Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu.
Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu.
Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo.
Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.
Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu. Adakhulupirira ndithu kuti Mulungu angathe kuchita zimene adalonjeza.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano. Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai. Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo. Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo. Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Pamenepo Yesu adacheuka, naona maiyo, ndipo adati, “Limbani mtima mai, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani.” Nthaŵi yomweyo mai uja adachiradi.
Apo Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere.”
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Komatu nchodziŵikiratu kuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Paja Malembo akuti, “Munthu amene ali wolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, adzakhaladi ndi moyo.”
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira munthu. Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira mafumu.
Yesu ataloŵa m'nyumba, akhungu aja adadzampeza, Iye nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukukhulupirira kuti ndingathe kuchita zimenezi?” Iwo adati, “Inde, Ambuye.” Apo Yesu adakhudza maso ao nati, “Zikuchitikireni monga momwe mwakhulupiriramo.”
Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.
Ine ndasankhula njira yoti ndizikhala wokhulupirika, ndaika malangizo anu mumtima mwanga.
Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Koma munthu atangokhulupirira, m'malo mwa kudalira ntchito zake, Mulungu amene amaŵaona kuti ngosapalamula anthu ochimwa, munthu ameneyo pakukhulupirira, Mulungu adzamuwona kuti ngwolungama pamaso pake.
nchifukwa chake ndilikumva masautsoŵa. Koma sindichita manyazi, pakuti ndimamdziŵa Iye amene ndakhala ndikumkhulupirira, ndipo sindikayika kuti Iyeyo angathe kusunga bwino, mpaka tsiku la chiweruzo, zimene adandisungiza ine.
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
Kodi ndinenenso chiyani tsopano? Nthaŵi yachepa yoti ndinene za anthu enanso ambiri monga Gideoni, Balaki, Samisoni, Yefita, Davide, Samuele ndiponso aneneri. Pokhala ndi chikhulupiriro anthu ameneŵa adagonjetsa maufumu, adakhazikitsa chilungamo, ndipo adalandira zimene Mulungu adaaŵalonjeza. Ena adapuya mikango pakamwa, ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.
Apo Yesu adati, “Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu. Zichitikedi zimene mukufuna.” Pompo mwana wake wamkazi uja adachira.
Wolungama wanga adzakhala ndi moyo pakukhulupirira. Koma akamachita mantha nkubwerera m'mbuyo, Ine sindikondwera naye.”
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu.
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Koma tsono muzikhala okhazikika kolimba pa maziko a chikhulupiriro chanu, osasunthika pa chiyembekezo chofumira ku Uthenga Wabwino umene mudamva. Uthenga Wabwinowu walalikidwa kwa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo Mulungu ndiye adandipatsa ine, Paulo, ntchito yoti ndiwulalike.
Paja ifenso tidaumva Uthenga Wabwino, monga iwo aja. Koma iwowo sadapindule nawo mau olalikidwawo, popeza kuti adangoŵamva, koma osaŵakhulupirira.
Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha nathedwa nzeru, nkumafunsana kuti, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani? Angolamula mphepo ndi madzi omwe, izo nkumumveradi.”
Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.
Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya.
Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.
Paja timasanduka anzake a Khristu, malinga tikasunga kwenikweni mpaka potsiriza kulimba mtima kumene tinali nako poyamba.
uli ndi chikhulupiriro ndiponso ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa. Ena sadamvere pamene mtima wao unkaŵatsutsa, motero chikhulupiriro chao chidaonongeka.
Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta. Mundiyankhe pa nthaŵi yabwino, Inu Mulungu, chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, ndi chithandizo chanu chokhulupirika.
Onseŵa adasunga chikhulupiriro chao mpaka kufa. Sadalandire zimene Mulungu adaaŵalonjeza, koma adangoziwonera chapatali ndi kuzikondwerera. Adaavomera kuti pansi pano analidi alendo osakhazikika.
Pakuti pamene tili mwa Khristu Yesu, kuumbalidwa kapena kusaumbalidwa kulibe kanthu, chachikulu nchakuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.
Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu.
Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Apo Abramu adakhulupirira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama.
Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
Pamene iwo adafikanso kumene kunali khamu la anthu kuja, munthu wina adadzagwadira Yesu. Adati, “Ambuye mchitireni chifundo mwana wanga. Ali ndi khunyu ndipo amavutika koopsa. Kaŵirikaŵiri amagwa pa moto mwinanso m'madzi. Ndinabwera naye kwa ophunzira anuŵa, koma alephera kumchiritsa.” Yesu adati, “Ha! Anthu a m'badwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo! Ndiyenera kukhala nanube mpaka liti? Ndiyenera kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwanayo.” Atatero, Yesu adazazira mzimu woipawo, ndipo udatuluka mwa mnyamatayo. Pompo iye adachira. Pambuyo pake ophunzira aja adadza kwa Yesu paseri namufunsa kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?” Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona. Nkhope yake idaŵala ngati dzuŵa, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [
Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupirika, pakuti sangathe kudzitsutsa.”
Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu. Monsemo Abrahamu ankadikira mzinda wa maziko okhazikika. Mzindawo, Mmisiri woganiziratu mamangidwe ake ndiponso woumanga, ndi Mulungu. Pokhala ndi chikhulupiriro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika. Nchifukwa chake mwa munthu mmodzi, wotinso anali ngati wakufa, mudatuluka mibadwo yochuluka ngati nyenyezi, ndi yosaŵerengeka ngati mchenga wa pa gombe la nyanja. Onseŵa adasunga chikhulupiriro chao mpaka kufa. Sadalandire zimene Mulungu adaaŵalonjeza, koma adangoziwonera chapatali ndi kuzikondwerera. Adaavomera kuti pansi pano analidi alendo osakhazikika. Paja anthu olankhula motere, amaonekeratu kuti akufunafuna malo ao enieni okhazikikamo. Akadakhala kuti ankaganizirako za kudziko kumene adaachokera, bwenzi atapeza danga lakuti abwerere kwakaleko. Koma monga zilirimu tikuwona kuti ankafuna dziko lina, lokoma kopambana, ndiye kuti dziko la Kumwamba. Nchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wao, popeza kuti Iye adaŵakonzera mzinda. Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu, pamene Mulungu adamuyesa, adapereka Isaki ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu adaampatsa lonjezo, adakhala wokonzeka kupereka ngati nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. Za mwana ameneyu Mulungu anali atanena kuti, “Mwa Isaki udzakhala ndi zidzukulu.” Abrahamu ankakhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa munthu kwa akufa. Tsono tingathe kunena mofanizira kuti adamlandiranso Isakiyo ngati wouka kwa akufa. Pokhala ndi chikhulupiriro, makolo anthu akale aja Mulungu adaonetsa kuti ankakondwera nawo.
Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Paja Malembo akuti bwanji? Akuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo pakukhulupirirapo, Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”
Inu mumakhulupirira kuti Mulungu ndi mmodzi yekha. Ai chabwino, mumakhoza, komatu ndi mizimu yoipa yomwe imakhulupirira zimenezi, imachitanso kunjenjemera.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.
Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika.
Komabe tikudziŵa kuti munthu sangapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo, koma pakukhulupirira Yesu Khristu. Ifenso tidakhulupirira Khristu Yesu kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira Khristu, osati chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Pakuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo.
Kumbukirani masiku akale aja mutangolandira kuŵala chatsopano. Pa nthaŵi imene ija mudaalimbana ndi mazunzo ambiri. Mwina ankakunyozani ndi kukuchitani chipongwe, anthu akuwonerera. Mwinanso munkamva nawo zoŵaŵa amene ankasautsidwa motero. Munkasaukira limodzi ndi amene adaaponyedwa m'ndende, ndipo mudalola mokondwa kuti alande chuma chanu, mutadziŵa kuti muli ndi chuma choposa ndi chosatha.
