Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 123:1 - Buku Lopatulika

1 Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndikukweza maso anga kwa Inu, Inu amene mumakhala pa mpando wachifumu kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 123:1
25 Mawu Ofanana  

Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.


Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.


Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; achita chilichonse chimkonda.


Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.


Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?


Ndinakondwera m'mene ananena nane, Tiyeni kunyumba ya Yehova.


Akadapanda kukhala nafe Yehova, anene tsono Israele;


Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.


Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota.


Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.


Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake.


Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;


M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova.


Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa.


Yehova, kumbukirani Davide kuzunzika kwake konse.


Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!


Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.


Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye; ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga.


Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza.


Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka; pakuti Iye adzaonjola mapazi anga mu ukonde.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?


Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.


Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa