Mawu a Mulungu ndi nyali yowunikira mtima wanga, yondiwongolera, yondipatsa nzeru kuchokera kumwamba. Ndiyo chinsinsi chotsegulira njira yolankhulirana ndi Atate wanga wakumwamba komanso Mwana wawo wokondedwa Yesu Khristu.
Ndikagwiritsa ntchito Malemba moyenera, mawu anga amakhala ndi mphamvu chifukwa Mawu a Mulungu ndi oona, okhulupirika, ndipo nthawi zonse amapezeka ndikawafuna.
Ndiyenera kuphunzira, kusinkhasinkha, kufufuza, ndi kusunga Malemba mumtima mwanga kuti ndidziwe choonadi ndi kumasulidwa ku mabodza onse a mdani.
"Malemba onse ndi ouziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kulangiza, ndi kulera m'chilungamo." (2 Timoteo 3:16)
Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha ophunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.
Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.
lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.
Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.
Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandire monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.
Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.
Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.
Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru. Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke kumaso ako; uwasunge m'kati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lao lonse.
Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.
Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.
Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.
Ndipo Yehova anatulutsa dzanja lake, nakhudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako;
Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, Chifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.
Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.
Kodi mau anga safanafana ndi moto? Ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?
Chifukwa chake uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzachitika, ati Ambuye Yehova.
Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.
Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe;
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.
Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.
Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.
Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.
Koma chitani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a chikhulupiriro, amene ife tiwalalikira:
Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.
Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.
Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhale ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.
umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirire chabe.
Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.
koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.
Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,
akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamange chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe.
chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu mu Mwamba, chimene mudachimva kale m'mau a choonadi cha Uthenga Wabwino,
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwe kuchokera mu zoonekazo.
Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.
Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoyamba za zolengedwa zake.
Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.
Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri! Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.
inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa; koma Mau a Ambuye akhala chikhalire. Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.
lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;
akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.
Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu; Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m'chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu. ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.
Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu; mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka; koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chionongeko cha anthu osapembedza.
Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m'maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo,
Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.
Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.
Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sangathe kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.
Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.
Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.
Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye. Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala. Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.
Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako; uwamange pamtima pako osaleka; uwalunze pakhosi pako. Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m'tulo, ndi kulankhula nawe utauka.
Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.
Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.
Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.
Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mau a chinenero cha buku ili, Munthu akaonjeza pa awa, adzamuonjezera Mulungu miliri yolembedwa m'bukumu: ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.