Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 17:11 - Buku Lopatulika

11 Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Amenewa anali mfulu koposa a m'Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ayuda akumeneko anali a mitima yomasuka, kusiyana ndi aja a ku Tesalonika. Iwoŵa adalandira mau a Mulungu ndi mtima wofunitsitsa, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza m'Malembo kuti aone ngati nzoona zimene Paulo ndi Silasi ankanena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 17:11
34 Mawu Ofanana  

Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.


Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu.


Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku, kuti ndilingirire mau anu.


Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.


kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira; ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;


Landirani mwambo wanga, si siliva ai; ndi nzeru kopambana ndi golide wosankhika.


Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake; ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira.


Funani inu m'buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzake; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wake wasonkhanitsa iwo.


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.


monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,


tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.


Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.


Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;


Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.


Koma atumwi ndi abale akukhala mu Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu.


Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda.


Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.


Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti tichite mau onse a chilamulo ichi.


Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;


Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandire monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.


ndi m'chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandire, kuti akapulumutsidwe iwo.


Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.


lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa