Abrahamu adakhulupirira, ndipo Mulungu adamdalitsa. Motero pamodzi ndi Abrahamuyo Mulungu amadalitsanso onse okhulupirira.
Pakuti ngakhale sindili nanu m'thupi, komabe mumtimamu ndili nanu pamodzi. Ndipo ndakondwa kuwona kuti mukulongosola bwino zonse, ndi kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu nchosagwedezeka konse.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Mose adachoka ku Ejipito, osaopa ukali wa mfumu, popeza kuti ankapirira ngati munthu woona Mulungu wosaonekayu.
Apo Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere.”
Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Paja Malembo akuti, ‘Munthu wokhulupirira Ine, mtima wake udzakhala ngati gwelo la mitsinje ya madzi opatsa moyo.’ ”
Koma Malembo akunenetsa kuti zinthu zonse zili mu ulamuliro wa uchimo, kuti pakukhulupirira Yesu Khristu, anthu okhulupirira alandiredi zimene Mulungu adalonjeza.
Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Paja timasanduka anzake a Khristu, malinga tikasunga kwenikweni mpaka potsiriza kulimba mtima kumene tinali nako poyamba.
Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.
Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.
Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Paja Malembo akuti bwanji? Akuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo pakukhulupirirapo, Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu.
Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu.
Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya.
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo.
Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko.
Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.
Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Abele adapereka kwa Mulungu nsembe yopambana ya Kaini, navomerezedwa kuti ngwolungama, chifukwa Mulungu mwiniwake adaamchitira umboni pakulandira zopereka zake. Mwakuti ngakhale iye adafa, koma chifukwa cha chikhulupiriro chakecho, akulankhulabe mpaka pano.
Pajatu palibe maziko enanso amene wina aliyense angathe kukhazika osiyana ndi maziko amene alipo kale. Mazikowo ndi Yesu Khristu.
Pompo Yesu adatambalitsa dzanja nkumugwira nati, “Iwe wa chikhulupiriro chochepawe, unakayikiranji?”
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu, pamene Mulungu adamuyesa, adapereka Isaki ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu adaampatsa lonjezo, adakhala wokonzeka kupereka ngati nsembe mwana wake mmodzi yekhayo.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu.
uli ndi chikhulupiriro ndiponso ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa. Ena sadamvere pamene mtima wao unkaŵatsutsa, motero chikhulupiriro chao chidaonongeka.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Mose atakula adakana kutchedwa mdzukulu wa Farao, mfumu ya ku Ejipito.
Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza.
Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”
Chimene Mulungu amalamula nchakuti tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira.
Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu.
Pokhala ndi chikhulupiriro anthu ameneŵa adagonjetsa maufumu, adakhazikitsa chilungamo, ndipo adalandira zimene Mulungu adaaŵalonjeza. Ena adapuya mikango pakamwa,
Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.
Koma Yesu sadasamale zimene anthuwo ankanena. Adauza mkulu uja kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupirira.”
Mulungu adati, “Zidzukulu zako zidzachulukadi.” Ndipo ngakhale zimenezi zinali zosayembekezeka konse, Abrahamu adalimbikirabe kukhulupirira kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.
Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”
Nchifukwa chake lonjezolo maziko ake ndi chikhulupiriro, kuti likhale mphatso yaulere ya Mulungu, ndipo patsimikizike kuti lonjezolo adzalilandiradi anthu ofumira kwa Abrahamu. Osati okhawo amene amasunga Malamulo a Mose ai, komanso onse okhala ndi chikhulupiriro chonga cha Abrahamu. Iye ndiyedi kholo la ife tonse.
Tiyenera kuthokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale. Nkoyeneradi kutero, chifukwa chikhulupiriro chanu chikunka chikukulirakulira kwambiri pamodzi ndi kukondana kwanu pakati pa inu nonse.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza.
Timathokoza chifukwa tamva kuti mumakhulupirira Khristu Yesu, ndiponso kuti mumakonda anthu onse a Mulungu.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Enoki adatengedwa kupita Kumwamba, osafa konse. Sadapezekenso, popeza kuti Mulungu adamtenga. Malembo amamchitira umboni kuti asanatengedwe, anali wokondweretsa Mulungu.
Tsono ngati Khristu sadauke, kulalika kwathu nkwachabe, ndipo chikhulupiriro chanu nchachabenso.
Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka.
Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.
Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu.
Yesu adati, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.”
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Komatu nchodziŵikiratu kuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Paja Malembo akuti, “Munthu amene ali wolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, adzakhaladi ndi moyo.”
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo.
Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”
Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.
Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro.
Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka.
Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.
Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo.
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu.
Paja monga momwe thupi lopanda mzimu limakhala lakufa, moteronso chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchakufa.
Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.
Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”
Wolungama wanga adzakhala ndi moyo pakukhulupirira. Koma akamachita mantha nkubwerera m'mbuyo, Ine sindikondwera naye.”
Mlandireni bwino munthu amene chikhulupiriro chake nchofooka, koma osati kuti mutsutsane naye pa maganizo ake.
Paja ifenso tidaumva Uthenga Wabwino, monga iwo aja. Koma iwowo sadapindule nawo mau olalikidwawo, popeza kuti adangoŵamva, koma osaŵakhulupirira.
Koma kunena za ife, chifukwa cha kulandira Mzimu Woyera ndiponso pakukhulupirira, tikuyembekeza kuti Mulungu adzatiwona kuti ndife olungama pamaso pake.
Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu.
Adakhulupirira ndithu kuti Mulungu angathe kuchita zimene adalonjeza.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu adamvera pamene Mulungu adamuitana kuti apite ku dziko lina limene adaamlonjeza kuti lidzakhala lake. Ngakhale sankadziŵa kumene ankapita, adapitabe.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika.
Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Pokhala ndi chikhulupiriro, malinga a mzinda wa Yeriko adagwa, Aisraele ataŵazungulira masiku asanu ndi aŵiri.
Poyamba ndikuthokoza Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akusimba za chikhulupiriro chanu.
Yesu atamva zimenezi, adachita chidwi, ndipo adauza anthu amene ankamutsata aja kuti, “Kunena zoona, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Nowa adalandira machenjezo a Mulungu onena za zinthu zomwe mpaka nthaŵi imeneyo zinali zisanaoneke. Adamvera, napanga chombo kuti apulumutse onse a m'banja mwake. Potero adaŵatsutsa kuti ngolakwa anthu a dziko lapansi, nalandira chilungamo chimene Mulungu amapatsa anthu omkhulupirira.
Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.
Pamenepo Yesu adacheuka, naona maiyo, ndipo adati, “Limbani mtima mai, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani.” Nthaŵi yomweyo mai uja adachiradi.
Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.”
Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.
Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.
Paja timaona kuti munthu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, osati pakutsata Malamulo ai.
Pokhala ndi chikhulupiriro timamvetsa kuti zonse zimene zilipo zidalengedwa ndi mau a Mulungu, mwakuti zinthu zoonekazi zidachokera ku zinthu zosaoneka.
Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira.
Koma tsono muzikhala okhazikika kolimba pa maziko a chikhulupiriro chanu, osasunthika pa chiyembekezo chofumira ku Uthenga Wabwino umene mudamva. Uthenga Wabwinowu walalikidwa kwa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo Mulungu ndiye adandipatsa ine, Paulo, ntchito yoti ndiwulalike.
Yesu adaŵayankha kuti, “Chimene Mulungu afuna kuti muchite nchakuti mundikhulupirire Ineyo amene Mulungu adandituma.”
Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.