Eksodo 13:15 - Buku Lopatulika15 ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Farao atauma mtima ndithu, natikaniza kuchoka, Chauta adapha mwana wachisamba aliyense wamwamuna m'dziko lonse la Ejipito. Adapha ana a anthu ndi a zoŵeta omwe. Nchifukwa chake nyama yamphongo iliyonse yoyamba kubadwa imaperekedwa nsembe kwa Chauta. Koma ana athu achisamba aamuna, timachita choombola. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Farao atakanitsitsa kuti asatitulutse, Yehova anapha aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira ana a anthu ndi ziweto zomwe. Nʼchifukwa chake ine ndimapereka nsembe kwa Yehova, chachimuna chilichonse choyamba kubadwa ndipo mwana wamwamuna woyamba kubadwa ndimamuwombola.’ Onani mutuwo |