Atate wathu wakumwamba watilangiza kuti tizipemphera nthawi zonse. Ndi m’pemphero momwe timayanjana ndi Mulungu wathu. Pemphero ndi njira yolankhulirana ndi Mulungu. Ndi m’pemphero momwe timaperekera mapempho athu onse pamapazi a Mlengi wathu. Ndi komwe timapita zinthu zikavuta, tili ndi nkhawa, kapena titakhala achisoni.
Mulungu amadziwa kale zosowa zathu, ndipo ankadziwa miyoyo yathu tisanabadwe. Koma amafuna kuti tizilankhula naye, kuti timufunefune. Mukapemphera, mumayamba kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Mumapanga ubale wolimba naye. Pemphero ndi chida champhamvu kwa ife okhulupirira Yesu. Ndi chida chodzitetezera pa nkhondo iliyonse. Ndi m’pemphero momwe mumapezera chipambano pa chilichonse.
Mphamvu ya pemphero sichokera kwa inu, koma kwa Yesu. Iye ndiye amayankha mapemphero ndi kuchititsa zinthu zomwe sizingatheke kwa anthu. Mukapemphera ndi mtima wonse, mumapeza chitonthozo, mtendere, ndi chikondi cha Atate. Yandikirani kwa Mulungu ndi mtima wodzichepetsa ndi wachisoni, ndipo sadzakukanani. (Aefeso 6:18)
Pemphani mwa Mzimu nthawi zonse, ndi mapempho osiyanasiyana. Khalani maso, ndipo pempherani nthawi zonse chifukwa cha oyera mtima onse. Mukapemphera, yambani ndi kuyamika Mulungu. Osangopereka mapempho anu okha, komanso khalani chete pamaso pake. (Atesalonika 1 5:16-18) Khalani okondwa nthawi zonse, pempherani nthawi zonse, ndipo yamikani Mulungu pa chilichonse, pakuti ichi ndi chifuniro chake kwa inu mwa Khristu Yesu.
Ine ndidzathokoza Chauta chifukwa cha kulungama kwake, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Chauta, Wopambanazonse uja.
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
“Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta, palibe wina koma Iye yekha. Palibe thanthwe lina lotchinjiriza lofanafana ndi Mulungu wathu.
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita pamaso pa onse okumverani.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano. Mtamandeni, inu okhala m'dziko lonse lapansi! Mtamandeni, inu zolengedwa zonse zam'nyanja. Imbani, inu maiko akutali ndi onse okhala kumeneko.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
Pambuyo pake ku mpando wachifumu uja kudachoka mau akuti, “Tamandani Mulungu wathu, inu nonse atumiki ake, inu nonse omuwopa, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe.”
Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a m'maiko onse,
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga, ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse mpaka muyaya.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cham'nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.”
Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza.
Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”
Koma wopereka mtima wake kwa Ine mothokoza, ndiye amene amandilemekeza. Woyenda m'njira zolungama, ndidzamuwonetsa chipulumutso changa.”
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.
Koma ine ndidzapereka nsembe kwa Inu ndi mau okuthokozani. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita ndithu. Chipulumutso nchochokera kwa Inu Chauta.”
Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.
Tsono nanenso ndidzalalika za kulungama kwanu. Ndidzakutamandani masiku onse, Inu Chauta.
“Zoonadi, ndinu aakulu, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha.
Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
Ndidzapambana adani anga ondizungulira, ndipo ndidzapereka nsembe m'Nyumba mwake ndili kufuula ndi chimwemwe. Ndidzaimba nyimbo yotamanda Chauta.
Adaafuna kuti tizitamanda ulemu wake chifukwa adatikomera mtima kopambana, pakutipatsa Mwana wake wokondedwa ngati mphatso yaulere.
Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Ndimamuuza Chauta kuti, “Inu ndinu Ambuye anga. Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.”
Munenenso kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, mutisonkhanitse ndi kutilanditsa kwa mitundu ina ya anthu, kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera, ndi kuti tizinyadira pokutamandani.
Mupereke buledi wanu kuti muthokoze Mulungu. Munene poyera ndi kulengeza zopereka zanu zaufulu, pakuti nzimene mumakonda kuchita, inu Aisraele.” Akutero Chauta.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Iwo aja atayamba kuimba ndi kutamanda, Chauta adaŵatchera msampha Aamoni, Amowabu ndiponso anthu a ku phiri la Seiri, amene adaadzalimbana ndi anthu a ku Yuda, kotero kuti adaŵagonjetsa onse.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse.
Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oŵazunzawo.
Mundikomere mtima, Inu Chauta. Onani m'mene akundisautsira anthu ondida. Inu mumandipulumutsa ku imfa,
kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse, pakati pa anthu anu a mu Ziyoni. Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa.
Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe. Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika wotcha iwo omwe.
Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe.
Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu.
Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe.
Dzambatukani, Inu Chauta, munthu asakunyozeni. Azengeni mlandu anthu akunja.
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Bwerani ndi zopereka, ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake. Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera.
Mitundu yonse ya anthu imene mwailenga idzabwera, idzakuŵeramirani, Inu Ambuye, ndipo idzalemekeza ukulu wanu.
Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.
Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi. Imbani mwaluso nyimbo zotamanda.
Paja ifeyo ndiye oumbala enieni, ife amene timapembedza Mulungu motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Timanyadira Khristu Yesu, osadalira miyambo ya thupi chabe.
Tsono tikamati, “Ambuye,” tikunena Mzimu Woyera. Ndipo kumene kuli Mzimu wa Ambuye, kuli ufulu.
Tonsefe, opanda chophimba nkhope yathu, timaonetsa ulemerero wa Ambuye, monga momwe galasi limaonetsera nkhope ya munthu. Monsemo Ambuye, amene ali Mzimu, amatisandutsa kuti tifanefane naye, ndi kukhala nawo ulemerero wake mochulukirachulukira.
Mulungu adzambatuke, adani ake amwazikane. Onse amene amamuda, athaŵe pamaso pake.
Anthu anu adapezamo malo okhala. Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao mwa ubwino wanu.
Ambuye apereka lamulo. Nchachikulu chiŵerengero cha amene abwera ndi uthenga wakuti,
“Mafumu a magulu a ankhondo akuthaŵa, indedi akuthaŵa. Tsono azimai ku mudzi akugaŵana zofunkha, ngakhale atsalira pakati pa makola ankhosa.
“Zofunkhazo zikuwoneka ngati mapiko a nkhunda okutidwa ndi siliva, nthenga zake nzokutidwa ndi golide wonyezemira.”
Pamene Mphambe adabalalitsa mafumu kumeneko, ku Zalimoni kudagwa chisanu choopsa.
Iwe phiri la Basani, phiri laulemerero, Iwe phiri la Basani, phiri la nsonga zambiri!
Iwe phiri la nsonga zambiriwe, chifukwa chiyani ukuliyang'ana mwansanje phiri limene Mulungu adasankha kuti azikhalapo? Ndithu Chauta adzakhalapo mpaka muyaya.
Ambuye adafika ku malo ao oyera kuchokera ku Sinai, ali ndi magaleta amphamvu zikwi zambirimbiri.
Inu mudakwera kumwamba, mutatenga am'ndende ambiri, ndipo mudalandira mphatso kwa anthu, ngakhale kwa anthu oukira, kuti mudzakhale kumeneko, Inu Chauta Mulungu.
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
Amwazeni iwowo monga m'mene mphepo imachitira utsi. Anthu oipa aonongeke pamaso pa Mulungu, monga m'mene sera amasungunukira pa moto.
Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa, ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa.
Koma Mulungu adzatswanya mitu ya adani ake, mitu ya anthu onse oyenda m'machimo ao.
Ambuye adati, “Ndidzaŵabweza adani anu kuchokera ku Basani, ndidzaŵabweza kuchokera ku nyanja yozama,
kuti musambe mapazi anu m'magazi, kuti agalu anu anyambiteko magazi a adaniwo.”
Inu Mulungu, mdipiti wa anthu anu oyenda mwaulemu ukuwoneka, mdipiti wolemekeza Mulungu wanga, Mfumu yanga, wokaloŵa m'malo opatulika.
Oimba nyimbo zapakamwa atatsogola, oimba ndi zipangizo ali pambuyo, anamwali oimba ting'oma ali pakati.
“Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu. Tamandani Chauta, inu zidzukulu za Israele.”
Patsogolo pao pali Benjamini mng'ono wa onsewo, akalonga a Yuda ali pambuyo, ndiponso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafutali.
Kungani mphamvu zanu, Inu Mulungu, onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu, amene mumatichitira zamphamvu.
Chifukwa cha Nyumba yanu ya ku Yerusalemu, mafumu amabwera ndi mphatso kwa Inu.
Koma anthu anu Mulungu, akondwere, asangalale pamaso panu, inde, asekere ndi chimwemwe.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta, inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Aisraele asangalale ndi Mlengi wao. Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yao.
Atamande dzina lake povina, amuimbire nyimbo yokoma ndi ng'oma ndi pangwe.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi. Kumwamba amaimba nyimbo zotamanda ulemerero wanu.
Nawonso ana ndi makanda omwe amauimbira. Mwamanga linga chifukwa cha adani anu, kuti mugonjetse onse okuukirani.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.