Ndikakupemphererani mzinda wathu, sindikupempherera malo okha basi, koma anthu onse okhalamo, kuti mtendere ukhale m'nyumba iliyonse, chifukwa mtendere ukufunika kwambiri kuno ku dziko lathu la Malawi komanso padziko lonse lapansi. Monga mmene lemba la Yeremiya 29:7 limatiuza, ndikofunikira 'kufunafuna mtendere wa mzinda umene ndinakutumizani, ndi kuwupempherera kwa Yehova; pakuti m'mtendere wake mudzakhala ndi mtendere inunso'.
Monga ana a Mulungu, ndi udindo wathu kupempherera malo amene tilimo. Tiyenera kulirira ndi kupembedzera mzinda wathu; sitili pano mwangozi, koma kuti tikhale yankho la Mulungu pakati pa mavuto ambiri a anthu okhala m'derali. Ndikukhulupirira kuti aliyense wa ife ali ndi cholinga chofunika m'mzinda momwe timakhala, tilole Mulungu kuti atithandize ngati zida m'manja mwake kuti ambiri amuone kudzera mwa ife.
Tipempherere ana, achinyamata, akuluakulu, ndi okalamba, tilirire kwa Atate kuti chifuniro chake chabwino chichitike m'miyoyo yawo ndi kuti apeze chipulumutso cha miyoyo yawo. Tisalole choipa kulamulira malo amene tilimo, tiyimirire molimba mtima motsutsana ndi mizimu yoipa yomwe ikufuna kulamulira mzinda wathu; tisachite mantha, Mulungu ali nafe ndipo amatipatsa mphamvu zomenyera nkhondo ndi kulengeza ufulu umene Khristu Yesu anatipatsa kudzera mu nsembe yake pa mtanda.
Kumbukirani kuti nkhondo yathu si yolimbana ndi anthu, koma ndi mizimu yoipa ya dziko lino. Tivale zida zonse za Mulungu ndi kukhulupirira kuti tapambana kale. Titsuke manja athu, tikweze mawu athu, ndi kulira kuti Mulungu atichitire chifundo ndi kuti chifuniro chake chichitike monga momwe adakonzerera kuyambira chilengedwe cha dziko lapansi.
Tigwirizane ndi ena, tigwirizane ndi mipingo ina, tisale kudya, tikhale maso usiku, tilowe m'misewu ya mzinda, ndi kulengeza madalitso a Mulungu m'dzina la Yesu.
Mfumu imalimbitsa dziko pakuweruza molungama, koma imene imaumiriza anthu kuti aipatse ziphuphu, imaononga dziko.
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
Petro adayamba kulankhula, adati, “Zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho.
Amalandira bwino munthu wa mtundu uliwonse womuwopa nkumachita chilungamo.
Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti, “Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu, zinthu ziziŵayendera bwino.
Mtendere ukhale m'kati mwa makoma ako, bata likhale m'nyumba zako zachifumu.”
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu.
Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu.
Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa.
Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete.
Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva.
Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu.
Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima.
Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Tsiku limenelo m'dziko la Yuda anthu adzaimba nyimbo iyi yakuti, “Tili ndi mzinda wamphamvu, Mulungu amautchinjiriza ndi zipupa ndi malinga.
Munthu woipa mukamchitira zabwino, saphunzira zachilungamo. Amachita zoipa m'dziko lachilungamoli, ndipo amalephera kuzindikira ukulu wa Chauta.
Inu Chauta, mwasamula dzanja lanu kuti muŵalange, koma iwo sakuliwona. Anthuwo achite manyazi poona m'mene mumakondera anthu anu, ndipo moto umene mwasonkhera adani anu, uŵapsereze.
Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.
Chauta, Mulungu wathu, ife ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena, sitilemekeza dzina lina, koma lanu lokha.
Ankhanza aja tsopano adafa, sadzakhalanso ndi moyo, sadzabweranso kudzativutitsa, pakuti mwaŵalanga ndi kuŵaonongeratu. Palibenso amene amaŵakumbukira.
Koma Inu Chauta, mwachulukitsa mtundu wathu, mwaukulitsa ndithu. Mwakuza dziko lathu, mwalandirapo ulemu mbali zake zonse.
Inu Chauta, pamene anali m'masautso, anthu anu adakufunafunani, pamene munkaŵalanga, adapemphera kwa Inu.
Inu Chauta, mwatiliritsa monga momwe amalirira mkazi pa nthaŵi yobala mwana.
Ife tidamva ululu, ndipo tidavutika ngati mkazi pa nthaŵi yobala mwana, koma sitidapindule kanthu. Sitidadzetse chipulumutso m'dziko lapansi pano, sitidabadwitse anthu atsopano pansi pano.
Anthu anu amene adafa adzakhalanso ndi moyo, matupi ao adzauka. Inu nonse amene muli m'manda, dzukani ndi kuimba mosangalala. Monga momwe mame amafeŵetsera pansi kutsitsimutsa zomera, momwemonso Chauta adzaukitsa anthu amene adafa kale.
Tsekulani zipata za mzinda, kuti mtundu wotsata malamulo ndi wokhulupirika uloŵe.
Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera,
Inu Mulungu, anthu amakutamandani ponseponse, monga dzina lanu latchuka pa dziko lonse lapansi. Dzanja lanu lamphamvu limapambana nthaŵi zonse.
Anthu okhala mu Ziyoni akondwe. A ku Yuda asangalale chifukwa cha kaweruzidwe kanu kolungama.
Zungulirani Ziyoni yense, inde zungulirani mzinda wonsewo, ndipo muŵerenge nsanja zake.
Yang'anani bwino machemba ake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzathe kusimbira mbadwo wakutsogolo.
Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”
mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu, wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi. Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu, ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Pambali pa mtsinjewo, pa gombe lililonse, padzakhala mitengo yobereka zipatso za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota, ndipo zipatso zake zidzakhala zosalekeza. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake ndi ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya, ndipo masamba ake azidzachita mankhwala.”
Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.
Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu
Yesu atayandikira, nkuwona Yerusalemu, adalira chifukwa cha mzindawo.
Adati, “Ha, iwenso ukadangodziŵa lero lino zinthu zopatsa mtendere! Koma ai, tsopano maso ako sangathe kuziwona.
Anthu anu adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthaŵi yaitali. Adzamanganso pa maziko akalekale. Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma, omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.”
Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
“Komabe m'tsogolo mwake ndidzaupatsanso moyo ndi kuuchiritsa. Anthu ake ndidzaŵachiritsa ndi kuŵapatsa zabwino zochuluka ndi mtendere weniweni.
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,
koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.
Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.
Muphunzitse mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma.
Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu.
Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Aweruzi ako ndidzaŵakhazikitsanso ngati pa masiku akale aja. Aphungu akonso ndidzaŵakhazikitsanso ngati poyamba paja. Pambuyo pake iweyo udzatchedwa mzinda waungwiro, mzinda wokhulupirika.”
Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu.
Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Amadzetsa mtendere m'malire a dziko lako, amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.
Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu, chilungamo ndiye chimalimbitsa ufumu wake.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?
Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Iwe Yerusalemu dzuka, ŵala, kuŵala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuŵalira.
Chauta akuuza Yerusalemu kuti, “Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu ao adzakutumikira. Ndidakulanga pamene ndinali wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndi kukuchitira chifundo.
Zipata zako zidzakhala zotsekula nthaŵi zonse. Usana ndi usiku womwe sadzazitseka, kuti choncho anthu a mitundu yonse adzabwere ndi chuma chao kwa iwe, akuyenda pa mdipiti, mafumu ao ali patsogolo.
Koma maiko ndi mafumu amene sakutumikira, adzaonongekeratu. Anthu a mitundu imeneyo adzaonongeka kotheratu.”
“Mitundu itatu ija ya mitengo ya paini, imene ili yabwino kwambiri m'nkhalango ya ku Lebanoni, adzabwera nayo kuti akongoletsere Nyumba yanga. Motero m'Nyumba m'mene ndimakhala Ine mudzalemekezeka.
Ana a amene adaakuzunzapo adzabwera ndipo adzakugwadira kuwonetsa ulemu. Onse amene adaakunyozapo adzakuŵeramira mpaka pansi. Adzakutchula kuti Mzinda wa Chauta, ndiye kuti Ziyoni, mzinda wa Woyera uja wa Israele.”
“Ngakhale anthu adakusiya nadana nawe, osadutsanso mwa iwe, ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe pa mibadwo ndi mibadwo.
Monga mwana woyamwa udzadya chuma cha anthu a mitundu ina, ndipo mafumu ao omwe adzakusamala. Motero udzadziŵa kuti Ine Chauta ndine Mpulumutsi wako, ndipo kuti ndine Momboli wako, Wamphamvu uja wa Yakobe.”
“Ndidzakupatsa golide m'malo mwa mkuŵa, m'malo mwa chitsulo ndidzakupatsa siliva, mkuŵa m'malo mwa mtengo, chitsulo m'malo mwa mwala. Okuyang'anira ndidzaŵasandutsa amtendere, okulamulira ndidzaŵasandutsa olungama.
Ziwawa sizidzamvekanso. Dziko lako silidzaonongekanso. Ndidzakhala ngati linga lokuteteza, ndipo udzanditamanda chifukwa chokupulumutsa.”
“Sipadzafikanso dzuŵa loti likuŵalire masana, kapena mwezi wokuŵalira usiku. Koma Ine Chauta ndiye ndidzakuŵalire mpaka muyaya. Ine Mulungu wako ndiye ndidzakhale ulemerero wako.
Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuŵalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
Chokuunikira ngati dzuŵa sichidzaloŵanso, ndipo chokuunikira ngati mwezi sichidzazimiriranso, chifukwa ndi Chauta amene adzakhala kuŵala kwako mpaka muyaya. Choncho masiku ako olira adzatha.
Anthu ako onse adzayenda m'njira zoyenera, ndipo dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya. Anthuwo ndidaŵaika ndine, ndidaŵalenga ndine, kuti aonetse ulemerero wanga kwa onse.
Ngakhale kabanja kakang'onong'ono kadzasanduka fuko, ndipo kafuko kakang'onong'ono kadzasanduka mtundu wamphamvu. Ndidzachita zimenezi mofulumira nthaŵi yake itafika. Ine ndine Chauta.”
Anthu a mitundu ina adzatsata kuŵala kwako, mafumu adzalondola kunyezimira kwako konga dzuŵa limene likutuluka kumene.
Tipulumutseni, tikukupemphani Inu Chauta. Chauta, tikukupemphani kuti zinthu zitiyendere bwino.
Uŵapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe. Uŵalanditse amene akuyenda movutikira popita kukaŵapha.
Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,” kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona? Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa? Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake?
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse. Uwone m'mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendere bwino masiku onse a moyo wako.
“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa.
Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.
Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu.
Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.
Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo. Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse.
Mulungu akamadalitsa anthu ake, mzinda wonse umatukuka. Oipa akaonongeka, anthu amafuula mwachimwemwe.
Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko,
ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina.
Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha.
Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta.
Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”
Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.”
Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu.
Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale.
Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale.
Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta, anthu amene Chauta waŵasankha akeake.
Chiwalo chimodzi chikamamva kuŵaŵa, ziwalo zonse zimamvanso kuŵaŵa. Chiwalo chimodzi chikamalandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwa nao.
Ngwodala amene alikudza m'dzina la Chauta. Tikufunirani madalitso ochokera m'nyumba ya Chauta.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate.
Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao.
Anthu ako ndidzaŵaphunzitsa ndekha, Ine Chauta, ana ako ndidzaŵadalitsa ndi kuŵapatsa mtendere waukulu.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu:
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.
Pakuti munthu wochita chilungamo sadzagwedezeka konse, sadzaiŵalika mpaka muyaya.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Anthu a Mulungu adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala m'menemo mpaka muyaya.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
“Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu,
Abale, chimene ndimakhumbitsa ndi mtima wanga wonse, ndipo chimene ndimapempha Mulungu, ndi chakuti Aisraele apulumuke.
Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Chauta amakonda anthu odana ndi zoipa. Iye amasunga moyo wa anthu ake oyera mtima. Amaŵapulumutsa kwa anthu oipa.
Ngodala anthu amene amakhala m'Nyumba mwanu, namaimba nyimbo zotamanda Inu nthaŵi zonse.
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera.
Zoonadi, amene amasunga Israele, ndithu sadzaodzera kapena kugona.
Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu. Chauta ndiye wotilamula, Chauta ndiye mfumu yathu, ndiye amene adzatipulumutsa.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Madalitso olandira anthu olungama amakweza mzinda, koma pakamwa pa anthu oipa mtima pamapasula mzindawo.
Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena.
Khala kuno ndipo Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakudalitsa chifukwa ndidzapereka maiko onseŵa kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako. Ndidzasunga lumbiro limene ndidachita kwa bambo wako Abrahamu.
Ndimalirira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu kothaŵira kwanga, ndinu zanga zonse m'dziko la amoyo.”
Muzikometsa ku mizinda kumene ndidakupirikitsirani ku ukapoloko, kuti zonse zizikuyenderani bwino. Muzipempherera mizindayo kwa Chauta, chifukwa choti mizindayo ikakhala pa mtendere, inunso mudzakhala pabwino.
Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu.
Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wa madzi m'manja mwa Chauta. Amauwongolera ku zimene Iyeyo akufuna.
Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.
Amakuza mitundu ina ya anthu, koma inanso amaiwononga. Amachulukitsa mafuko, nkuŵamwazanso.
Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai.
Nchifukwa chake tsono khalani anzeru, inu mafumu. Chenjerani inu amene muli olamula dziko lapansi.
Tumikirani Chauta mwamantha ndi monjenjemera.
Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.
Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.
Koma Petro ndi atumwi enawo adati, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu.