo amakhululukira onse olapa machimo awo.
Monga Akhristu, tiyenera kudziwa kuti Mulungu analenga kugonana kuti anthu abereke ana komanso kuti mwamuna ndi mkazi wake azisangalalana. Sikuti kugonana ndi kwakuthupi kokha, komanso ndi kwauzimu ndi kwamalingaliro pakati pa awiri okwatirana.
Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi,
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.
Mbiri yawanda ponseponse yonena kuti pakati panu pali dama. Ndipo damalo ndi la mtundu wakuti ndi anthu akunja omwe sachita. Ndamva ndithu kuti munthu wina akukhala ndi mkazi wa bambo wake.
Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza fano) sadzaloŵa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano. Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera.
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana, zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa.
Nchifukwa chake Mulungu adaŵasiya kuti azingochita zonyansa zimene mitima yao inkalakalaka, mpaka kunyazitsa matupi ao.
Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.
Tsono ndikunenetsa kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, nakwatira wina, akuchita chigololo.”
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, akumchititsa chigololo mkaziyo ngati akwatiwanso. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.
Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.
Kani simudziŵa kuti anthu osalungama sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu? Musadzinyenge: anthu adama, opembedza mafano, achigololo, ochimwa ndi amuna anzao,
Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama. Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa. Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,
Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.
Munthu akagona ndi munthu wamwamuna mnzake ngati mkazi, onsewo achita chinthu chonyansa, ndipo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo.
Ndikuwopa kuti ndikadzabweranso kwanuko, mwina Mulungu wanga nkudzandinyazitsa pamaso panu, ineyo nkudzalira misozi chifukwa cha ambiri amene adachimwa kale, ndipo sadalape zonyansa zao, dama lao, ndi mayendedwe ao oipa.
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
“Munthu wina aliyense mwa inu asagone ndi wachibale wake. Ine ndine Chauta. Usachititse manyazi bambo wako pakugona ndi mai wako. Ameneyo ndi mai wako, usamchititse manyazi.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.
Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo.
Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.
“Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo onsewo aphedwe.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake. Aliyense angokhala monga momwe analiri pamene Mulungu adamuitana. Kodi unali kapolo pamene Mulungu adakuitana? Usavutike nazo. Komanso ngati upeza mwai woti ulandire ufulu, uugwiritse ntchito mwaiwo. Pakuti munthu amene anali kapolo pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi mfulu ya Ambuye. Momwemonso amene anali mfulu pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi kapolo wa Khristu. Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono musasanduke akapolo a anthu. Abale, aliyense angokhala pamaso pa Mulungu monga momwe analiri pamene Mulunguyo adamuitana. Kunena za amene sali pa banja, ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye. Koma ndikuuzani maganizo anga, ngati munthu amene Ambuye adandichitira chifundo kuti ndikhale wokhulupirika. Chifukwa cha masautso a nthaŵi ino, ndiyesa nkwabwino kuti munthu akhale monga momwe aliri. Kodi ndiwe wapabanja? Usayese kuthetsa banja lako. Kodi ndiwe wopanda banja? Usayese kupeza banja. Komabe ngati ukwatira, sukuchimwa ai. Ndipo ngati namwali akwatiwa, sakuchimwa ai. Komabe oloŵa m'banja adzakumana ndi zovuta m'moyo wao, ndipo pano ndingofuna kukupewetsani zovutazo. Chimene ndikukuuzani, abale, nchakuti nthaŵi yachepa. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale monga ngati sadakwatire. Mwamuna azipereka kwa mkazi wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mkazi wake, momwemonso mkazi azipereka kwa mwamuna wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mwamuna wake. Amene akulira, akhale monga ngati sakulira, amene akukondwa, akhale monga ngati sakukondwa, amene akugula zinthu, akhale monga ngati sali nazo zinthuzo. Ndipo amene akugwiritsa ntchito zinthu zapansipano, zisaŵagwire mtima zinthuzo. Pakuti dziko lino lapansi, monga liliri tsopanomu, likupita. Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye. Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake. Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake. Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati kuti ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye. Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai. Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino. Ndiye kuti, munthu wokwatira namwali amene adamtomera, akuchita bwino, koma woleka osamkwatira, akuchita bwino koposa. Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu. Mkazi thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mwamuna wake yemwe. Momwemonso mwamuna thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mkazi wake yemwe. Koma m'mene ndikuganizira ine, adzakhala wokondwa koposa ngati akhala wosakwatiwanso. Ndipo ndikuyesa inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu. Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.
Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo umboni wakuti mtsikanayo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ukusoŵa, pamenepo apite naye pakhomo pa bambo wake. Pomwepo amuna amumzindamo amuphe pakumponya miyala. Mtsikanayo wachita chinthu chochititsa manyazi pakati pa mtundu wathu wa Israele pochita zadama m'nyumba ya bambo wake. Motero mudzachotsa choipa pakati pa inu.
Munthu akagwidwa akuchita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, aphedwe onsewo, mwamuna ndi mkazi yemwe. Choncho mudzachotsa choipa pakati pa inu.
Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake.
Paja mkazi wadama ali ndi pakamwa pokoma ngati uchi, mau ake ndi osalala koposa mafuta. Koma kotsiriza kwake ngwoŵaŵa ngati chivumulo, ngwolasa ngati lupanga lakuthwa konsekonse. Mapazi ake ndi oloza ku imfa, poyenda amaloŵera njira yakumanda.
Mwana wanga, ungakopekerenji ndi mkazi wadama, ungamkumbatire bwanji mkazi wosakhala wako? Mayendedwe a munthu Chauta amaŵaona bwino lomwe, njira zake zonse amazipenyetsetsa. Zoipa za munthu woipa zimamtchera msampha iyeyo, ntchito za machimo ake zimamkwidzinga. Amafa chifukwa chosoŵa mwambo, amatayika chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.
Zimenezi zidzakupulumutsa kwa mkazi woipa, zidzakuthandiza kuti usamvere mau osalala a mkazi wachiwerewere. Mumtima mwako usamakhumbira kukongola kwake, usakopeke nawo maso ake. Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe. Kodi munthu angathe kufukata moto, zovala zake osapsa? Kodi munthu angathe kuponda makala amoto, mapazi ake osapserera? Ndizo zimamchitikira wokaloŵerera mkazi wamwini. Aliyense wokhudza mkazi wotero adzalangidwa.
Zikuteteze kwa mkazi wadama, ku mau oshashalika a mkazi wosakhala wako. Tsiku lina pa windo la nyumba yanga, ndidasuzumira pa made, ndipo pakati pa anthu opusa, pakati pa achinyamata, ndidaona wachinyamata mmodzi wopanda nzeru.
Amamkopa mnyamatayo ndi mau onyengerera, amamkakamiza ndi mau ake oshashalika. Pamenepo mnyamatayo amatsatira mkaziyo monga momwe ng'ombe imapitira kokaphedwa, kapena monga momwe mbaŵala imakodwera mu msampha, mpaka muvi kuilasa m'mimba mwake. Amakhala ngati mbalame yothamangira m'khwekhwe, osadziŵako kuti aferapo.
“Madzi akuba ndiwo amatsekemera, buledi wodya mobisa ndiye amakoma.” Koma mwamunayo sadziŵa kuti kumeneko kuli imfa, kuti alendo ake aloŵa kale m'manda ozama.
Mkazi wadama ali ngati dzenje lakuya, mkazi wachiwerewere ali ngati chitsime chophaphatiza. Amabisalira ngati mbala yachifwamba, ndipo chifukwa cha iyeyo amuna ambiri amasanduka osakhulupirika.
Ndidapeza china choŵaŵa kupambana imfa. Chinthucho ndi mkazi amene ali ngati msampha, amene mtima wake uli ngati ukonde, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu wokondweretsa Mulungu amamthaŵa mkaziyo, koma wochimwa amalolera kukhala kapolo wake.
“Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usachite chigololo.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.
Iye adati, “Malamulo ake oti?” Yesu adayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama,
Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana, zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”
Iye adaŵauza kuti, “Aliyense amene asudzula mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo. Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.”
“Aliyense amene asudzula mkazi wake, nakwatira wina, akuchita chigololo. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.”
Aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adabwera ndi mai amene adaamugwira akuchita chigololo, nkumukhalitsa pakati pao. Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, anthu ambiri adamkhulupirira. Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziŵa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu.” Iwo adati, “Ife ndife ana a Abrahamu, ndipo chikhalire chathu sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Nanga bwanji ukuti, ‘Mudzasanduka aufulu?’ ” Yesu adaŵayankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. Kapolo sakhala nao m'banja nthaŵi zonse, koma mwana. Tsono ngati Mwana akumasulani, mudzakhaladi mfulu. Ndikudziŵa kuti ndinu ana a Abrahamu, komabe mukufuna kundipha, chifukwa simukuvomereza mau anga m'mitima mwanu. Ine ndimalankhula zimene ndidaziwona kwa Atate anga, koma inu mumachita zimene mudamva kwa atate anu.” Iwo adati, “Ifetu atate athu ndi Abrahamu.” Yesu adaŵauza kuti, “Mukadakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zimene Abrahamuyo ankachita. Tsono adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mai uyu wagwidwa ali m'kati mochita chigololo. Koma tsopano mukufuna kundipha Ine, amene ndakuuzani zoona zimene ndidamva kwa Mulungu. Abrahamu sadachite zotere. Inu mukuchita zimene tate wanu amachita.” Iwo adamuuza kuti, “Ife ndiye sindife ana am'chigololotu ai. Tili ndi Tate mmodzi yekha, ndiye Mulungu.” Yesu adati, “Mulungu akadakhaladi Atate anu, bwenzi mutandikonda Ine, chifukwa ndidafumira kwa Mulungu, ndipo tsopano ndili kuno. Sindidabwere ndi ulamuliro wa Ine ndekha ai, koma Iyeyo adachita kundituma. Nanga chifukwa chiyani simukumvetsa zimene ndikunena? Chifukwa chake nchakuti simungakonde konse kumva mau anga. Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mukufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka. Iye uja chikhalire ngwopha anthu. Sadakhazikike m'zoona, chifukwa mwa iye mulibe zoona. Kunena bodza ndiye khalidwe lake, pakuti ngwabodza, nkukhalanso chimake cha mabodza onse. Koma Ine ndimalankhula zoona, nchifukwa chake simundikhulupirira. Kodi ndani mwa inu anganditsimikize kuti ndine wochimwa? Nanga ngati ndikunena zoona, mukulekeranji kundikhulupirira? Munthu wochokera kwa Mulungu amatchera khutu ku mau a Mulungu. Koma inu simuchokera kwa Mulungu ai, nchifukwa chake simutchera khutu.” Ayuda aja pomuyankha Yesu, adati, “Kodi ife sitikunena zoona kuti Iwe ndiwe Msamariya, ndipo kuti ndiwe wogwidwa ndi mizimu yoipa?” Yesu adati, “Ine sindidagwidwe ndi mizimu yoipa. Ndimalemekeza Atate anga, koma inu mumandipeputsa. Paja m'buku la Malamulo Mose adatilamula kuti munthu wotere tizipha pakumponya miyala. Nanga Inuyo mukuti chiyani pamenepa?”
Koma tiŵalembere kalata kuŵauza kuti asamadye zimene zili zosayera chifukwa zidaperekedwa kwa mafano. Alewe dama, ndipo asamadye nyama zochita kupotola, alewenso magazi.
musamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe kwa mafano, musamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso musachite dama. Mukalewa zimenezi, mudzachita bwino. Tsalani bwino.”
Koma kunena za anthu a mitundu ina amene adasanduka okhulupirira, ife taŵalembera kalata yoŵauza zimene tidavomerezana: kuti asamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe ku mafano, asamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso asamachite dama.”
Chifukwa cha zimenezi Mulungu adaŵasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe adaleka machitidwe achibadwa pa zachikwati, namatsata machitidwe ena otsutsana ndi achibadwawo. Chimodzimodzinso amuna, adaleka machitidwe achibadwa osirira akazi, nkumakhumbana amuna okhaokha. Ankachitana zamanyazi, motero adadziitanira chilango choyenera molingana ndi zochita zao zopotokazo.
Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja. Ngati ndichita zimene sindizifuna, sindinenso amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine. Motero ndimaona kuti chimene chimachitika nchakuti pamene ndifuna kuchita zabwino, zoipa zili nane pomwepo. Mtima wanga umakondwa ndi Malamulo a Mulungu, koma m'kati mwanga ndimaona lamulo lina lolimbana ndi lamulo limene mtima wanga wavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa kapolo wa lamulo la uchimo lokhala m'kati mwanga. Kalanga ine! Ndani adzandipulumutsa ku khalidwe langa lino londidzetsera imfa? Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Motero ineyo, ndi mtima wanga ndimatumikira Malamulo a Mulungu, chonsecho ndi khalidwe langa lokonda zoipa, ndimatumikira lamulo la uchimo. Nchifukwa chake ngati adzipereka kwa mwamuna wina, pamene mwamuna wake ali moyo, mkaziyo amati ngwachigololo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi uja wamasuka ku malamulo a ukwati, kotero kuti sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.
