Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 124:4 - Buku Lopatulika

4 Akadatimiza madziwo, mtsinje ukadapita pa moyo wathu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Akadatimiza madziwo, mtsinje ukadapita pa moyo wathu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 bwenzi chigumula chitatisesa, madzi amkokomo atatikokolola,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 124:4
17 Mawu Ofanana  

kapena mdima kuti ungaone, ndi madzi aunyinji akumiza.


Tulutsani manja anu kuchokera m'mwamba; ndikwatuleni ndi kundilanditsa kumadzi aakulu, kudzanja la alendo;


Zingwe za imfa zinandizinga, ndipo mitsinje ya zopanda pake inandiopsa.


Zingwe za manda zindizinga, misampha ya imfa inandifikira ine.


Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu, pa nthawi ya kupeza Inu; indetu pakusefuka madzi aakulu sadzamfikira iye.


Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.


Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.


Chigumula chisandifotsere, ndipo chakuya chisandimize; ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje.


Ndamira m'thope lozama, lopanda poponderapo; ndalowa m'madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza.


Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati chimphepo cha matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu.


Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.


Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pamadzi ambiri,


Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa