Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu.
Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
Chimalizo cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake khalani ochenjera ndi odziletsa, kuti muthe kupemphera.
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga. M'maŵa ndimapemphera kwa Inu, ndi kudikira kuti mundiyankhe.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.
Adati, “Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautsochi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Pemphero langa likwere kwa Inu ngati lubani, kukweza kwa manja anga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
Ndimakonda Chauta chifukwa amamva mau anga omupemba. Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati, “Ndazunzika koopsa.” Pamene ndinkachita mantha, ndidati, “Anthu ndi osakhulupirika.” Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira? Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta, ndi yamtengowapatali pamaso pake. Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni, mwana wa mdzakazi wanu. Inu mwamasula maunyolo anga. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Ndidzazipereka m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, mu mzinda wa Yerusalemu. Tamandani Chauta! Iye amatchera khutu kuti andimve, nchifukwa chake ndidzampempha nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Nchifukwa chake, kuyambira tsiku limene tidamva zimenezi, sitileka kukupemphererani. Timapempha Mulungu kuti akudzazeni ndi nzeru ndi luntha, zimene Mzimu Woyera amapatsa, kuti mumvetse zonse zimene Iye afuna.
Masiku amenewo Yesu adapita ku phiri kukapemphera, ndipo adachezera usiku wonse akupemphera kwa Mulungu.
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa.
Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu.
Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika tsiku ndi tsiku, Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo, ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi.
Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera? Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
Ndidafuula kwa Iye, ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga. Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera. Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa. Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu. Mulungu atamandike chifukwa sadakane pemphero langa, sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.
Imvani pemphero langa, Inu Chauta. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. Mundiyankhe chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndi kulungama kwanu.
Imvani, Inu Chauta, pamene ndikulira mofuula, mundikomere mtima ndi kundiyankha. Pajatu Inu mudati, “Muzifunafuna nkhope yanga.” Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu.
Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta. Mundiyankhe pa nthaŵi yabwino, Inu Mulungu, chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, ndi chithandizo chanu chokhulupirika.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.
Ndidalankhula mwankhaŵa kuti, “Andipirikitsira kutali ndi Inu.” Koma Inu mudamva kupempha kwanga pamene ndidakudandaulirani kuti mundithandize.
Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.
Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
Pa tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mungapemphe kwa Atate potchula dzina langa, adzakupatsani. Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”
Mulungu adaŵathandiza pomenya nkhondoyo, ndipo Ahagiriwo pamodzi ndi onse amene adaaphatikana nawo, adaperekedwa m'manja mwao. Ankalira kwa Mulungu pomenya nkhondoyo, tsono Mulungu adaŵapatsa zimene ankapemphazo, popeza kuti adaamkhulupirira.
Hana adapemphera nati, “Mtima wanga ukukondwa chifukwa cha zimene Chauta wandichitira, Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta. Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola. Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa.
Adati, “Inu Chauta, pamene ndinali m'mavuto ndidakuitanani, ndipo mudandiyankha. Pamene ndinali m'dziko la akufa ndidalira kwa Inu kuti mundithandize, ndipo mudamva pempho langa.
Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo.
Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.
“Pamene mukupemphera, musachite monga anthu achiphamaso aja. Iwowo amakonda kuimirira ndi kupemphera m'nyumba zamapemphero ndi pa mphambano za miseu yam'mizinda. Amachita zimenezi kuti anthu aŵaone. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.
Ndikulirira Mulungu Wopambanazonse, Mulungu amene amandichitiradi zonse zimene walonjeza.
Nthaŵi imeneyo mudzandiitana ndi kumanditama mopemba, ndipo ine ndidzakumverani. Mudzandifunafuna, ndipo mudzandipeza. Mukadzandifunafuna ndi mtima wanu wonse,
Ndikupemphera kwa Inu Mulungu, chifukwa mudzandiyankha. Tcherani khutu kuti mumve mau anga.
Ndithudi, inu anthu a ku Ziyoni, okhala ku Yerusalemu, simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu, ndipo akadzangomva, pompo adzakuyankhani.
Ndikulira mopemba kwa Mulungu, ndi mau okweza ndikufuula kwa Mulungu kuti andimve. “Chondiŵaŵa ndi chakuti, Mulungu Wopambanazonse wasintha mchitidwe wake.” Komabe ndidzakumbukira ntchito zanu, Inu Chauta, inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zakalekale. Ndidzasinkhasinkha za zonse zimene mwachita, ndidzalingalira za ntchito zanu zamphamvuzo. Njira zanu, Inu Mulungu, nzoyera. Kodi alipo mulungu winanso wamkulu ngati Mulungu wathu? Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu. Mudaombola anthu anu ndi mkono wanu wamphamvu, ndiye kuti ana a Yakobe ndi Yosefe. Pamene madzi adakuwonani, Inu Mulungu, pamene madzi adakuwonani, adachita mantha, inde, nyanja yakuya idanjenjemera. Mitambo idachucha madzi, mumlengalenga mudachita bingu. Zing'aning'ani mbali ndi mbali. Phokoso la bingu lanu lidamveka konsekonse, mphezi zanu zidaŵalitsa dziko lonse, dziko lapansi lidanjenjemera ndi kugwedezeka. Inu mudadzera pa nyanja, njira yanu idadzera pa madzi akuya, komabe mapazi anu sadaoneke. Pa tsiku lamavuto ndimafunafuna Ambuye. Usiku wonse ndimakweza manja anga ndi kupemphera kosalekeza. Mtima wanga umakana kuusangalatsa.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Chauta amayang'ana anthu omumvera, ndi odalira chikondi chake chosasinthika. Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala.
“Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu,
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga.
Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Komabe Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani pemphero la ine mtumiki wanu ndi kupemba kwanga. Mverani kulira kwanga ndiponso pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu lero lino.
Ndi mtima wonse timapemphera usana ndi usiku kuti tiwonane nanunso maso ndi maso, kuti tikakwaniritse zimene zikusoŵa pakuwonetsa chikhulupiriro chanu.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa. Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.
Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
Ukadzapemphera kwa Iye adzakumvera, udzapereka kwa Iye zija udalumbira kuti udzaperekazi.
Yabezi adatama Mulungu wa Israele mopemba kuti, “Mundidalitse ine, ndipo dziko langa mulikuze. Dzanja lanu lamphamvu likhale nane, ndipo mundisunge ine, kuti choipa chisandigwere ndi kumandisautsa.” Motero Mulungu adampatsadi zimene adaapemphazo.
Inu nomwe muthandizane nafe pakutipempherera. Pamenepo anthu ambiri adzathokoza Mulungu m'malo mwathu, chifukwa cha zimene Iye adatichitira mwa kukoma mtima kwake.
Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu.
Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu.
Nchifukwa chake Davide adatamanda Chauta pamaso pa msonkhano wonse. Adati, “Mutamandike mpaka muyaya Inu Chauta, Mulungu wa Israele, kholo lathu. Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu. Tsopano tikukuthokozani, Inu Mulungu wathu, ndi kutamanda dzina lanu laulemerero.
Anthu inu, ikani mtima wanu pa Iye nthaŵi zonse. Muuzeni zonse za kukhosi kwanu. Mulungu ndiye kothaŵira kwathu.
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Petro adaŵapempha onse kuti atuluke, ndipo adagwada pansi nkumapemphera. Kenaka adatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka!” Apo Tabita adatsekula maso, ndipo pamene adaona Petro, adakhala tsonga.
Koma mngeloyo adamuuza kuti, “Usaope, Zakariya, Mulungu wamva pemphero lako. Mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani.
Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Muzimva mapemphero opemba a mtumiki wanu ndiponso a anthu anu Aisraele, akamapemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mutikhululukire.
Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima.
Inutu ndinu kothaŵira kwanga, nsanja yolimba yonditeteza kwa adani. Mundilole ndizikhala m'Nyumba mwanu nthaŵi zonse. Mundilole ndibisale pansi pa mapiko anu kuti munditeteze.
Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
Koma maso anga amayang'anirabe kwa Inu, Chauta Mulungu wanga. Ndimathaŵira kwa Inu kuti munditeteze, musandisiye opanda wonditchinjiriza. Mundipulumutse ku msampha umene iwo anditchera, ndi ku makhwekhwe a anthu ochita zoipa.
Atapemphera kwa Iye, Mulungu adamva kupempha kwake ndi kupemba kwake, ndipo adambwezanso ku Yerusalemu mu ufumu wake. Motero Manase adadziŵa kuti Chauta ndi Mulungu.
Koma tsono ndimayembekezera Inu Chauta, Ndinu Chauta, Mulungu wanga amene mudzayankha.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani. Tcherani khutu, Inu Chauta, kuti mumve pemphero langa. Mverani kulira kwanga kopemba. Pa tsiku lamavuto ndimakuitanani, pakuti mumayankha mapemphero anga.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m'mapemphero athu.
Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta, koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa.
Motero Petro ankasungidwa m'ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.