Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

135 Mauthenga a Mulungu Okhudza Kupemphera M'mawa


Masalimo 5:3

M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga. M'maŵa ndimapemphera kwa Inu, ndi kudikira kuti mundiyankhe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:147

Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 63:1

Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 88:13

Koma ine ndimalirira Inu Chauta, m'maŵa pemphero langa limakafika kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:6

Mtima wanga umayembekeza Chauta kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha, kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:55

Ndimakukumbukirani usiku, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:9

Mtima wanga wonse umalakalaka Inu usiku, mzimu wanga m'kati mwa ine umakufunafunani. Pamene muweruza dziko lapansi, anthu onse okhalamo amaphunzira chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 143:6

Ndimatambalitsira manja anga kwa Inu, mtima wanga umamva ludzu lofuna Inu, monga limachitira dziko louma.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 55:17

Madzulo, m'maŵa ndi masana ndikudandaula ndi kulira, ndipo Iye adzamva mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 4:1

Ndikamaitana, mundiyankhe Inu Mulungu, Mtetezi wanga. Mudabwera kudzandithandiza pamene ndinali m'mavuto. Mundichitire chifundo, ndi kumvera pemphero langa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 90:14

Tidzazeni m'maŵa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika, kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:62

Ndimadzuka pakati pa usiku kuti ndikutamandeni, chifukwa cha malangizo anu olungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:6

Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:1-2

Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga.

Kunyoza kwa adani anga kumandipweteka ngati bala lofa nalo la m'thupi mwanga, akamandifunsa nthaŵi zonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?”

Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu, Mulungu wamoyo. Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:10

Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 3:22-23

Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha.

M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 4:16

Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:5

Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 8:17

Anthu ondikonda, ine nzeru ndimaŵakonda, anthu ondifunafuna mosamala, amandipeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:145-146

Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu.

Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:119

Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.

Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:15

Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:7

Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 63:5-6

Mudzandikhutitsa ndi zonona, ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala.

Ndikagona pabedi panga ndimalingalira za Inu, usiku wonse ndimasinkhasinkha za Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 50:4

Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 4:8

Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:1

Ndikulirira Inu Chauta, ndili m'dzenje lozama lamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:58

Ndikukupemphani ndi mtima wanga wonse, mundikomere mtima molingana ndi malonjezo anu aja.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:9

Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:9

Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:19

Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 36:5

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:5

Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:14-15

Koma ndimadalira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.”

Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 58:9

“Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:80

Mtima wanga ukhale wopanda choudzudzulira pa malamulo anu, kuti ndisachite manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:7

“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 38:15

Koma tsono ndimayembekezera Inu Chauta, Ndinu Chauta, Mulungu wanga amene mudzayankha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:143

Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:8

Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta, koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:18

Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:24

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:82

Maso anga afiira nkuyang'anira malonjezo anu. Ndimafunsa kuti, “Kodi mudzandithandiza liti?”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:28

Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:8

Pajatu Inu mudati, “Muzifunafuna nkhope yanga.” Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:111

Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:1

Ndidzayamika Chauta nthaŵi zonse, pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:7

Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:10

Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:77

Mundichitire chifundo kuti ndikhale ndi moyo, pakuti malamulo anu amandikondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:29

Mundichotse m'njira zondisokeza, kuti ndisayendemo. Mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:1-2

Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa.

ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza.

Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,”

ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.

Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.

Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse.

Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.

Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere.

Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:5

Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo, ndipo mumandisanjika dzanja lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:5-6

Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.

Mtima wanga umayembekeza Chauta kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha, kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:3-4

Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu.

Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:169

Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:66

Patseni luntha ndi nzeru, chifukwa ndimakhulupirira malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:140

Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 111:10

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Wotsata malamulo ake amakhala ndi nzeru zenizeni. Chauta ndi wotamandika mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3-4

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 63:6-7

Ndikagona pabedi panga ndimalingalira za Inu, usiku wonse ndimasinkhasinkha za Inu.

Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 5:12

Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 54:2

Inu Mulungu, imvani pemphero langa, tcherani khutu kuti mumve mau a pakamwa panga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:7

Pa tsiku lamavuto ndimakuitanani, pakuti mumayankha mapemphero anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:8

Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika tsiku ndi tsiku, Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo, ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 84:2

Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:113

Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:5

Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:6

Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 5:2

Imvani kulira kwanga, Inu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti ndikupempha chithandizo kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:72

Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:39

Mundichotsere chipongwe chimene ndimachiwopa, chifukwa malangizo anu ndi abwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:8

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:5

Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:23-24

Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga.

Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 40:1

Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:26

Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:10

ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 5:1-2

Imvani mau anga, Inu Chauta, mverani kusisima kwanga.

Asenzetseni tchimo lao, Inu Mulungu. Upo wao woipa uŵagwetse iwo omwe, muŵachotse pamaso panu chifukwa cha zochimwa zao zambirimbiri, chifukwa akuukirani Inu.

Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.

Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.

Imvani kulira kwanga, Inu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti ndikupempha chithandizo kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:2

Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:170

Kupempha kwanga kumveke kwa Inu. Mundipulumutse potsata malonjezo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:29

Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 143:8

Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 4:4

Opani Mulungu, ndipo musachimwe. Mukhale phee ndipo muganize zimenezi mu mtima pamene mukugona.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 22:3

Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:145

Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:10

Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:142

Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:5

Pamene ndinali m'mavuto ndidapemphera kwa Chauta, ndipo Iye adandichotsera mavutowo.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:3

Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:12

Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 11:28-30

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.

“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”

Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 36:7-9

Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu.

Mumaŵadyetsa zonona m'nyumba mwanu, ndipo mumaŵamwetsa madzi a mu mtsinje wa madalitso anu.

Kwa Inu kuli kasupe wamoyodi, m'kuŵala kwanu ifenso timaona kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:1

Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:1

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 12:2

“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:6

Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:175

Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 66:20

Mulungu atamandike chifukwa sadakane pemphero langa, sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:168

Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:18

Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:14

Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 22:19

Koma Inu Chauta musakhale kutali. Inu, mphamvu zanga, fulumirani kudzandithandiza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:19

Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 146:5

Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 113:7

Amakweza munthu wosauka kuchokera ku fumbi, ndipo amatulutsa ku dzala anthu osoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:43

Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe kulankhula mau anu oona, pakuti ndimakhulupirira malangizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:19-22

Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu.

Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe.

Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake.

Ndiponso tili ndi Wansembe wamkulu woyang'anira nyumba ya Mulungu.

Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 136:1

hokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:1-2

Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?

Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:8

Inu Chauta, ife timatsata njira ya malamulo anu, ndipo timakhulupirira Inu. Mtima wathu umangolakalaka kukumbukira ndi kulemekeza dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:10

Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:14

“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:14

Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:2

Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu, Mulungu wamoyo. Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 19:14

Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 69:13

Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta. Mundiyankhe pa nthaŵi yabwino, Inu Mulungu, chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, ndi chithandizo chanu chokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 77:1-2

Ndikulira mopemba kwa Mulungu, ndi mau okweza ndikufuula kwa Mulungu kuti andimve.

“Chondiŵaŵa ndi chakuti, Mulungu Wopambanazonse wasintha mchitidwe wake.”

Komabe ndidzakumbukira ntchito zanu, Inu Chauta, inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zakalekale.

Ndidzasinkhasinkha za zonse zimene mwachita, ndidzalingalira za ntchito zanu zamphamvuzo.

Njira zanu, Inu Mulungu, nzoyera. Kodi alipo mulungu winanso wamkulu ngati Mulungu wathu?

Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu.

Mudaombola anthu anu ndi mkono wanu wamphamvu, ndiye kuti ana a Yakobe ndi Yosefe.

Pamene madzi adakuwonani, Inu Mulungu, pamene madzi adakuwonani, adachita mantha, inde, nyanja yakuya idanjenjemera.

Mitambo idachucha madzi, mumlengalenga mudachita bingu. Zing'aning'ani mbali ndi mbali.

Phokoso la bingu lanu lidamveka konsekonse, mphezi zanu zidaŵalitsa dziko lonse, dziko lapansi lidanjenjemera ndi kugwedezeka.

Inu mudadzera pa nyanja, njira yanu idadzera pa madzi akuya, komabe mapazi anu sadaoneke.

Pa tsiku lamavuto ndimafunafuna Ambuye. Usiku wonse ndimakweza manja anga ndi kupemphera kosalekeza. Mtima wanga umakana kuusangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 36:5-6

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.

Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya, Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:19

Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 136:2

Thokozani Mulungu wa milungu, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 10:12

Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa mooloŵa manja onse otama dzina lake mopemba.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:24

Ndidzaŵayankha asanatsirize nkomwe kupemphera, ndidzaŵamva akulankhula kumene.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:25

Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 5:11

Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo