Lero ndikufuna ndikukumbutse kuti Mulungu amakupatsa mphamvu zokumana ndi vuto lililonse lovuta. Nthawi zambiri timaganiza kuti mavuto akabwera sitikonzeka kulimbana nawo, koma ukunama, Mulungu nthawi zonse amatikonzekeretsa. Mawu ake amati Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha, koma wa mphamvu, chikondi ndi kudziletsa. Choncho limbika mtima, Mulungu ali nawe, akulimbana nkhondo zako zonse.
Gwiritsa ntchito zipangizo zimene Mulungu anakupatsa kudzera m'mawu ake ndi mzimu wake woyera. Khala wolimba mtima, pita patsogolo molimba mtima komanso modzidalira. “Limbikani mtima, mukhale amphamvu, nonsenu inu akuyembekezera Yehova.” (Masalimo 31:24) Choncho limbika mtima, Mulungu sanama.
Mulungu ndiye mphamvu yako, ndiye wokulanditsa wako, ndiye mthandizi wako, ndiye chishango chako, ndiye pothawirapo pako, khulupirira Atate wako wakumwamba, zonse zidzakhala bwino. “Mulungu ndiye amene amandipatsa mphamvu; Mulungu ndiye amene anwongola njira yanga.” (2 Samueli 22:33)
“Pa mavuto ngati ameneŵa pafunika abwenzi okhulupirika, kuwopa kuti mwina mwake munthu angasiyane ndi Mphambe.
Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu.
Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.
Kukhala aŵiri nkwabwino koposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu aŵiri ili ndi phindu lopambana.
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la atate ako. Usachite kupita ku nyumba ya mbale wake, ukakhala pa mavuto. Mnzako wokhala naye pafupi amaposa mbale wako wokhala kutali.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, koma kukoma kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene ndikulamulani.
Sindikutchulaninso antchito ai, pakuti wantchito sadziŵa zimene mbuye wake akuchita. Koma ndikukutchulani abwenzi, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziŵitsani.
Aŵiriwo akagwa, wina adzautsa mnzake. Koma tsoka amene ali yekha: akagwa, ndiye kuti zavuta, chifukwa palibe wina womuutsa.
Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.
Nkotheka kuti munthu apambane mnzake amene ali yekha, koma pakakhala aŵiri, iwoŵa adzalimbana naye. Chingwe cha nkhosi zitatu sichidukirapo.
Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.
Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Munthu wochita zabwino amatsogolera anzake pa njira yokhoza, koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa.
Tsono abwenzi ake a Yobe, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki, ndi Zofari wa ku Naama, adazimva za masoka onseŵa amene adamgwera. Ndiye tsiku lina anthu atatuwo adabwera, aliyense kuchokera kwao. Onsewo anali atapangana za nthaŵi yoti adzampepese ndi kudzamsangulutsa.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo, koma akatsitsa pansi manja, Aamaleke ankapambana.
Tsono manja a Mose atatopa, Aroni pamodzi ndi Huri uja adatenga mwala namkhazikira Mose kuti akhalepo. Aŵiriwo adakhala wina uku wina uku, atagwirira manja a Mose aja. Adaŵagwirira ndithu mpaka dzuŵa kuloŵa.
Motero zidachitikadi zimene Malembo adaanena, kuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, nchifukwa chake Mulungu adamuwona kuti ngwolungama;” mwakuti ankatchedwa bwenzi la Mulungu.
Kunyumba kwa mnzako uzipitako kamodzikamodzi, kuwopa kuti angatope nawe, nkuyamba kudana nawe.
Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali,
kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake, ndi kukodwa mu msampha.
Choncho Chauta ankalankhula ndi Mose pamasompamaso, monga momwe munthu amalankhulira ndi bwenzi lake. Tsono pambuyo pake Mose ankabwerera kumahema komweko. Koma mnyamata wina, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, amene anali mtumiki wa Mose, sankachoka kuchihemako.
Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko.
“Saulo ndi Yonatani pa moyo wao anali okondedwa ndi okondwetsa, ndipo sadalekane ali moyo ngakhale pa imfa. Anali ndi liŵiro loposa la ziwombankhanga. Anali amphamvu kuposa mikango.
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.
Ndipo wina akadzafunsa kuti, ‘Nanga zilonda zili kumsana kwakozi, udatani?’ Iye adzati, ‘Zilondazi ndidazilandira m'nyumba mwa abwenzi anga.’ ”
Davide atatha kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani udagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani adakonda Davideyo monga momwe ankadzikondera iye mwini.
Apo Yonatani adalumbiritsanso Davide kuti asaleke kumkonda, pakuti Yonatani ankakonda Davide monga momwe ankadzikondera iye mwini.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani.
Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu.
Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa.
Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye, ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.
Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?
Ngakhalenso bwenzi langa lapamtima amene ndinkamkhulupirira, amene ankadya nane pamodzi, wandiwukira.
Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa wozoloŵerana naye, ndi amene ukuchita zimenezi.
Tinkakambirana nkhani zokoma tili aŵiri, tinkapembedza limodzi m'Nyumba ya Mulungu.
Davide atatha kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani udagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani adakonda Davideyo monga momwe ankadzikondera iye mwini.
