Luka 1:17 - Buku Lopatulika17 Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Molimba mtima ndiponso mwamphamvu monga mneneri Eliya, adzatsogolako Ambuye akubwera. Adzayanjanitsanso makolo ndi ana ao, adzatembenuza anthu osamvera kuti akhale ndi nzeru zonga za anthu olungama. Adzakonzera Ambuye anthu okonzekeratu kuŵatumikira.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.” Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.