Ana inu, tiyeni tiganizire ana athu, ndi amene akufuna chisamalo, chikondi, ndi kumvetsetsa kwambiri m'nyumba mwathu. Tiyenera kuwasamalira nthawi zonse, ndipo nthawi yathu yabwino kwambiri tiyenera kuigwiritsa ntchito ndi iwo.
Masiku ano, ana athu akukumana ndi mavuto ambiri; mdani akufuna kuwavulaza kuti awaletse kukula m'chikhulupiriro. Anthu ambiri sakusamala ndipo zoipa zikuchulukirachulukira. Anthu oipa akufuna kuwavulaza ana amene Yesu anati, "Lolani ana aang'ono abwere kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wa otere."
Mwana aliyense ali ndi cholinga chabwino; Atate wakumwamba amawakonda kwambiri ndipo amatiuza kuti tikhale ngati iwo. Ndikukulimbikitsani kuti muzisamalira ana aang'ono m'nyumba mwanu, muziwateteza, ndipo ngati muli ndi mphamvu, muziwachitira zabwino. Mulungu adzakudalitsani chifukwa cha zimenezi.
Tsiku lililonse, ana ambiri amatayidwa, amazunzidwa, ndipo sakulandira chilungamo. Thandizani kukula kwawo ndipo muwachitire zinthu zabwino zomwe zingawathandize kuiwala zopweteka ndi chisoni chawo. Pali ana ambiri omwe ali m'misewu omwe akufuna chakudya, chitonthozo, ndi pokhala, ndipo alibe zovala zokwanira. Ndibwino kuwalimbikitsa ndi mawu abwino, koma ngati mungathe kuchita zambiri, musazengereze.
Yang'anani m'maso mwawo, ndipo monga momwe Yesu anakukomerani mtima, mukhale nacho chifundo ndipo musanyalanyaze. Dziko lino likufuna kuti ana a Mulungu adzaze ndi chikondi, ndipo inu mwamuitanidwa kuchita ntchito yofunika kwambiriyi.
Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.
Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.
Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.
Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.
Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.
Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere.
Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye; chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.
Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.
Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.
Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.
Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.
Ndipo anatenga kamwana, nakaika pakati pao, nakayangata, nanena nao, Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.
Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.
Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pamaso chifukwa cha akufa.
Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.
Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?
Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani? Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.
Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.
Usamane mwana chilango; pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai. Udzammenya ndi nthyole, nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda.
Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.
Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda, nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.
Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.
nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi. Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordani, kulilandira.
Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.
Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru. Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;
Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.
Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.
Ndipo Yakobo anatukula maso ake, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja. Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga padzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine. Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindikwanira. Ndipo anamkakamiza, nalandira. Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine. Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali anthete, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa. Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang'onopang'ono monga mwa mayendedwe a zoweta zili pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri. Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga. Ndipo Esau anabwerera tsiku lomwelo kunka ku Seiri. Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti. Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumzinda wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mzindapo. Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, padzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu. Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse.
Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi, chifukwa cha maweruzo anu olungama.
Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;
Ndipo anadza nao kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene ophunzira anaona anawadzudzula. Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere. Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.
Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.
Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.
Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?
Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka. Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu; zinduna ndi oweruza onse a padziko. Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo. Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya. Mlemekezeni, angelo ake onse; mlemekezeni, makamu ake onse. Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
Imba, iwe wouma, amene sunabale; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabale mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!
Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,
Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.
Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.
Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
Ndiye chifundo changa, ndi linga langa, msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga; chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama; amene andigonjetsera anthu anga.
Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:
ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.
Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti, Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana. Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.
M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.
Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.