Masalimo 122 - Buku LopatulikaApempherera mtendere wa Yerusalemu Nyimbo yokwerera; ya Davide. 1 Ndinakondwera m'mene ananena nane, Tiyeni kunyumba ya Yehova. 2 Mapazi athu alinkuima m'zipata zanu, Yerusalemu 3 Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda woundana bwino: 4 Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova. 5 Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo, mipando ya nyumba ya Davide. 6 Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu. 7 M'linga mwako mukhale mtendere, m'nyumba za mafumu mukhale phindu. 8 Chifukwa cha abale anga ndi mabwenzi anga, ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu. 9 Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu ndidzakufunira zokoma. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi