Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 127 - Buku Lopatulika


Madalitso onse, a m'banja omwe, achokera kwa Mulungu
Nyimbo yokwerera; ya Solomoni.

1 Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.

2 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.

3 Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

4 Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona.

5 Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa