“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.
Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.
“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”
Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.
Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala?
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake?
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Ndipo Mulungu adati, “Ine ndemwe ndidzapita nawe pamodzi, ndipo ndidzakupatsa mtendere.”
Ambuye, eniake mtendere amene, akupatseni mtenderewo nthaŵi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Ndimagona ndipo ndimapeza tulo. Ndimadzukanso m'maŵa pakuti Chauta amanditchinjiriza.
Sindichita mantha ngakhale adani anga ndi osaŵerengeka, ngakhale andizinge ndi kundithira nkhondo.
Ndikagona pabedi panga ndimalingalira za Inu, usiku wonse ndimasinkhasinkha za Inu.
Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa, ndipo m'katikati mwangamu ndikusangalala. Thupi langanso lidzakhala pabwino,
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Koma amene amamvera ine adzakhala pabwino, adzakhala mosatekeseka, osaopa choipa chilichonse”.
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?
Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu.
Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.
Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziŵa, ndipo zimanditsatira.
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga.
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Anthu a Mulungu adzakhala m'midzi yamtendere, m'nyumba zokhulupirika, ndiponso m'malo ousira abata.
Mumtima mwa anthu opangana zoipa mumakhala kunama, koma anthu olinga zabwino amakhala ndi chimwemwe.
Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza, amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu.
Mumampumitsa pa nthaŵi yamavuto, mpaka woipa ataloŵa m'dzenje.
Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu,
“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Ndimve zimene Chauta adzalankhula, chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake, kwa anthu ake oyera mtima, ngati sabwereranso ku zopusa zao.
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Mulungu ali m'kati mwa mzindawo, sudzaonongeka konse. Mulungu adzauthandiza dzuŵa lisanatuluke.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga.
Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu.
Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.
Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu.
Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza.
Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa.
Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera.
Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!”
Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza.
Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe.
Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.”
Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana.
Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Adavutika poona mavuto ao onse, Mngelo wochokera kwa Iye adaŵapulumutsa. Adaŵaombola mwa chikondi ndi chifundo chake. Wakhala akuŵasamala ngati ana kuyambira kale.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa.
Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo, motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe.
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa.
Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo.
Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.
Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?
Pamene ndinali m'mavuto ndidapemphera kwa Chauta, ndipo Iye adandichotsera mavutowo.
Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani?
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu.
Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Inu mwakhala ngati ngaka kwa anthu osauka, mwakhala ngati linga kwa anthu osoŵa pa nthaŵi yamavuto. Mwakhala ngati pobisalirapo namondwe, ndiponso ngati mthunzi wousirapo dzuŵa. Anthu ankhalwe ali ngati namondwe woomba pa khoma, ngati chitungu m'dziko louma.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo ndiponso machimo ako ngati nkhungu. Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.”
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.
Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu.
Mumaŵadyetsa zonona m'nyumba mwanu, ndipo mumaŵamwetsa madzi a mu mtsinje wa madalitso anu.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.
Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”
Mulungu wathu ndi wa chifundo chachikulu, adzatitumizira kuŵala kwa dzuŵa lam'maŵa kuchokera Kumwamba.
Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
“Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Mudzanditsitsimutsanso Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa, mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka.
Inu mudzaonjezera ulemu wanga ndipo mudzandisangalatsanso.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera.
Zoonadi, amene amasunga Israele, ndithu sadzaodzera kapena kugona.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja,
Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu.
Inde, Mulungu adatipulumutsa, koma tikuyembekezabe chipulumutsocho. Koma tsono tikamaona ndi maso zimene tikuziyembekezazi, apo si chiyembekezonso ai.
Koma ngati tiyembekeza zimene sitidaziwone ndi maso, timazidikira mopirira.
Chauta amatsekula maso a anthu osapenya, Chauta amakweza anthu otsitsidwa. Chauta amakonda anthu ochita chilungamo.
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa.
Nchifukwa chake, monga Malembo anenera, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.”
Nthaŵi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu.
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
Chauta akunena kuti, “Ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati mtsinje wa madzi. Chuma cha mitundu ya anthu chidzafika kwa inu ngati mtsinje wosefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene mai wake wamnyamulira pambalipa, kapena akumluluza pa maondo.
Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!”
Nzoonadi, kupembedza Mulungu kumapindulitsa kwambiri, malinga munthu akakhutira ndi zimene ali nazo.
Sitidatenge kanthu poloŵa m'dziko lino lapansi, ndipo sitingathenso kutenga kanthu potulukamo.
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.
Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa.
Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse.
Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.