Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 3:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Pamenepo ndidzasintha malankhulidwe a mitundu yonse, nkuŵapatsa malankhulidwe abwino, kuti onse azitama dzina la Chauta mopemba ndi kumamtumikira mogwirizana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova ndi kumutumikira Iye pamodzi.

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 3:9
21 Mawu Ofanana  

Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.


Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwa mwana wamwamuna: anamutcha dzina lake Enosi: pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.


Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova.


Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Tsiku limenelo padzakhala mizinda isanu m'dziko la Ejipito yolankhula chinenero cha Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzatchedwa, Mzinda wa chionongeko.


Ndilenga chipatso cha milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutali, ndi kwa iye amene ali chifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamchiritsa iye.


nakhudza nalo kukamwa kwanga nati, Taona ichi chakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zaomboledwa.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


nuiphatikize wina ndi unzake ikhale mtengo umodzi m'dzanja lako.


Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi amphimba pansi pa nyanja.


Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.


Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa.


Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa