Masalimo 124 - Buku LopatulikaMulungu yekha walanditsa anthu ake Nyimbo yokwerera; ya Davide. 1 Akadapanda kukhala nafe Yehova, anene tsono Israele; 2 Akadapanda kukhala nafe Yehova, pakutiukira anthu: 3 Akadatimeza amoyo, potipsera mtima wao. 4 Akadatimiza madziwo, mtsinje ukadapita pa moyo wathu; 5 madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu. 6 Alemekezedwe Yehova, amene sanatipereke kumano kwao tikhale chakudya chao. 7 Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi; msampha unathyoka ndi ife tinaonjoka. 8 Thandizo lathu lili m'dzina la Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi