Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 124:1 - Buku Lopatulika

1 Akadapanda kukhala nafe Yehova, anene tsono Israele;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Akadapanda kukhala nafe Yehova, anene tsono Israele;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta akadapanda kukhala pa mbali yathu, Israele anene choncho tsopano,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 124:1
27 Mawu Ofanana  

Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.


Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.


Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?


Ndinakondwera m'mene ananena nane, Tiyeni kunyumba ya Yehova.


Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba.


Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.


Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota.


Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.


Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake.


Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;


M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova.


Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa.


Yehova, kumbukirani Davide kuzunzika kwake konse.


Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!


Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.


Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga, Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.


Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, mwa Yehova ndidzalemekeza mau ake.


Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.


Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova, moyo wanga ukadakhala kuli chete.


Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa