Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 33:6 - Buku Lopatulika

6 Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa. Zonse zakumeneko zidalengedwa pamene Iye adalankhula mau ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 33:6
18 Mawu Ofanana  

Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pamadzi, lilekanitse madzi ndi madzi.


Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.


Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.


Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.


Mwa mzimu wake anyezimiritsa thambo; dzanja lake linapyoza njoka yothawayo.


Mzimu wa Mulungu unandilenga, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.


Potumizira mzimu wanu, zilengedwa; ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi.


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.


ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.


Ndipo pamene anati ichi anawapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera.


amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.


ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.


Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwe kuchokera mu zoonekazo.


Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa