Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 13:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo, ndi dzanja lamphamvu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 M'tsogolo mwana wanu wamwamuna adzakufunsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Pamenepo inu mudzayankhe kuti, ‘Chauta adatitulutsa ku Ejipito, ku dziko laukapolo, ndi dzanja lake lamphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, ‘Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 13:14
29 Mawu Ofanana  

Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m'tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.


Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita, zizindikiro zake, ndi maweruzo a pakamwa pake.


Ndipo awa ndi akapolo anu ndi anthu anu, amene munawaombola ndi mphamvu yanu yaikulu, ndi dzanja lanu lolimba.


Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha.


Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.


Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.


ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita mu Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m'dziko la Ejipito.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine mu Ejipito.


Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.


Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;


ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito.


Yehova Mulungu wa Israele atero: Ndinapangana mapangano ndi makolo anu tsiku lija ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kutuluka m'nyumba ya ukapolo, kuti,


Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m'dziko la Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tachimwa, tachita choipa.


Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.


Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.


Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.


pamenepo mudzichenjera mungaiwale Yehova, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.


ndipo ngati ife sitinachite ichi chifukwa cha kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli chiyani inu kwa Yehova Mulungu wa Israele?


pakuti Yehova Mulungu wathu ndi Iye amene anatikweza kutitulutsa m'dziko la Ejipito kunyumba ya ukapolo, nachita zodabwitsa zazikuluzo pamaso pathu, natisunga m'njira monse tidayendamo, ndi pakati pa anthu onse amene tinapita pakati pao;


kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu?


nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawatulutsa m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.


Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israele, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ine ndinakukwezani kuchokera mu Ejipito, ndi kukutulutsani m'nyumba ya ukapolo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa