Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

74 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu Yauzimu

Ndikufuna ndikuuzeni kuti tifunika kusakasaka nthawi zonse kukhala pafupi ndi Mulungu, chifukwa pamenepo ndi pomwe timapeza mphamvu zatsopano zomwe timazifuna. Mulungu ndiye pothawirapo pathu, ndipo ngati pothawirapo polimba, amatiteteza ku ziwawa za mdani.

Nga mmene Paulo analili, ifenso tili ndi mphamvu yotithandiza ya Mulungu, imene imatitsitsimutsa ndi kutithandiza kukhala olimba mwa Iye. Pa nthawi ya mavuto aakulu ndi zolakwa, mudzaona mphamvu yodabwitsa ya Mulungu ikugwira ntchito mwa inu.

Mphamvu imeneyi siiyambira mwa inu, koma imachokera mwachindunji kwa Mzimu wa Atate wanu amene amakukondani kwambiri. Idzakuthandizani kuyenda m'moto osapsa, idzakupatsani mapazi olimba kuti muyende pamwamba, mapiko ngati a chiwombankhanga kuti musatope, ndi mphamvu ngati za njati kuti musagonje.

Anthu ambiri adzadabwa akaona kuonekera kwa Mulungu m'moyo wanu, popanda kuwauza momwe zinthu zakhalira; adzadziwa kuti mwapitiriza chifukwa cha chisomo ndi chikondi cha Yesu. Pamenepo, mudzatha kufotokoza zodabwitsa zake ndi kulengeza ntchito zake zazikulu, kukhala umboni wamoyo wa mphamvu ya Mulungu kwa onse amene akuzungulirani.


2 Akorinto 12:9

koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Habakuku 3:19

Ambuye anga, Chauta, ndiwo amandipatsa mphamvu. Amalimbitsa miyendo yanga kuti ikhale ngati ya mbaŵala, kuti ndikafike mpaka pamwamba pa phiri. Kwa Woimbitsa nyimbo. Aimbire zazingwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:29-31

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.

Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu.

Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa.

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:14

Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 6:27

“Iwe Yeremiya, ndakusankha kuti ukhale choyesera zitsulo. Uŵayese anthu anga kuti uwone m'mene aliri makhalidwe ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoweli 3:16

Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake amveka ngati bingu kuchokera ku Yerusalemu. Ndipo thambo ndi dziko lapansi zikugwedezeka. Koma Chauta ndiye pothaŵirapo anthu ake, ndiye linga lotetezera a ku Israele.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 144:2

Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:10

Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 22:33

Mulungu wathu ndiye linga langa lolimba, wandichotsera zoopsa m'njira zanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 2:18

Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuŵathandiza anthu amene amayesedwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 29:11

Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 22:2

Davideyo adaimbira Chauta nyimbo iyi yakuti, “Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 29:12

Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 22:3

Ndiye Mulungu wanga ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga. Ndiye linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndinu amene mumandiwombola pa nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:39

Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 32:17

“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 20:4

Chauta, Mulungu wanu, apita nanu Iye yemwe kuti akuthandizeni pa nkhondoyo ndipo kuti akupambanitseni.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 31:6

Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 4:18

“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 1:37

Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 59:17

Inu mphamvu zanga, ndidzakuimbirani nyimbo zokuyamikani, pakuti Inu Mulungu ndinu linga langa, ndinu Mulungu wondiwonetsa chikondi chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:19

Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 1:9

Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:2

Tcherani khutu kuti mundimve, fulumirani kudzandipulumutsa. Mukhale thanthwe langa lothaŵirako, ndi linga langa lolimba londipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 22:23

Ndidamvera malangizo ake onse, ndipo malamulo ake sindidaŵataye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 81:1

Kwezani mau kuimbira Mulungu amene ali mphamvu zathu. Fuulani ndi chimwemwe kwa Mulungu wa Yakobe.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 15:2

Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:29

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:2

Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 12:2

“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:2-3

Tcherani khutu kuti mundimve, fulumirani kudzandipulumutsa. Mukhale thanthwe langa lothaŵirako, ndi linga langa lolimba londipulumutsa.

Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo.

Atamandike Chauta: wandiwonetsa modabwitsa chikondi chake chosasinthika, pamene ndinali mu mzinda wozingidwa ndi gulu la ankhondo.

Ndidalankhula mwankhaŵa kuti, “Andipirikitsira kutali ndi Inu.” Koma Inu mudamva kupempha kwanga pamene ndidakudandaulirani kuti mundithandize.

Kondani Chauta, inu nonse anthu oyera mtima. Chauta amasunga anthu okhulupirika, koma amalanga koopsa anthu odzikuza.

Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta.

Zoonadi, ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Tsogolereni ndi kundiwongolera chifukwa Inu ndinu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:26

Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 28:7

Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 25:8

Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 16:11

Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake. Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 71:3

Mundikhalire thanthwe lothaŵirako, ndiponso linga lolimba lopulumukirako. Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:32-34

Mulungu wathu ndiye amene amandiveka mphamvu, wandichotsera zoopsa m'njira zanga.

Amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbaŵala, ndipo amandisunga bwino m'mapiri.

Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 11:34

ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 16:13

Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:10

Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:24

Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:37

Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 1:11

Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yaulemerero, kuti muzipirira zonse ndi mitima yoleza ndi yosangalala.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:3

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:10

Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 3:16

Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:4

Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:7

Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 24:10

Ukataya mtima pamene upeza zovuta, ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:28

Ndafookeratu ndi chisoni. Limbitseni monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:5-6

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye.

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 4:16

Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 3:14

Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:1-2

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake.

Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.

Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka.

Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.

Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.

Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.

Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha.

Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi.

Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho;

limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse,

Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1-3

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.

Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.

Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.

Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:6-7

Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye.

Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 11:28-30

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.

“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”

Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 143:10

Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu, pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:24

Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:1-2

Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga.

Adakwera pa mkerubi nauluka. Adayenda mwaliŵiro ndi mphepo.

Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake.

M'kuŵala kumene kunali pamaso pake, munkafumira matalala ndi makala amoto, amene adabzola mitambo yophimba ija.

Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka m'kati mwa matalala ndi makala amoto.

Adaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa.

Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Inu Chauta mudakhuluma mokalipa, pamene mudatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwanu.

Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira, ndi kundivuula m'madzi ozama.

Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane, pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine.

Adaniwo adandithira nkhondo pamene ndinali m'mavuto, koma Chauta adandichirikiza.

Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane.

Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:3-5

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira,

kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.

Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:22

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wachikondi ndi wokhulupirika! Ndabwera kwa Inu ndikudziwa kuti ndikukusowani, kuti popanda Inu ndilibe chifukwa chopitirira patsogolo ndikukhala wolimba, Ambuye Yesu Khristu, ndikusowa mphamvu zanu kuti ndipitirire, mphamvu zanga zatha. Ndikupemphani kuti mundinyamule ndikundithandiza kuti ndisatayike chikhulupiriro ndikupitirizabe kuyenda. Inu mwanena m'mawu anu: "Wofooka anene kuti ndili ndi mphamvu mwa Iye." Ambuye, ndine wopanda chuma, koma ndikutsimikiza kuti mphamvu zanga zimachokera kwa Inu. Lero ndikulengeza zomwe mawu anu amanena: "Amapatsa mphamvu wotopa, ndipo amachulukitsa mphamvu za wopanda mphamvu." Ndikupemphani kuti mundikonzere ngati chiwombankhanga kuti ndiwuluke ndikukwera kumwamba. M'dzina la Yesu. Ameni.