Mukayang'anitsitsa nkhani ya chikhalidwe cholimba mtima m’Baibulo, mukupeza nkhani zambiri zotilimbitsa mtima ndikutisonyeza tanthauzo leni la khalidweli. Baibulo limatiuza za amuna ndi akazi olimba mtima omwe, podalira Mulungu, anakumana ndi mavuto, n’kumenyana ndi zovuta, n’kudzuka molimba mtima poyesedwa.
Chitsanzo chimodzi chodziwika bwino cha chikhalidwe cholimba mtima m’Baibulo ndi nkhani ya Davide ndi Goliyati. Davide, mbusa wachinyamata, anali ndi mtima wolimbana ndi chimphona champhamvu chokongoletsedwa ndi zida, ngakhale kuti ananyozedwa ndi ena, Davide anadalira Mulungu ndipo analimba mtima kukumana ndi mdani wake. Chilimbikitso chake ndi chikhulupiriro chake mwa Mulungu chinapatsidwa mphoto, ndipo ena anadabwa ndi chipambano chake.
Kukhala wolimba mtima kumatanthauza kudalira Mulungu ndikuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake, ngakhale pamene zopinga zikuoneka zosagonjetseka. Sikuti kungowonetsa mphamvu zakuthupi kapena kulimba mtima, koma kukhala ndi chikhulupiriro ndi chitsimikizo chakuti Mulungu ali nafe pa sitepu iliyonse ya ulendo wathu.
Mzimu Woyera umatipatsa chilimbikitso, umatiphunzitsa kuti sitili tokha ndi kuti Mulungu amatilimbitsa kuti tithe kukumana ndi vuto lililonse, ngakhale litaoneka lovuta bwanji.
Tikamaganizira za chikhalidwe cholimba mtima, tiyenera kukumbukira kuti tikuyenera kukhala olimba mtima m’chikhulupiriro chathu mwa Mulungu ndi m’zochita zathu. Nthawi zina, tidzakumana ndi mavuto ndi zovuta zomwe zidzayesa kulimba mtima kwathu. Komabe, tingapeze chitonthozo m’mawu a Yoswa 1:9: “Taona, ndikulamula kuti ukhale wolimba mtima ndi wamphamvu; usachite mantha kapena kutaya mtima, pakuti Yehova Mulungu wako adzakhala nawe kulikonse kumene ukupita.”
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Tsono Davide adauza mwana wake Solomoni kuti, “Khala wamphamvu ndipo uchite zimenezo molimba mtima. Usaope, usataye mtima, pakuti Chauta Mulungu wanga ali nawe. Sadzaleka kukusamala ndipo sadzakusiya pa ntchito zonse za Nyumba ya Chautazi.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Koma ophunzira aja, pomuwona akuyenda pa madzi, adaaganiza kuti ndi mzukwa, nayamba kukuwa. Motero sadathe kuchita zinthu zamphamvu kumeneko. Adangosanjika manja pa odwala oŵerengeka, nkuŵachiritsa. Onsewotu atamuwona adaaopsedwa. Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine, musaope.”
Komatu ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti usunge malamulo onse amene Mose mtumiki wanga adakupatsa. Usatayepo ndi kagawo kamodzi komwe, ndipo kulikonse kumene udzapite, udzapambana.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha. Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiŵatiŵa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiŵapatse madzi anthu anga osankhidwa. Amenewo ndi anthu amene ndidadzilengera, ndipo azindiimbira nyimbo zotamanda Ine.” Chauta akuti, “Koma simudapemphere kwa Ine, inu am'banja la Yakobe, mudatopa nane, inu Aisraele. Simudadzatule kwa Ine nkhosa kuti zikhale zopereka zopsereza, simudandilemekeze ndi nsembe zanu. Sindidakulemetseni pomakupemphani zopereka zanu, sindidakutopetseni pomakupemphani lubani. Simudandigulire bango lonunkhira, simudandipatse mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma m'malo mwake inu mwanditopetsa ndi machimo anu, mwandilemetsa ndi zolakwa zanu. “Ine, Ineyo ndithu, ndine amene ndimafafaniza machimo anu, kuti ulemerero wanga uwoneke. Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu. Mundikumbutse zakale, titsutsane. Mufotokoze mlandu wanu kuwonetsa kuti simudalakwe. Atate anu oyamba adachimwa, atsogoleri anu aja adandilakwira. Mafumu anu adaipitsa malo anga opatulika. Nchifukwa chake ndidalola kuti banja la Yakobe liwonongedwe, ndidalola kuti Aisraele anyozedwe.” Pajatu Ine ndine Chauta, Mulungu wako. Ndine Woyera uja wa Israele, Mpulumutsi wako. Ndidzapereka Ejipito pofuna kuwombola iwe. Ndidzapereka Etiopiya ndi Seba m'malo mwa iwe.
Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”
Musaŵaope anthu ameneŵa. Chauta Mulungu wanu ali nanu. Iyeyo ndiye Mulungu wamkulu woyeneradi kumuwopa.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Ndi chithandizo chanu ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo. Ndi chithangato cha Mulungu, ndingathe kupambana.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
“Imvani anthu anga, Ine ndidzalankhula. Ndidzapereka umboni wokutsutsani inu Aisraele. Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,
Koma inu limbani mtima, manja anu asafooke chifukwa mudzalandira mphotho ya ntchito yanu.”
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Limba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.”
Chauta, Mulungu wanu, apita nanu Iye yemwe kuti akuthandizeni pa nkhondoyo ndipo kuti akupambanitseni.”
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Ukadzamvera mosamala malamulo ndi malangizo amene Chauta adalamula Mose kuti auze Aisraele, ndiye kuti zinthu zidzakuyendera bwino. Khala wamphamvu, limba mtima, usati uziwopa, usatinso ude nkhaŵa.
Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.
Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Koma Davide adauza Mfilistiyo kuti, “Wadza kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo. Koma ine ndikudza kwa iwe m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa magulu ankhondo a Aisraele, amene iwe wamunyoza. Lero lomwe lino Chauta akupereka m'manja mwanga. Ndikulasa ndi kukugwetsa pansi, ndipo ndikudula mutu. Mitembo ya magulu ankhondo a Afilisti ndiipereka lero lino kwa mbalame zamumlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo, kuti dziko lonse lapansi lidziŵe kuti kuli Mulungu ku dziko la Israele. Anthu onse amene asonkhanaŵa adzadziŵa kuti Chauta sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo wokha. Wopambanitsa pa nkhondo ndi Chauta, ndipo akuperekani m'manja mwathu.”
Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima. Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Woipa mtima amangodzithaŵira popanda wina wompirikitsa, koma wochita zabwino amalimba mtima ngati mkango.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
“Khalani amphamvu, limbani mtima. Musati muwope kapena kutaya mtima pamaso pa mfumu ya ku Asiriya ndi chigulu chankhondo chimene ali nachochi.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
“Ine ndi ulendo uno, nchifukwa chake tsono khala wamphamvu ndipo ulimbike mtima. Ndipo maiyo adati, “Ndikufuna kukupemphani kanthu kakang'ono. Chonde musandikanize.” Tsono mfumu idauza mai wakeyo kuti, “Pemphani chimene mukufuna, mai wanga, sindikukanizani.” Maiyo adati, “Mulole kuti Abisagi Msunamu uja apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu, kuti akhale mkazi wake.” Mfumu Solomoni adafunsa mai wakeyo kuti, “Chifukwa chiyani mukumpemphera Abisagi Msunamu Adoniyayu? Mpemphereninso ndi ufumu womwe, poti iyeyu ndi mkulu wanga, ndipo akugwirizana ndi wansembe Abiyatara ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya.” Pomwepo mfumu Solomoni adalumbira m'dzina la Chauta kuti, “Mulungu andilange koopsa ngati Adoniya saphedwa chifukwa cha zimenezi. Nchifukwa chake, pali Chauta wamoyo, amene adandisankhula ndi kundikhazika pa mpando waufumu wa Davide bambo wanga, nandipatsa ufumuwu monga momwe adalonjezera, Adoniya aphedwa ndithu lero lomwe lino.” Choncho mfumu Solomoni adatuma Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye adakamkantha Adoniyayo, naafa. Tsono mfumu idauza wansembe Abiyatara kuti, “Pita ku Anatoti ku minda yako. Uyenera kufa ndithu, koma sindikupha tsopano lino ai, chifukwa udasunga Bokosi lachipangano la Chauta pamaso pa Davide bambo wanga, ndiponso poti udazunzika naye limodzi bambo wanga.” Choncho Solomoni adachotsa Abiyatara pa ntchito yokhala wansembe wa Chauta. Motero zidachitikadi zija adaanena Chautazi za banja la Eli ku Silo. Pamene Yowabu adamva zimenezi, adathaŵira ku hema lopatulika la Chauta nakagwira nsonga za guwa lansembe. Yowabu ndiye uja ankathandiza Adoniya koma osati Abisalomu. Tsono Mfumu Solomoni atamva kuti Yowabu wathaŵira ku hema la Chauta, ndipo kuti wakhala pambali pa guwa lansembe, adatuma Benaya mwana wa Yehoyada namuuza kuti, “Pita, ukamuphe.” Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.
Tsono Chauta adauza Yoswa, mwana wa Nuni, kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Udzaŵatsogolera Aisraele kukaloŵa m'dziko lomwe ndidaŵalonjeza. Ndipo ndidzakhala nawe.”
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
“Mverani, inu amene mukudziŵa chilungamo, inu amene mukusunga malamulo anga mumtima mwanu. Musachite mantha anthu akamakudzudzulani, musataye mtima akamakulalatirani.
Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza, amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga kumenya nkhondo.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zoŵaŵa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthaŵi. Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.
Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga.
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.
Usamaopa zoopsa zobwera modzidzimutsa, usamachita mantha ndi tsoka lodzagwera anthu oipa. Chauta ndiye adzakhale chikhulupiriro chako, adzasunga phazi lako kuti lingakodwe.
Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye. “Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha? Mulungu wathu ndiye linga langa lolimba, wandichotsera zoopsa m'njira zanga.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Inu adani athu musatiseke. Tidagwa inde, koma tidzadzukanso. Ngakhale tikhale mu mdima, Chauta ndiye nyale yathu.
Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu.
Sikudzafunika kuti mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale m'malo mwanu, mungoima, ndipo muwonerere Chauta akukumenyerani nkhondo, inu anthu a ku Yuda ndi inu anthu a mu Yerusalemu.’ Musaope ndipo musataye mtima, mutuluke maŵa mukalimbane nawo, Chauta adzakhala nanu.”
Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu. Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziŵa kuti sadzandichititsa manyazi.
Musaŵaope, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaponye nkhondo pamodzi nanu.”
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Ena amatamira magaleta ankhondo, ena amadalira akavalo, koma ife timatamira dzina la Chauta, Mulungu wathu, timamutama Iyeyo mopemba.
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.”
Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye.
Mundichitire chifundo Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti mtima wanga ukudalira Inu. Ndidzathaŵira pansi pa mapiko anu, mpaka chiwonongeko chitandipitirira.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu. Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza.