Yeremiya 5:14 - Buku Lopatulika14 Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, Chifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, Chifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Nchifukwa chake tsono Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, akuti, “Poti iwowo atero, mau anga ndidzaŵasandutsa moto m'kamwa mwako, anthuwo ndidzaŵasandutsa nkhuni, ndipo motowo udzaŵapserezeratu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti, “Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa, tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwako ndipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu. Onani mutuwo |