Masalimo 123 - Buku LopatulikaPemphero la wonyozedwa Nyimbo yokwerera. 1 Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba. 2 Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo. 3 Mutichitire chifundo, Yehova, mutichitire chifundo; pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo. 4 Moyo wathu wakhuta ndithu ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu, ndi mnyozo wa odzikuza. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi