Masalimo 128:1 - Buku Lopatulika Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake. |
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.
Pamenepo ndipo Mpingo wa mu Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.
Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.