Koma ngati sangathe kudziletsa, aloŵe m'banja, pakuti nkwabwino kuloŵa m'banja kupambana kupsa ndi moto wa zilakolako.
Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu.
Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima? Kodi Khristu nkuvomerezana ndi Satana? Kodi mkhristu ndi mkunja angagaŵanenso chiyani pamodzi?
Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa.
Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni.
Nchifukwa chake nkadakonda kuti azimai amasiye a zaka zochepera azikwatiwanso, abale ana, ndipo azisamala bwino panyumba pao, kuti adani athu asapeze mpata wotisinjirira. Paja alipo kale azimai amasiye ena amene adapatukapo nkumatsata Satana.
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.
Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.
Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.
Ambiri adzatsata mkhalidwe wodzilekerera ndipo anthu adzanyoza njira ya choona chifukwa cha iwowo.
Makamaka adzalanga anthu amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi namanyoza ulamuliro. Aphunzitsi onyenga ndi odzikuza, osasamala munthu, saopa kuchita chipongwe aulemerero a Kumwamba.
Iwowotu amalankhula mau odzitama auchitsiru, ndipo ndi zilakolako zonyansa zathupi amanyengerera anthu amene angopulumuka chatsopano pakati pa anzao oipa. Amaŵalonjeza ufulu, chonsecho eniakewo ndi akapolo a chivunde. Pajatu munthu amasanduka kapolo wa chimene chamugonjetsa.
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Paja anthu ena osasamala za Mulungu adaloŵa mobisika pakati panu. Iwo amapotoza kukoma mtima kwa Mulungu, ndi kukuyesa ufulu wochitira zonyansa. Amakana Yesu Khristu, amene Iye yekha ndiye Mbuye wathu ndi Mfumu yathu. Zakuti anthu ameneŵa adzalangidwa zidalembedwa kale lomwe.
Mukumbukirenso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu ake m'menemonso ankangochita dama, namachitanso zonyansa zotsutsana ndi umunthu. Mulungu adaaŵaika ngati chitsanzo pakuŵalanga ndi moto wosatha.
Koma pali zinthu zingapo zoti ndikudzudzulireni. Kwanuko muli ndi anthu ena otsata chiphunzitso cha Balamu mneneri wonama uja. Iye uja adaaphunzitsa mfumu Balaki kukopa Aisraele kuti azidya za nsembe zoperekedwa kwa mafano, ndi kumachita chigololo.
Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mumamlekerera mkazi uja Yezebele, amene amadzitcha mneneri. Iye uja amanyenga atumiki anga nkumaŵaphunzitsa kuti azichita dama ndi kumadya zansembe zoperekedwa kwa mafano. Ndidampatsa nthaŵi kuti atembenuke mtima, koma safuna kutembenuka ndi kuleka kusakhulupirika kwake. Tsono ndidzamgwetsa m'matenda, ndipo ochita naye dama lakelo, ndidzaŵagwetsa m'masautso aakulu, akapanda kutembenuka mtima ndi kuleka zoipa zonse zimene ankachita naye.
Ndi ameneŵa amene ankadzisunga angwiro osadziipitsa ndi akazi. Ndi ameneŵa amene amatsata Mwanawankhosa uja kulikonse kumene akupita. Ndiwo amene adaomboledwa pakati pa anthu ena onse, kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa uja.
Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno ndikakuwonetse m'mene akukaweruzidwira mkazi wadama wotchuka uja, amene akukhala pambali pa madzi ambiri. Ikufaniziranso mafumu asanu ndi aŵiri. Mwa iwo, asanu adagwa, imodzi ikulamulirabe, imodzi inayo siinafikebe. Koma ikadzafika, idzayenera kungokhala kanthaŵi. Tsono chilombo chija chimene kale chidaali chamoyo, koma tsopano si chamoyonso, chikufanizira mfumu yachisanu ndi chitatu ichocho, komabe ndi imodzi mwa mafumu asanu ndi aŵiri aja, ndipo ikupita kukaonongedwa. “Nyanga khumi zimene unaona, zikufanizira mafumu khumi amene asanayambebe kulamulira. Koma adzalandira mphamvu zolamulira ngati mafumu pa ora limodzi, pamodzi ndi chilombo chija. Mafumu khumi ameneŵa, cholinga chao ndi chimodzi, ndipo amapereka mphamvu zao ndi ulamuliro wao m'manja mwa chilombo chija. Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.” Mngelo uja adandiwuzanso kuti, “Madzi unaona aja amene mkazi wadama uja wakhalapo, akufanizira mitundu ya anthu, makamu a anthu, mafuko a anthu ndiponso anthu a zilankhulo zosiyanasiyana. Tsono nyanga khumi unaona zija, pamodzi ndi chilombo chija, zidzadana naye mkazi wadamayo. Zidzamlanda zake zonse ndi kumsiya maliseche. Zidzadyako mnofu wake, kenaka nkumuponya pa moto kuti apserere. Zidzaterodi, pakuti Mulungu adazipatsa mtima wofuna kuchita zimene Iye adazikonzeratu. Zimenezi nzakuti zidzagwirizana pakupereka mphamvu zake zolamulira kwa chilombo chija, mpaka zitachitika zonse zimene Mulungu adanena. “Mkazi unaona uja akufanizira mzinda waukulu uja wolamulira mafumu onse a pa dziko lapansi.” Mafumu a pa dziko lapansi ankachita naye chigololo, ndipo anthu okhala pa dziko lapansi ankaledzera naye vinyo wa dama lakelo.”
