Masalimo 123:2 - Buku Lopatulika2 Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la mbuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Monga momwe anyamata amayang'anira ku dzanja la bwana wao, monga momwe adzakazi amayang'anira ku dzanja la dona wao, ndi momwenso timayang'anira ife kwa Chauta Mulungu wathu, mpaka atatichitira chifundo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo. Onani mutuwo |