“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Kuli bwino kudya mkute wouma pali bata, kuposa kuchita madyerero m'nyumba m'mene muli mikangano.
Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.
Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
Ndimve zimene Chauta adzalankhula, chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake, kwa anthu ake oyera mtima, ngati sabwereranso ku zopusa zao.
Ambuye, eniake mtendere amene, akupatseni mtenderewo nthaŵi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama, ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Ndili wokhazikika pa malo opanda zovuta, ndipo ndidzatamanda Chauta pa msonkhano waukulu.
Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Anthu osasamala za Mulungu muŵachititse manyazi, chifukwa andilakwira pondinamizira. Koma ine ndidzasinkhasinkha za malamulo anu.
Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino. Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako. Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta.
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi, kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa pali chidani.
Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.
Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti, “Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu, zinthu ziziŵayendera bwino. Mtendere ukhale m'kati mwa makoma ako, bata likhale m'nyumba zako zachifumu.”
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola. Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu.
Amadzetsa mtendere m'malire a dziko lako, amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Upenye munthu wopanda cholakwa ndi wolungama, ndipo udzapeza kuti munthu wamtendere ali ndi zidzukulu zambiri.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Mumtima mwa anthu opangana zoipa mumakhala kunama, koma anthu olinga zabwino amakhala ndi chimwemwe.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake! Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.
Ngwodala munthu amene Inu mumamsankha nkubwera naye kudzakhala m'mabwalo anu. Mutikhutitse ndi zinthu zabwino za m'Nyumba yanu, Nyumba yanu yoyera.
Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.
Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
Adzalandira madalitso kwa Chauta, ndipo Mulungu Mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.
Chauta adatontholetsa namondwe, ndipo mafunde apanyanja adachita bata. Waŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko onse, kuchokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera. Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata, ndipo Chauta adakaŵafikitsa kudooko kumene ankalinga.
Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta, ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Koma ndimadalira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.” Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza.
Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.
Malonjezo a Chauta ndi angwiro, ali ngati siliva womkometsa m'ng'anjo yamoto, woyeretsedwa kasanunkaŵiri. Titetezeni, Inu Chauta, titchinjirizeni nthaŵi zonse kwa anthu ameneŵa,
Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe. Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo. Ng'ombe yaikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ndipo ana ao adzagona pamodzi. Mkango udzadya udzu ngati ng'ombe. Mwana woyamwa adzaseŵera pa dzenje la mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake ku funkha la mphiri, osalumidwa. Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena choononga pa phiri lopatulika la Mulungu. Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi adzakhala odzaza ndi nzeru ya kudziŵa Chauta, monga nyanja imadzazira ndi madzi.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye. Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima. Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Muphunzitse mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma. Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Munthu abwino amakhala mwachilungamo, ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake.
Mtima wanga wonse umalakalaka Inu usiku, mzimu wanga m'kati mwa ine umakufunafunani. Pamene muweruza dziko lapansi, anthu onse okhalamo amaphunzira chilungamo.
Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
‘Choipa chikatigwera mwachilango, monga nkhondo, mlili kapena njala, tidzaima m'Nyumba ino ndiponso pamaso panu, popeza kuti dzina lanu lili m'Nyumba muno. Tsono tidzalira kwa Inu pa mavuto athu, Inuyo mudzamva, ndipo mudzatipulumutsa.’
Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga. Adakwera pa mkerubi nauluka. Adayenda mwaliŵiro ndi mphepo. Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake. M'kuŵala kumene kunali pamaso pake, munkafumira matalala ndi makala amoto, amene adabzola mitambo yophimba ija. Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka m'kati mwa matalala ndi makala amoto. Adaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa. Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Inu Chauta mudakhuluma mokalipa, pamene mudatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwanu. Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira, ndi kundivuula m'madzi ozama. Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane, pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine. Adaniwo adandithira nkhondo pamene ndinali m'mavuto, koma Chauta adandichirikiza. Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane. Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa. Chauta adandipatsa mphotho molingana ndi ntchito zanga zabwino, adandifupa molingana ndi ungwiro wanga. Ine ndidatsata njira za Chauta, sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga. Ndidamvera malangizo ake onse, ndipo malamulo ake sindidaŵataye. Ndinalibe mlandu pamaso pake, ndinkalewa zoipa m'moyo mwanga. Nchifukwa chake Chauta wandipatsa mphotho molingana ndi ntchito zanga zabwino, monga momwe akuwonera kuti ndilibe mlandu. Kwa anthu okhulupirika, Inu Mulungu mumadziwonetsa okhulupirika. Kwa anthu aungwiro, mumadziwonetsa abwino kotheratu. Kwa anthu oyera mtima mumadziwonetsa okoma mtima, koma kwa anthu oipa mtima, mumawonetsa kunyansidwa nawo. Paja anthu odzichepetsa, Inu mumaŵapulumutsa, koma anthu odzikuza mumaŵatsitsa. Ndithu, Inu mumayatsa nyale ya moyo wanga. Chauta, Mulungu wanga, amandiwunikira mu mdima. Ndi chithandizo chanu ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo. Ndi chithangato cha Mulungu, ndingathe kupambana. Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga.
Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu. Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima
Ukadamvera malamulo anga, bwenzi mtendere ukukufikira ngati madzi amumtsinje, ndipo bwenzi chilungamo chikukuphimba kosalekeza ngati mafunde apanyanja.
Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa. Tsogolo langa lili m'manja mwanu. Malire a malo anga andikhalira mwabwino. Inde, ndalandira madalitso abwino ndithu.
Mulungu ali m'kati mwa mzindawo, sudzaonongeka konse. Mulungu adzauthandiza dzuŵa lisanatuluke.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya. Anthu a Mulungu adzakhala m'midzi yamtendere, m'nyumba zokhulupirika, ndiponso m'malo ousira abata.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi. Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo, motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa. Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo.
Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati anthu amene akulota. Pamenepo tidasekera kwambiri, ndipo tidalulutira ndi chimwemwe. Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti, “Chauta waŵachitira zazikulu.” Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.
Anthu a Mulungu adzakhala m'midzi yamtendere, m'nyumba zokhulupirika, ndiponso m'malo ousira abata.
Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.
Akudalitseni Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kumwamba nkwa Chauta, koma dziko lapansi adapatsa anthu.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Mwana wanga, uvomere mau anga, ndi kusunga bwino malamulo anga. Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza. Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri, amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima. Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama. Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga. Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake. Pakuti nyumba yake imatsenderekera ku imfa, njira zake zimamufikitsa kwa anthu akufa. Opita kwa iye, palibe ndi mmodzi yemwe wobwerako, sazipezanso njira zopita ku moyo. Uzitchera khutu ku nzeru, uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu. Ndiye iwe, uzitsata njira za anthu abwino, uziyenda m'njira za anthu ochita chilungamo. Paja anthu olungama ndiwo adzakhale m'dziko, anthu okhulupirika ndiwo adzakhazikike m'menemo. Koma anthu oipa Mulungu adzaŵachotsa pa dziko, anthu onyenga adzaŵatulutsa m'dzikomo. Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu, ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu. Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika. Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta, udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu.
Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani? Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.
Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya. Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”