Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.
pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.
Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.
Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.
Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.
Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika. Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?
Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.
ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeke chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu,
Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu,
Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.
Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafune.
Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo.
Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi. Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru, ndi lilime lake linena chiweruzo. Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake; pakuyenda pake sadzaterereka. Woipa aunguza wolungama, nafuna kumupha. Yehova sadzamsiya m'dzanja lake; ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye. Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya. Ndapenya woipa, alikuopsa, natasa monga mtengo wauwisi wanzika. Koma anapita ndipo taona, kwati zii; ndipo ndinampwaira osampeza. Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere. Koma olakwa adzaonongeka pamodzi; matsiriziro a oipa adzadulidwa. Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso. Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.
Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.
Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya?
Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;
Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani!
Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera. lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso; Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,
Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake.
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,
Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera m'chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo.
Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye.
Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.
Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.
Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi; adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa.
kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.
Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.
Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.
Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.
Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.
Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.
Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.
Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'chikondi cha mulungu ndi m'chipiriro cha Khristu.
M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.