Mateyu 11:25 - Buku Lopatulika25 Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda: Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda: Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Pa nthaŵi imeneyo Yesu adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono. Onani mutuwo |