Mtima wanga uli ndi chikhulupiriro, kukhulupirira zinthu zomwe sindiziona ndi maso anga. Ndimakondwera podziwa kuti Mulungu amasangalala ndi chikhulupiriro changa, pakuti Mawu ake amati popanda chikhulupiriro sitingakondweretse Mulungu. Ndili mwana wa Mulungu, ndimayenda ndi chikhulupiriro, ndikukhulupirira malonjezo a Atate wanga wakumwamba.
Ndi chikhulupiriro ndapeza chipulumutso mwa Khristu. Kuti upulumuke, uyenera kukhulupirira kuti Mulungu aliko, ndipo alikodi ngati mpweya womwe timapuma. Ndi mwa chisomo ndi chikhulupiriro momwe tingalandire Yesu ngati Ambuye wathu, kuchoka mu mdima kulowa mu kuunika kwake kodabwitsa.
Tsiku lililonse, pemphani Yesu kuti akuwonjezere chikhulupiriro chako. Ngati uli ndi kukayikira, werenga Mawu a Mulungu ndipo pemphera mu Mzimu kuti maganizo ako achepe, kuti usakhale ndi moyo wotsatira zomwe waona, koma motsatira zomwe Mulungu wanena. Ukamachita izi, udzakhala wokonzeka ndi mtima wosangalala pa tsiku limene Mulungu adzabwera kudzakutengera kumwamba pamodzi ndi Khristu Yesu.
Konda Mulungu ndi mtima wako wonse, mfunefune ndi moyo wako wonse. Mukamamufunafuna mozama kwambiri, simudzakhalanso ndi nthawi yokayikira za iye, ndipo mzimu wako udzakhala wotetezeka mwa iye.
Ochita zoipa adzalephera, koma ochita chifuniro cha Chauta adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake.
Ifetu sindife anthu oti nkumabwerera m'mbuyo ndi kutayika ai, ndife anthu okhulupirira, kuti tipulumuke.
Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”
Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Tsono pamenepo tinene chiyani? Tinene kuti anthu a mitundu ina, amene sankalabadira zoti akhale olungama pamaso pa Mulungu, adachilandira chilungamocho pakukhulupirira.
Nchifukwa chake lonjezolo maziko ake ndi chikhulupiriro, kuti likhale mphatso yaulere ya Mulungu, ndipo patsimikizike kuti lonjezolo adzalilandiradi anthu ofumira kwa Abrahamu. Osati okhawo amene amasunga Malamulo a Mose ai, komanso onse okhala ndi chikhulupiriro chonga cha Abrahamu. Iye ndiyedi kholo la ife tonse.
Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Pamenepo Yesu adacheuka, naona maiyo, ndipo adati, “Limbani mtima mai, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani.” Nthaŵi yomweyo mai uja adachiradi.
Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse.
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
“Munthu wokhulupirira Mwanayo, sazengedwa mlandu. Koma wosakhulupirira, wazengedwa kale, chifukwa sadakhulupirire Mwana mmodzi yekha uja wa Mulungu.
Koma Yesu adauza maiyo kuti, “Chikhulupiriro chanu chakupulumutsani. Pitani ndi mtendere.”
Nzoona, iwo adakadzukadi chifukwa sadakhulupirire, ndipo inu pakukhulupirira, mukukhala mu mtengo tsopano. Komatu tsono musamadzitame, makamaka muzichita mantha.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu.
Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai, popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.
Paja timaona kuti munthu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, osati pakutsata Malamulo ai.
Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.”
Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”
Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m'dzina lake.
Pakuti chimene Atate anga afuna nchakuti munthu aliyense amene aona Mwanayo namkhulupirira, akhale ndi moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa.
Ndipo ngati enawo aleka kusakhulupirira kwao, adzaŵalumikizanso ku mtengo. Pakuti Mulungu ndi wamphamvu, atha kuŵalumikizanso.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Ngati ndi odalira Malamulo okha amene adzalandire zimene Mulungu adalonjeza, ndiye kuti chikhulupiriro nchopanda pake, ndipo lonjezo lija lilibe phindu.
Nchifukwa chake ndakuuzani kuti mudzafera m'machimo anu. Pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine Ndilipo, mudzaferadi m'machimo anu.”
Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona.
Kumeneko anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu wa ziwalo zakufa ali chigonere pa machira. Poona chikhulupiriro chao, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Limba mtima, mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”
Yesu adaŵayankha kuti, “Muzikhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wolamula phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ atanena ndi mtima wosakayika, nakhulupirira ndithu kuti zimene akunenazo zichitikadi, ndithu zidzachitikadi monga momwe waneneramo. Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [
Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye. Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.
Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu. Adakhulupirira ndithu kuti Mulungu angathe kuchita zimene adalonjeza.
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira munthu. Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira mafumu.
Ngakhale Mulungu andiphe, ndidzamkhulupirirabe, ndipo ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
nchifukwa chake ndilikumva masautsoŵa. Koma sindichita manyazi, pakuti ndimamdziŵa Iye amene ndakhala ndikumkhulupirira, ndipo sindikayika kuti Iyeyo angathe kusunga bwino, mpaka tsiku la chiweruzo, zimene adandisungiza ine.