Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:10 - Buku Lopatulika

10 Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndodo yaufumu siidzachoka mwa Yuda, adzachita kuupanira ufumu umenewo, adzasunga mphamvu zake, mpaka mwiniwake weniweni atabwera, wodzalamulira anthu onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndodo yaufumu sidzachoka mwa Yuda, udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse, mpaka mwini wake weniweni atabwera ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:10
58 Mawu Ofanana  

Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthawi zonse.


Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.


Ana a Yuda akunyamula zikopa ndi mikondo ndiwo zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi atatu, okonzekeratu kunkhondo.


Ndipo anali komweko kwa Davide masiku atatu kudya ndi kumwa, popeza abale ao anazikonzeratu.


Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga; ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.


Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.


Adzandifikitsa ndani m'mzinda wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu?


koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.


Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.


Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.


Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira.


Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake.


Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.


Ndipo mkulu wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? Ati Yehova.


pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo.


Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zachifumu, za ochita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, ndipo zinaoneka m'kusomphoka kwao pakati pa nthambi zake zambiri.


Unatulukanso moto kundodo za kunthambi zake, unatha zipatso zake; m'mwemo ulibe ndodo yolimba ikhale ndodo yachifumu ya kuchita ufumu. Iyi ndi nyimbo idzakhala nyimbo ya maliro.


Ndidzagubuduzagubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.


Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati padziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndachinena.


Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.


Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.


Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.


ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.


Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


chitsime adakumba mafumu, adachikonza omveka a anthu; atanena mlamuli, ndi ndodo zao. Ndipo atachoka kuchipululu anamuka ku Matana;


Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.


Ndipo wina wotuluka mu Yakobo adzachita ufumu; nadzapasula otsalira m'mizinda.


Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!


ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;


Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha.


Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge Iye inu, ndi kumweruza Iye monga mwa chilamulo chanu. Ayuda anati kwa iye, Tilibe ulamuliro wakupha munthu aliyense;


Pa ichi Pilato anafuna kumasula Iye; koma Ayuda anafuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.


Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.


nati kwa iye, Muka, kasambe m'thamanda la Siloamu (ndilo losandulika, Wotumidwa). Pamenepo anachoka, nasamba, nabwera alikuona.


Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.


Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.


ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu.


Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa