Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 127:2 - Buku Lopatulika

2 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa ndi kukagona mochedwa, kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya. Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao iwowo ali m'tulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa ndi kusagona msanga madzulo, kuvutikira chakudya choti mudye, pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 127:2
17 Mawu Ofanana  

Ndipo udzalimbika mtima popeza pali chiyembekezo; nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka.


Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo; ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza.


Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.


Kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.


Madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.


Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.


Ntchito zake zonse munthu angogwirira m'kamwa mwake, koma mtima wake sukhuta.


Pamenepo ndinauka, ndinaona; ndipo tulo tanga tinandizunira ine.


Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa