Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

MAVESI OLIMBIKITSA

Moyoyo, ndikudziwa kuti nthawi zina zinthu zimavuta kwambiri. Timakumana ndi mavuto osiyanasiyana, nthawi zina timamva ngati titayika mtima. Koma dziwani izi, Mulungu watiitana kuti tikhale ngati mitengo yomera m’mphepete mwa mtsinje, yomwe imakhalabe yolimba ngakhale mvula ikugwa bwanji.

Ndikudziwa kuti nthawi zina ukhoza kumva ngati sudzatuluka m’mavuto amene ukukumana nawo. Koma Mulungu, m’chifundo chake chachikulu, nthawi zonse amatilankhula mawu olimbikitsa. Mawu ake ndiwo amene amatilimbitsa, amatipatsa mphamvu kuti tipitirize ulendo wathu. Chofunika ndicho kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumvera Mulungu.

Dziwani kuti simuli nokha. Mulungu ali nanu nthawi zonse. Adzachiritsa mabala anu onse ndipo adzakudzazani ndi chimwemwe. Ndikupempherera kuti Mzimu Woyera akubweretsereni mtendere ndi mpumulo umene mukufuna. Mulungu alimbitse mtima wanu ndi kukupatsani mphamvu zatsopano.


1 Atesalonika 5:18

Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 20:4

Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi.

Mutu    |  Mabaibulo
Numeri 6:24-26

Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni.

Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima.

Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:3-4

Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani.

Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu.

Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 90:12

Tsono tiphunzitseni kuŵerenga masiku athu, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Yuda 1:2

Mulungu achulukitse chifundo chake, mtendere wake ndi chikondi chake kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:24

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:13-14

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:13

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 65:11

Pakutha pa chaka mumapereka zokolola zambiri mwa ubwino wanu, kulikonse kumene Inu mupita, kumapezeka dzinthu dzambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:4

Nthaŵi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:3-4

Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.

Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa.

Nchifukwa chake, monga Malembo anenera, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.”

Nthaŵi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:10

Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo
3 Yohane 1:2

Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 1:5

“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 29:11

Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 9:11

Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo ndidzaonjezera zaka pa moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:1-2

Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.

Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina.

Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha.

Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta.

Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”

Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.

Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.”

Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu.

Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale.

Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale.

Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.

Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga.

Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo.

Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake.

Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.

Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe.

Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo.

Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu.

Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha.

Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika.

Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino.

Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 9:15

Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso yake yosaneneka.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 2:7-8

Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro.

Ndiye mlonda wa njira zolungama, amatchinjiriza njira ya anthu ake oyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 46:4

Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:4

Muzikondwa mwa Ambuye nthaŵi zonse. Ndikubwerezanso kuti, “Muzikondwa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:8

Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:7

Koma Chauta amakhala pa mpando wake waufumu nthaŵi zonse, adakhazika mpando wake kuti aziweruza.

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 3:22-23

Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha.

M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 92:1-2

Nkwabwino kuthokoza Chauta, kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.

Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano.

Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga, makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira.

Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni.

Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu.

Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira,

imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota.

Nkwabwino m'maŵa kulalika za chikondi chanu chosasinthika, ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu,

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 2:10

Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:14

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 95:1-2

Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa.

Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.”

Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo.

Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 21:4

Iyo idakupemphani moyo, ndipo Inu mudaipatsa moyo wautali, wamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 3:1

Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu:

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 126:3

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:3-6

Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani.

Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu.

Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa.

Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:16

Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:7

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 84:11

Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:4

Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1-2

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.

Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.

Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:1-2

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.

Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:1-3

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.

Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.

Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:10

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:4

Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wamphamvuzonse! Inu nokha ndinu woyenera kutambasula ulemu wonse ndi kulambira. Ndikukupemphani kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu kuti mundipatse mphamvu zatsopano, ndatopa ndipo ndataya mtima wopitirira. Nthawi zina ndimamva ngati ndiyenera kusiya zonse, ndichifukwa chake ndikupempha kuti munditsanulire chisomo ndi chifundo pa moyo wanga kuti ndipitirire ku cholinga changa popanda kuima. Mawu anu amati: "Chifundo changa ndi linga langa, mphamvu yanga ndi wopulumutsa wanga, chishango changa, amene ndimakhulitsa; amene aweramitsa anthu pansi panga." Ngakhale mavuto a kuntchito ndi kunyumba akufuna kundigwetsa, ndidzakutambasulani Ambuye ndipo ndidzakhala ndikuyembekezera thandizo lanu. Nditsogolereni Mzimu Woyera kuti ndithamangire kwa Yesu popanda kutopa kapena kudandaula. Ndikufuna kukhala wolimba mtima ndi wamphamvu, koma ndikufunika thandizo lanu ndi mphamvu zanu Ambuye. Lero ndikulengeza kuti Mulungu ndiye chishango changa ndi Ambuye wanga, inu ndinu thanthwe langa, wochirikiza wanga, wopulumutsa wanga, inu ndinu mphamvu yanga ndi chishango changa, chipulumutso changa champhamvu, pothawirapo panga, ndipo chifukwa chake sindidzagwa kapena kusunthika pa thanthwe lomwe ndi Khristu. Munditsuke ndi kundikonza Ambuye, lamulirani maganizo anga, malingaliro anga ndi mbali zonse za moyo wanga, mundipatse chimwemwe chanu ndi mtendere wanu. M'dzina la Yesu. Ameni.