Genesis 33:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Esau atayang'ana, adaona akazi ndi ana omwe aja, ndipo adamufunsa kuti, “Anthu aŵa ali ndi iweŵa nga yani?” Yakobe adayankha kuti, “Aŵa, mbuyanga, ndi ana amene Mulungu adandipatsa mwa chifundo chake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Kenaka Esau ataona amayi ndi ana awo anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi anthu amene uli nawowa ndi a ndani?” Yakobo anayankha kuti, “Awa ndi ana amene Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, wapereka kwa mtumiki wanune.” Onani mutuwo |