Koma munthu akamadya ali wokayika, waweruzidwa kale kuti ngwolakwa, popeza kuti zimene akuchita nzosagwirizana ndi zimene iye amakhulupirira kuti nzoyenera. Paja chilichonse chimene munthu achita, chotsutsana ndi zimene iye amakhulupirira, chimenecho ndi tchimo.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Pakuti ngakhale sindili nanu m'thupi, komabe mumtimamu ndili nanu pamodzi. Ndipo ndakondwa kuwona kuti mukulongosola bwino zonse, ndi kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu nchosagwedezeka konse.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta. Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake. Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta, mundikhululukire machimo anga pakuti mlandu wanga ndi waukulu. Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate. Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao. Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye, ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake. Maso anga akuyang'ana kwa Chauta nthaŵi zonse, pakuti adzaonjola mapazi anga mu ukonde. Inu Chauta yang'aneni ine, ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha, ndipo ndazunzika kwambiri. Mundichotsere nkhaŵa za mumtima mwanga, ndipo munditulutse m'masautso anga. Penyani mazunzo anga ndi mavuto anga, ndipo mundikhululukire machimo anga onse. Onani m'mene adani anga ankhalwe achulukira ndi m'mene chidani chao ndi ine chakulira. Ndikuika mtima wanga pa Inu Mulungu wanga. Musalole kuti adani anga andichititse manyazi, musalole kuti akondwere pamene ine ndikuvutika.
“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu.
Ndimalirira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu kothaŵira kwanga, ndinu zanga zonse m'dziko la amoyo.”
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino. Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika. Munthu wabwino amalankhula zanzeru, pakamwa pake pamatuluka zachilungamo. Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno. Munthu woipa amazonda munthu wabwino, amafunafuna kuti amuphe. Koma wolungamayo Chauta sadzamsiya yekha m'manja mwa mdani wake, sadzalola kuti pomuweruza, mlandu wake umuipire. Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka. Ndidaona munthu woipa akunyada ndi kudzitukumula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Koma pambuyo pake, podutsanso, ndidaona kuti palibe. Ngakhale ndidamfunafuna, sindidathe kumpeza. Upenye munthu wopanda cholakwa ndi wolungama, ndipo udzapeza kuti munthu wamtendere ali ndi zidzukulu zambiri. Koma anthu ochimwa adzaonongekeratu kwathunthu, iwo pamodzi ndi zidzukulu zao zomwe. Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.
Ndaganiza kuti nkofunikadi kuti ndikutumizireni mbale wathu uja, Epafrodito. Mudaamtuma kuti adzandithandize pa zosoŵa zanga, ndipo wagwiradi ntchito ndi kumenya nkhondo yachikhristu pamodzi ndi ine. Tsonotu akukulakalakani nonsenu, ndipo ndi wokhumudwa podziŵa kuti inu mudamva zoti iye ankadwala. Nzoonadi adaadwala zedi mpaka pafupi kufa. Mwai kuti Mulungu adamchitira chifundo. Ndipotu sadangochitira chifundo iye yekhayu, komanso ineyo, kuti chisoni changa chisakhale chosanjikizana. Nchifukwa chake ndikufunitsitsa ndithu kumtumiza kwa inu, kuti podzamuwonanso mudzasangalale, kutinso nkhaŵa yanga ichepeko. Mlandireni mwachikhristu ndi chimwemwe chachikulu. Anthu otere muziŵachitira ulemu. Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika. Koma kulimbika kumeneku kuzigwira ntchito yake kotheratu, kuti mukhale angwiro, opanda chilema ndi osapereŵera pa kanthu kalikonse.
Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
Yesu atamva zimenezi, adachita chidwi, ndipo adauza anthu amene ankamutsata aja kuti, “Kunena zoona, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Koma Malembo akunenetsa kuti zinthu zonse zili mu ulamuliro wa uchimo, kuti pakukhulupirira Yesu Khristu, anthu okhulupirira alandiredi zimene Mulungu adalonjeza.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.
Pompo Yesu adatambalitsa dzanja nkumugwira nati, “Iwe wa chikhulupiriro chochepawe, unakayikiranji?”
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”