Pamphumi pake padaalembedwa dzina lachinsinsi lakuti, “Babiloni wotchuka uja, manthu wa achiwerewere onse, ndi a zonyansa zonse za dziko lapansi.”
Pakuti adamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zadama. Mafumu a pa dziko lonse lapansi adachita naye chigololo, ndipo anthu amalonda a pa dziko lonse lapansi ankalemererapo pa zolakalaka zake zodziwunjikira chuma.”
Mafumu a pa dziko lapansi amene ankachita naye chigololo ndi kudzisangalatsa naye, adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa.
Iwe, uzimwera m'chitsime chakochako, ndiye kuti khala wokhulupirika kwa mkazi wako. Kodi ana ako azingoti mbwee ponseponse ngati madzi ongoyenda m'miseu? Anawo akhale a iwe wekha, osatinso uŵagaŵane ndi alendo. Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse.
Momwe chimaonekera chipini chagolide chikakhala pa mpuno wa nkhumba, ndi momwenso kumakhalira kukongola kwa mkazi wam'kamwa.
Dama la Israele linali lochititsa manyazi, kotero kuti potsiriza pake adaipitsa dziko. Adachita chigololo popembedza mafano amiyala ndi amitengo.
Ndaona zonyansa zanu, zigololo zanu, kutchetcherera kwanu, ndi ziwerewere zanu zochitika pa mapiri, kuthengo. Tsoka kwa inu a ku Yerusalemu! Mudzakhala osayeretsedwabe pa zachipembedzo mpaka liti?”
Senderani kuno, inu anthu ochita zoipa, pakuti muli ngati zidzukulu zam'chigololo, zochokera m'zadama.
Azidzadya koma sadzakhuta. Azidzachita zachiwerewere, koma sadzachulukana, poti adasiya Chauta, kuti adzipereke ku zachiwerewere.” Chauta akuti, “Vinyo, kaya ndi wakale kaya ndi watsopano, amaononga nzeru.
Amapereka nsembe pa mapiri, amafukiza lubani pa zitunda, patsinde pa mitengo yogudira monga thundu, mnjale ndi mkundi, chifukwa amati mithunzi yake njabwino. “Nchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere, ndipo akamwana anu akuchita zigololo. Koma sindidzaŵalanga ana anu aakazi chifukwa chochita zachiwerewere, sindidzaŵalanga akamwana anu chifukwa cha zigololo zao. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi adama akuchipembedzo. Anthu opanda nzeru chitere adzaonongeka.
Udachita zigololo ndi Aejipito adama oyandikana nawe, ndipo udandikwiyitsa chifukwa udachulukitsa zigololo zako.
Koma ankachitabe zadama zake osalekeza, namakumbukira zadama zimene ankachita pamene anali hule ku Ejipito pa ubwana wake. “Iwe mwana wa munthu, panali akazi aŵiri, ana a mimba imodzi. Ankalakalaka abwenzi ake amene ziwalo zao zinali zazikulu ngati za bulu, amene kutentha kwao kunali ngati kwa akavalo. Motero iwe Oholiba udafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Ejipito ukadali namwali, kumene ankakusisita pa chifuwa, nkumakugwira maŵere ako osagwa aja.
Motero ndidzaletsa zonyansa zako ndi zigololo zako zimene wakhala ukuchita kuyambira nthaŵi imene unali ku Ejipito. Choncho sudzalakalakanso za ku Ejipito kapena kuzikumbukira.
“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake. Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.
Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye. Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.