Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha.
M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.
Inde, Mulungu adatipulumutsa, koma tikuyembekezabe chipulumutsocho. Koma tsono tikamaona ndi maso zimene tikuziyembekezazi, apo si chiyembekezonso ai.
Koma ngati tiyembekeza zimene sitidaziwone ndi maso, timazidikira mopirira.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Mulungu adapereka Malamulo kuti anthu azindikire kuchuluka kwa machimo ao. Koma pamene uchimo udachuluka, kukoma mtima kwa Mulungu kudachuluka koposa.
Choncho monga uchimo unkalamulira anthu ndi kudzetsa imfa pa iwo, momwemonso kunali koyenera kuti kukoma mtima kwa Mulungu kulamulire pakudzetsa chilungamo kwa anthu, ndi kuŵafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira,
kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m'dziko la amoyo.
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Chauta amayang'ana anthu omumvera, ndi odalira chikondi chake chosasinthika.
Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala.
Tamandani Chauta ndi pangwe. Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu.
Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Koma ine ndidzadalira Chauta. Ndidzaika mtima pa Mulungu Mpulumutsi wanga. Mulungu wanga adzandimva.
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.
Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.
Mafumu adzakhala ngati atate okulerani, akazi a mafumuwo adzakhala ngati amai okuyamwitsani. Adzagwetsa nkhope zao pansi ndi kukuŵeramirani. Adzaseteka fumbi la m'mapazi mwanu modzichepetsa. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndipo amene amakhulupirira Ine sadzachita manyazi.”
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.
Udzalimba mtima poti chikhulupiriro chilipo. Mulungu adzakutchinjiriza, ndipo udzapumula mwamtendere.
Mulungu adati, “Zidzukulu zako zidzachulukadi.” Ndipo ngakhale zimenezi zinali zosayembekezeka konse, Abrahamu adalimbikirabe kukhulupirira kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.
Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye.
Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika.
Iwe Israele, khulupirira Chauta. Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani, Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga.
Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.
Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa,
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu.
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa, ndipo m'katikati mwangamu ndikusangalala. Thupi langanso lidzakhala pabwino,
Munthu aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi pa Khristu, amadzisandutsa woyera monga momwe Khristuyo ali woyera.
Zoonadi, onse okhulupirira Inu asaŵachititse manyazi, koma muchititse manyazi onse ochita dala zosakhulupirika.
Ndidzakuthokozani Inu Mulungu mpaka muyaya, chifukwa cha zimene mwachita. Ndidzatamanda dzina lanu pamaso pa anthu okukondani, pakuti ndinu abwino.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Ndikagona pabedi panga ndimalingalira za Inu, usiku wonse ndimasinkhasinkha za Inu.
Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.
Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.
Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi.
Nchifukwa chake timagwira ntchito kolimba, ndipo timayesetsa kupambana, pakuti chiyembekezo chathu chili pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka okhulupirira Khristu.
Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwa kukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma.
Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse.
Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke.
“Nanga tsopano, Inu Ambuye, ndikudikira chiyani? Chikhulupiriro changa chili pa Inu.
Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse. Musandisandutse chinthu chochinyodola zitsiru.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Koma Khristu anali wokhulupirika m'nyumba ya Mulungu ngati mwana wolamulira pa zonse za m'nyumba mwakemo. Ndipo nyumba yakeyo ndife, ngati tiika mphamvu pa kulimba mtima ndi kunyadira zimene tikuziyembekeza.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.
Gwero la zonsezi ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzalandira zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Mudamva za zimenezi pamene mau oona, adakufikani poyamba paja. Mau oonawo ndi Uthenga Wabwino.
Mudzanditsitsimutsanso Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa, mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka.
Inu mudzaonjezera ulemu wanga ndipo mudzandisangalatsanso.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Tsiku limenelo aliyense adzati, “Uyu ndiye Mulungu wathu! Tidamkhulupirira kuti adzatipulumutsa. Iyeyu ndiye Chauta. Tidamkhulupirira, tsopano tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa choti watipulumutsadi.”
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
“Mtengo chiyembekezo chake nchakuti akaudula udzaphukanso, nthambi zake sizidzaleka kuphuka.
Ngakhale mizu yake ikalambe m'nthaka, ndipo chitsa chake chiwole,
komabe chinyontho chikafika, udzaphukira, udzaphukadi nthambi ngati mtengo wanthete.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.
Pamene ndinali m'mavuto ndidapemphera kwa Chauta, ndipo Iye adandichotsera mavutowo.
Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani?
Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira munthu.
Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira mafumu.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe.
Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.
Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu.
Koma chonsecho ndili ndi Inu nthaŵi zonse. Inu mumandigwira dzanja lamanja.
Mumandiwongolera ndi malangizo anu, pambuyo pake mudzandilandira ku ulemerero.
Nanga ndili ndi yani kumwamba kupatula Inu? Pansi pano palibe kanthu kena kamene ndimafuna, koma Inu nokha.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.”
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga.
Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu.
Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.
Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu.
Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza.
Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa.
Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera.
Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!”
Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza.
Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe.
Chauta ndi wokoma mtima ndi wolungama. Mulungu wathu ndi wachifundo.
Chauta amasunga a mtima wodzichepetsa. Pamene ndidagwa m'zoopsa, Iye adandipulumutsa.
Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo.
Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake.
Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka.
Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.
Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha.
Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi.
Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho;
limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse,
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.
Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.
Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima.
Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.
Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe amene adaona kapena kumva za Mulungu wina wonga Inu, wochitira zotere anthu omkhulupirira.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni.
Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano.
Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa.
Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai.
Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu.
Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu.
Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri.
Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo.
Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo.
Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi.
Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa.
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Inu Chauta Wamphamvuzonse, ngwodala munthu woika chikhulupiriro chake pa Inu.
“Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja.
Kumene tsopano kuli mitengo yaminga kudzamera mitengo ya paini. Kumene tsopano kuli mkandankhuku kudzamera michisu. Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Ine Chauta, ngati chizindikiro chamuyaya chimene sichidzafafanizika konse.”
Koma pali chinanso chimene ndimachikumbukira, chimenecho ndicho chimandilimbitsa mtima.
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha.
M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
Chauta ndiye zanga zonse motero ndimadalira Iyeyo.
Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.
Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake.
Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa.
Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake.
Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo.
Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera.
Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse.
Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Chinthu chochiyembekeza chikalephereka, chimafooketsa mtima, koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi, chili ngati mtengo wopatsa moyo.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Kukhulupirika kwanga ndi kulungama kwanga kunditeteze, popeza kuti ndakukhulupirirani.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu mtima wanga wakonzekadi. Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda.
Ndimalirira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu kothaŵira kwanga, ndinu zanga zonse m'dziko la amoyo.”
Tikufunitsitsa kuti aliyense mwa inu apitirire kuwonetsa changu chomwechi mpaka potsiriza, kuti chiyembekezo chanu chifike pake penipeni.
Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza.
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.
“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
Khungu langa litatha nkuwonongeka, m'thupi langa lomweli ndidzamuwona Mulungu.
Ine ndemwe ndidzamuwona, osati winanso ai. Ndidzamuwona ndi maso angaŵa. Mtima wanga ukulifunitsitsa tsikulo.
Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
Lewa kupsa mtima ndi kukwiya. Usachite zimenezi, pakuti sudzapindula nazo kanthu.
Pajatu anthu oipa adzaonongeka, koma okhulupirira Chauta adzalandira dziko kuti likhale lao.
Munyadire dzina lake loyera. Ikondwe mitima ya anthu amene amapembedza Chauta.
Dziko lao lidadzaza ndi achule, ngakhale m'zipinda za mafumu zomwe.
Adalankhula, ndipo kudatuluka ntchentche zochuluka, mtundu wa udzudzu udaloŵa m'dziko mwao monse.
Adaŵagwetsera matalala m'malo mwa mvula, adaŵagwetsera ching'aning'ani chimene chinkang'anima m'dziko mwao monse.
Adagwetsa mipesa yao ndi mikuyu yao, adathyola mitengo yonse ya m'dziko mwao.
Adalankhula, ndipo kudafika dzombe ndi mandowa osaŵerengeka,
amene adaononga zomera zonse za m'dziko mwao, nadya zipatso zonse za m'minda mwao.
Iye adapha ana onse achisamba m'dziko mwao, ana onse oyamba, oŵabala akadali abiriŵiri.
Kenaka Chauta adaŵatulutsa Aisraele atatenga siliva ndi golide, pakati pa mafuko awo panalibe amene adafooka.
Aejipito adasangalala pamene iwo adapita, chifukwa ankachita nawo mantha anthuwo.
Chauta adaika mtambo kuti uziphimba anthu ake, adaika moto kuti uziŵaunikira usiku.
Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake. Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndikupemphera kwa Inu Mulungu, chifukwa mudzandiyankha. Tcherani khutu kuti mumve mau anga.
Onetsani chifundo chanu pakuchita zodabwitsa, Inu amene mumaŵapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja onse obwera kwa Inu, kuthaŵa adani ao.
Amene mudaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa. Chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pankhope pao. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chisangalalo. Chisoni ndi kubuula zidzatha.
Anthu inu, ikani mtima wanu pa Iye nthaŵi zonse. Muuzeni zonse za kukhosi kwanu. Mulungu ndiye kothaŵira kwathu.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.
Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao.
Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo.
Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate.
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana.
Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
“Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga.
Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse.
Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu.
Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu.
Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo.
M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo.
Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu.
“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”
Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?”
Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.
Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma.
“Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu.
Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine.
Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire.
Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.
Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira.
Ndidafuula kwa Iye, ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga.
Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera.
Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa.
Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu.
Mulungu atamandike chifukwa sadakane pemphero langa, sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa?
Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.”
Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.
Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, monga adalamulira Mulungu, Mpulumutsi wathu, ndiponso Khristu Yesu, chiyembekezo chathu.
Mutichitire chifundo, Inu Chauta, tikukhulupirira Inu. Mutitchinjirize ndi dzanja lanu lamphamvu tsiku ndi tsiku, ndipo mutipulumutse pa nthaŵi yamavuto.
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo.
Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
Koma zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse, maganizo a mumtima mwake amakhazikika mpaka muyaya.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Koma tsopano mwamasulidwa ku uchimo, ndipo ndinu otumikira Mulungu. Phindu lake ndi kuyera mtima, ndipo potsiriza pake kulandira moyo wosatha.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu.
Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.