M'maŵa mwake mzimu woipa uja udamtsikira Saulo, ndipo adayamba kubwebweta moyaluka m'nyumba mwake. Davide ankamuimbira zeze, monga momwe ankachitira tsiku ndi tsiku. Saulo anali ndi mkondo m'manja mwake.
Tsono adaponya mkondowo ndipo mumtima mwake adati, “Ndimubaya ndi kumkhomera ku chipupa.” Koma Davide adauleŵa. Zidachitika kaŵiri konse.
Pambuyo pake Saulo adayamba kuwopa Davide, chifukwa choti tsopano Chauta anali ndi Davide, kumsiya iyeyo.
Motero Saulo adamtuma Davide kwina kwake, ndipo adamuika kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Davide ankapita namabwera akuŵatsogolera.
Ndipo ankapambana pa zonse zimene ankachita, chifukwa Chauta anali naye.
Tsono pamene Saulo adaona kuti Davide akupambana kwambiri, adayamba kuchita naye mantha.
Koma anthu onse a ku Israele ndi a ku Yuda ankamkonda Davide, chifukwa iyeyu ankaŵatsogolera namapambana pa zonse.
Tsiku lina Saulo adauza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkulu. Ndidzakupatsa kuti akhale mkazi wako. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Chauta.” Potero Saulo ankaganiza kuti, “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisti.”
Tsono Davide adafunsa Saulo kuti, “Kodi ine ndine yani, ndipo abale anga ndi banja la bambo wanga ndife yani m'dziko la Israele, kuti ine nkukhala mkamwini wa mfumu?”
Koma pa nthaŵi yoti Merabi, mwana wa Saulo, akwatiwe ndi Davide, bambo wake adampereka kwa Adriyele Mmehola, kuti akhale mkazi wake.
Mwakuti adamtenga Davideyo tsiku lomwelo, osamlola kuti abwerere ku banja kwa bambo wake.
Komabe Mikala, mwana wina wamkazi wa Saulo, ankakonda Davide. Saulo atamva, adakondwa kwambiri.
Adaganiza kuti, “Ndimpatse amkwatire, kuti adzakhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo Afilisti adzamupha.” Nchifukwa chake Saulo adauza Davide kachiŵiri kuti, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.”
Motero adalamula nduna zake kuti, “Mulankhule naye Davide pambali nkumuuza kuti, ‘Mfumu imakukonda, ndipo ngakhale nduna zake zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ”
Nduna za Saulo zidamuuza Davide mau amenewo. Koma iye adati, “Kani mukuchiyesa chinthu chapafupi kukhala mkamwini wa mfumu? Kodi simukuwona kuti ndine wosauka ndi wosatchuka?”
Nduna za Saulo zidamuuza zonse zimene Davide adaanena.
Tsono Saulo adati, “Kamuuzeni kuti, sindikufuna chiwongo cha mtundu uliwonse ai, ndingofuna timakungu ta nsonga za mavalo a Afilisti 100, kuti ndilipsire adani anga.” Potero Saulo ankaganiza zoti Davide aphedwe ndi Afilisti.
Ndiye nduna za Saulozo zitamuuza Davide mau ameneŵa, zidamkondweretsa kuti akhale mkamwini wa mfumu. Nthaŵi yoti atenge mkazi wake isanakwane,
Davide adanyamuka napita pamodzi ndi ankhondo ake, ndipo adakapha Afilisti 200. Adabwera nato timakungu tija natipereka kwa mfumu, kuti choncho akhale mkamwini wake. Apo Saulo adapatsa Davideyo mwana wake Mikala, kuti akhale mkazi wake.
Koma Saulo atazindikira kuti Chauta ali naye Davide, ndiponso kuti mwana wake Mikala ankamkonda Davideyo,
adamuwopabe kwambiri ndi kudana naye moyo wake wonse.
Adachita naye chipangano chifukwa ankamkonda monga momwe ankadzikondera iye mwini.
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni.
Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza,
Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.
Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.
Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,
pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.
Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu.
Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi.
Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko.
Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Ambuye achitire chifundo banja la Onesifore, chifukwa iye ankandisangulutsa kaŵirikaŵiri. Sankachita nane manyazi, ngakhale ndinali womangidwa ndi unyolo:
adangoti atafika ku Roma, nkuyamba kundifunafuna mwachangu, mpaka adandipeza.
Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Mulungu pa tsiku la chiweruzo. Ukudziŵa bwino ndi iwe wemwe kuti adandithandiza kwambiri ku Efeso.
Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
Lewa kupsa mtima ndi kukwiya. Usachite zimenezi, pakuti sudzapindula nazo kanthu.
Pajatu anthu oipa adzaonongeka, koma okhulupirira Chauta adzalandira dziko kuti likhale lao.
Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha.
Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
Thupitu si chiwalo chimodzi chokha ai, koma lili ndi ziwalo zambiri.
Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni.
Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu, koma amalemekeza anthu omvera Chauta. Ndi amene amachitadi zimene walonjeza, ngakhale zikhale zoŵaŵa chotani.
Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,
Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai,
ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu.
Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga.
Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano.
Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.
Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu.
Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire.
Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.
Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.