Ana anga, ndi ofunika kwambiri kwa Mulungu. Iye amawakonda kwambiri, ndipo ndi ntchito yake yabwino kwambiri. Ngakhale ali aang'ono, ali ndi maloto ambiri, ndipo amatha kutibweretsera chimwemwe chochuluka ndi kumwetulira kwawo kokha.
Monga mukudziwira, dziko lapansi likuipa kwambiri, ndipo anthu ambiri sakondana monga kale. Ndikofunikira kuti muziwapempherera ana anu nthawi zonse, chifukwa mdani amafuna kuwavulaza ndi kuwabweretsera mavuto.
Muyenera kukhala ngati mpanda wowateteza kuti zolinga zoyipa za mdani zisachitike. Mapemphero anu ali ndi mphamvu kwambiri. Mulungu amamva pemphelo lililonse, mawu alionse, ndipo amatumiza angelo kuti awateteze nthawi zonse.
Musaleke kuwapempherera, chifukwa mukachita zimenezo, simuteteza tsogolo la ana anu okha, komanso tsogolo la ana onse padziko lapansi. Mngelo wa Yehova amazungulira iwo akumuopa ndi kuwapulumutsa. Mulungu watumiza angelo ake kuti aziwasamalira nthawi zonse.
Ambuye adzawatumizira chitetezo nthawi zonse, choncho khulupirirani kuti Mulungu ali pafupi ndi ana athu. Ameni!
Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”
Kukadakhala kwabwino kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamponya m'nyanja, kupambana kuti achimwitse mmodzi mwa ana ang'onoang'onoŵa.
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”
Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao,
Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?”
Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.
“Tsono Ufumu wakumwamba tingaufanizire motere: Panali mfumu ina imene idaaitanitsa antchito ake kuti iwonenso bwino ngongole zao.
Atangoyamba kumene, adabwera ndi wantchito wina amene anali ndi ngongole ya ndalama zochuluka kwabasi.
Ndiye popeza kuti adaasoŵa chobwezera ngongoleyo, mbuye wake uja adalamula kuti amgulitse wantchitoyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake ndi zake zonse, kuti ngongole ija ibwezedwe.
Apo wantchito uja adamgwadira nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani ndithu zonse.’
Mbuye wake uja adamumveradi chifundo, ndipo adamkhululukira ngongole ija, namlola kuti apite.
“Koma pamene wantchitoyo ankatuluka, adakumana ndi mmodzi mwa antchito anzake, yemwe iye adaamkongoza ndalama zochepa. Adamgwira pa khosi mwaukali namuuza kuti, ‘Bweza ngongole yako ija.’
Apo wantchito mnzake uja adadzigwetsa pansi ku mapazi ake nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani.’
ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.
Koma iye adakana, nakamponyetsa m'ndende kuti mpaka abweze ndithu ngongoleyo.
“Antchito anzake ena ataona zimenezi, adamva chisoni kwambiri. Adapita kukafotokozera mbuye wao zonsezo.
Tsono mbuye wakeyo adamuitana namuuza kuti, ‘Wantchito woipa iwe, ine ndinakukhululukira ngongole yonse ija pamene unandidandaulira.
Kodi sunayenera kuti iwenso umchitire chifundo wantchito mnzako, monga ndinakuchitira iwe chifundo?’
Motero mbuye wakeyo adapsa mtima kwambiri, nampereka kuti akamzunze mpaka atabweza ngongole yonse ija.
“Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”
Nchifukwa chake munthu wodzichepetsa ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wakumwamba.
Ndipo aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene.”
“Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukammiza m'nyanja pozama.
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Anthu ako ndidzaŵaphunzitsa ndekha, Ine Chauta, ana ako ndidzaŵadalitsa ndi kuŵapatsa mtendere waukulu.
“Mundimvere, inu zidzukulu za Yakobe, inu nonse otsala a m'nyumba ya Israele. Ndakhala ndikukusamalani chibadwire chanu, ndidakunyamulani kuyambira m'mimba mwa amai anu.
Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake.
Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo.
Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
Nawonso ana ndi makanda omwe amauimbira. Mwamanga linga chifukwa cha adani anu, kuti mugonjetse onse okuukirani.
Ana sadzafanso ali akhanda, ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zao zonse. Amene adzafe ali a zaka zana limodzi zokha adzaoneka ngati anyamata. Kufa zisanakwane zaka zana limodzi kudzasonyeza kutembereredwa.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako.
Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.
Munthu abwino amakhala mwachilungamo, ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake.
Mukhale tcheru, ndipo musadzaiŵale zonse zimene mudaziwona. Zimenezo zisachoke m'mitima mwanu pa moyo wanu wonse. Muzizifotokoza kwa ana anu ndi kwa zidzukulu zanu zomwe.
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.
Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu.
Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.
Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima.
Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo.
Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira.
Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye.
Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima.
Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro.
Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse.
Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.
Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
Ndithu ndikunenetsa kuti amene salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.”
Yesu ataona zimenezi, adakalipa naŵauza kuti, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Mwana uyu ndidachita kupempha, ndipo Chauta wandipatsa chopempha changacho.
Nchifukwa chake ndampereka kwa Chauta. Moyo wake wonse mwanayu adzakhala wake wa Chauta.” Ndipo onsewo adapembedza Chauta kumeneko.
Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.
Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Koma chonsecho ndili ndi Inu nthaŵi zonse. Inu mumandigwira dzanja lamanja.
Mumandiwongolera ndi malangizo anu, pambuyo pake mudzandilandira ku ulemerero.
Tsono mwana iwe, udzatchedwa mneneri wa Mulungu Wopambanazonse, chifukwa udzatsogola pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zao.
Udzadziŵitsa anthu ao kuti Mulungu adzaŵapulumutsa pakuŵakhululukira machimo ao.
Mulungu wathu ndi wa chifundo chachikulu, adzatitumizira kuŵala kwa dzuŵa lam'maŵa kuchokera Kumwamba.
Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
Ndimakumbukira chikhulupiriro chako chosanyenga. Chikhulupiriro chimenechi adaayamba ndi agogo ako aLoisi kukhala nacho. Amai ako aYunisi anali nachonso, ndipo tsopano sindikukayika konse kuti iwenso uli nacho.
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu.
Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye.
Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine.
Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.