Zefaniya 3:8 - Buku Lopatulika8 Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Chauta akunena kuti, “Nchifukwa chake mundidikire, mudikire tsiku limene ndidzakuimbeni mlandu. Pakuti ndatsimikiza zosonkhanitsa mitundu ya anthu pamodzi ndi maufumu onse, kuti ndiŵaonetse kusakondwa kwanga amve ululu wa ukali wanga. Dziko lonse lapansi lidzapserera ndi moto waukali wa mkwiyo wanga.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Choncho mundidikire,” akutero Yehova, “chifukwa cha tsiku limene ndidzaperekera umboni. Ndatsimikiza kusonkhanitsa pamodzi mitundu ya anthu, kusonkhanitsa maufumu ndi kutsanulira ukali wanga pa iwo; mkwiyo wanga wonse woopsa. Dziko lonse lidzatenthedwa ndi moto wa mkwiyo wa nsanje yanga. Onani mutuwo |