Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

142 Mauthenga a M'Baibulo Okukhozera Banja


Aefeso 5:25

Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:18-21

Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye.

Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaƔavutitse ai.

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.

Inu atate, musamaƔapsetsa mtima ana anu, kuti angataye mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:8

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 127:3-5

Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake.

Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo.

Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 133:1

Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale!

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 2:24

Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aƔiriwo amakhala thupi limodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 1:8-9

Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.

Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluƔa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:4-7

Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza.

Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaƔa.

Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona.

Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaƔi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 128:1-4

Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake.

Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako.

Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:14

Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:19

Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 19:6

Choncho tsopano salinso aĆ”iri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:4

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaƔalanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:18

Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:13

Anthu ako ndidzaƔaphunzitsa ndekha, Ine Chauta, ana ako ndidzaƔadalitsa ndi kuƔapatsa mtendere waukulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 17:17

Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaƔi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:1-3

Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera.

Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.

Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.

Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu.

NthaƔi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.

Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.

Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaƔi zonse. NthaƔi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.

Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziƔitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima.

Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo.

Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira.

Tikiko adzakudziƔitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye.

Ndikumtuma kwa inu kuti mudziƔe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima.

Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro.

Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aƔadalitse.

Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:17

Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 5:8

Ngati wina aliyense saƔapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:7

“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:5-6

Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naƔalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,

akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:2-3

Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaƔi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,

Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai,

ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu.

Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga.

Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano.

Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.

Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu.

Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuƔa likuloƔereni muli chikwiyire.

Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.

Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoƔa.

M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.

ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:2

Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:25

NkhaƔa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:29

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaƔaonjezera mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:10

Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaƔi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maƔa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 18:19

Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:24

Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:9

Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. NdikudziƔa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:20

Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:27

Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuƔagwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaƔi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloƔera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 18:19-20

“Ndikunenetsanso kuti aĆ”iri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani.

Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao,

Pajatu pamene aĆ”iri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:1-2

Chimodzimodzinso inu azimai, muzimvera amuna anu, kuti ngati ena mwa iwo samvera mau a Mulungu, azikopeka ndi makhalidwe a akazi aonu. Sipadzafunikanso kunenerera mau,

Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.

Alewe zoipa, azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza.

Paja Ambuye amaĆ”ayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saĆ”ayang'ana bwino.”

Ndani angakuchiteni choipa ngati muchita changu pa zabwino?

Koma ngakhale mumve zoƔaƔa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaƔi iliyonse kuƔayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao.

Nkwabwino kumva zoƔaƔa chifukwa chochita zabwino, ngati Mulungu wafuna choncho, koposa kumva zoƔaƔa chifukwa chochita zoipa.

Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.

Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m'ndende.

popeza kuti adzadziwonera okha makhalidwe anu aulemu ndi angwiro.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:4

Inu atate, musamaƔapsetsa mtima ana anu, koma muziƔalera bwino pakuƔasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:6

Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:18

Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,

kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 133:1-3

Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale!

Ndi ngati mafuta amtengowapatali oƔathira pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aroni, oyenderera mpaka ku khosi la mkanjo wake.

Ndi ngati mame a ku Heremoni, omatsikira ku mapiri a Ziyoni. Ku Ziyoni Chauta amaperekako madalitso, ndiye kuti moyo wamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 1:10

Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuƔakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziƔa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1-3

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.

Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.

Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.

Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:33

Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaĆ”atsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaĆ”apambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:23-24

Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.

Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:3

Ndimayamika Mulungu wanga nthaƔi zonse ndikamakukumbukirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:12

Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:1

Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 16:14

Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:5

Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:18

Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:1

Pitirizani kukondana monga abale.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:24

Mau okometsera ali ngati chisa cha uchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:4-5

MundidziƔitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu.

Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:11

Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:21

Inu amene mumaopa Khristu, muzimverana.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiƔale malangizo angaƔa, koma mtima wako usunge malamulo anga.

Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo.

Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake.

Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.

Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe.

Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo.

Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu.

Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha.

Nzeru ili ngati mtengo woƔapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika.

Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino.

Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaƔi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:10-11

KanthaƔi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo.

Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:16

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuƔala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:2

Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:19

Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaƔa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoƔani, ndipo nthaƔi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.

Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:14

Ndi wodala munthu amene amaopa Chauta nthaƔi zonse, koma woumitsa mtima wake adzagwa m'tsoka.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:18-19

UƔalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaƔana zinthu zao ndi anzao.

Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaƔathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:1-2

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.

Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.

Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta.

Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.

Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaƔachitira chifundo omulemekeza.

AmadziƔa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi.

Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duƔa lakuthengo.

Koma mphepo ikaombapo, duƔalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake.

Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.

Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.

Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiƔale zabwino zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:32

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:14

Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:114

Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:1

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muƔachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 31:49

Labani adanenanso kuti, “Chauta atiyang'anire ife tonse aĆ”iri pamene tikulekana. Motero malowo adaĆ”atcha Mizipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 128:5

Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse. Uwone m'mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendere bwino masiku onse a moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:2

Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaƔi ake sadzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 1:5

Ndi oti wanzeru akaƔamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:5-6

Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.

Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako, ndipo kulungama kwako kudzaƔala ngati usana.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:12

Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:14-15

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaƔala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 113:9

Amapatsa banja mkazi wosabala, namsandutsa mai wosangalala wa ana. Tamandani Chauta!

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 30:5

Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaƔira kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:1

Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 40:1-3

Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. AdaƔeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga.

Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. SindidaƔabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu.

Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaƔi zonse.

Mavuto osaƔerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu.

Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza.

Anthu ofunafuna moyo wanga, muƔachititse manyazi ndi kuƔasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa.

Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera.

Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!”

Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoƔa, koma simunandiiƔale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza.

Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe.

Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:4

Ngodala anthu amene akumva chisoni, pakuti Mulungu adzaƔasangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:14-15

Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:24

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:10

Amene amadziƔa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuƔasiya anthu okufunitsitsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:15

Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:8

Mau otsiriza ndi aƔa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 31:10-31

Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali.

Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoƔa phindu.

Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa.

Amanka nafunafuna ubweya ndi thonje, ndipo amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.

Ali ngati zombo za anthu amalonda, zakudya zake amakazitenga kutali.

Amadzuka usikusiku nkuyamba kukonzera chakudya anthu a pabanja pake, ndi kuƔagaƔira ntchito adzakazi ake.

Amalingalira za munda, naugula. Amalima munda wamphesa ndi ndalama zozipeza ndi manja ake.

Amavala dzilimbe ndipo sachita manja khoba pogwira ntchito.

Amazindikira kuti malonda ake ndi aphindu, choncho nyale yake sizima usiku wonse.

Thonje amadzilukira yekha, ndipo nsalu amadziwombera yekha.

Nchiyani, mwana wanga? Nchiyani, mwana wa m'mimba mwanga? Nchiyani, mwana wanga amene ndidachita kukupempha polonjeza ndi malumbiro?

Anthu osauka amaƔachitira chifundo, amphaƔi amaƔapatsa chithandizo.

A pabanja pake saƔaopera kuti nkufa nacho chisanu, poti amadziƔa kuti onsewo amavala zovala zofunda.

Amadzipangira yekha zofunda, ndipo iye amavala zovala zabafuta ndi za mtengo wapatali.

Mwamuna wake ndi wodziƔika ndithu ku mabwalo, akakhala pakati pa akuluakulu a dziko.

Mkazi ameneyu amasoka zovala za nsalu yabafuta, nazigulitsa, amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.

Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake. Amaganiza zakutsogolo mosangalala.

Amalankhula mwanzeru, ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma.

Amayang'anira makhalidwe a anthu a pabanja pake, ndipo sachita ulesi mpang'ono pomwe.

Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati,

“Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.”

Mphamvu zako usathere pa akazi, usamayenda nawo ameneƔa, amaononga ndi mafumu omwe.

Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.

Muzimlemekeza chifukwa cha zochita zake, ntchito zake zizimpatsa ulemu ku mabwalo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:28

Ndipo tikudziƔa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziƔakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaƔaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:19

Pamene nkhaƔa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 19:14

Koma Yesu adati, “Alekeni anaĆ”a azibwera kwa Ine, musaĆ”aletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:10-11

Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:30

Maso okondwa amasangalatsa mtima, ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 12:2

“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:8

NthaƔi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 9:7

Tsopano mubalane, kuti zidzukulu zanu zidzachulukane ndi kudzabalalika pa dziko lonse lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:13

Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuƔala kwa amoyo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 1:5

Cholinga changa pokupatsa malangizo ameneƔa, nchakuti pakhale chikondi chochokera mu mtima woyera, mu mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndiponso m'chikhulupiriro chopanda chiphamaso.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:8

Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:1

Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziƔira zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:3

Wandituma kuti ndiƔakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiƔapatse maluƔa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiƔapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiƔapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 40:5

Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziƔerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:37

Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:19-21

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba.

“Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. IwoĆ”a amachita zimenezi kuti anthu aĆ”atame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.

Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba.

Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:3

ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:29

Anthu a Mulungu adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala m'menemo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:1-2

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaƔi zonse.

Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoƔa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.

Pemphani Mulungu kuti aƔadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aƔadalitse, osaƔatemberera ai.

Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira.

Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.

Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino.

Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uĆ”alange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. NdidzaĆ”alanga ndine, akutero Chauta.”

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziƔa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 5:14-15

Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.

Ndipo ngati tikudziƔa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziƔanso kuti talandiradi zimene tampempha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:1-2

Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.

Amene amadziƔa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuƔasiya anthu okufunitsitsani.

Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse.

Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oƔazunzawo.

Mundikomere mtima, Inu Chauta. Onani m'mene akundisautsira anthu ondida. Inu mumandipulumutsa ku imfa,

kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse, pakati pa anthu anu a mu Ziyoni. Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa.

Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe. Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika wotcha iwo omwe.

Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe.

Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu.

Koma anthu aumphaƔi Mulungu saƔaiƔala nthaƔi zonse, anthu osauka Mulungu saƔagwiritsa mwala mpang'ono pomwe.

Dzambatukani, Inu Chauta, munthu asakunyozeni. Azengeni mlandu anthu akunja.

Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:10

Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaƔiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:11-12

Sindikunena zimenezi modandaula kuti ndikusoƔa kanthu, pakuti ine ndaphunzira kukhutira ndi zimene ndili nazo.

Kukhala wosauka ndimakudziƔa, kukhala wolemera ndimakudziƔanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoƔeratu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:5

Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:1

Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziƔa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:10

Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:25

Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaƔira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaƔi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31-32

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:1-2

Pitirizani kukondana monga abale.

Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo.

Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloƔa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa.

Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake.

Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi.

Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza.

Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.

Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.

Muzimvera atsogoleri anu ndi kuƔagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. MukaƔamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.

Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo.

Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga.

Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:19

Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:137

Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:7

Tulani pa Iye nkhaƔa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:13

Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoƔa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo