Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:11 - Buku Lopatulika

11 Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa, ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika; natsuka malaya ake m'vinyo, ndi chofunda chake m'mwazi wa mphesa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa, ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika; natsuka malaya ake m'vinyo, ndi chofunda chake m'mwazi wa mphesa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Bulu wake amamumangirira ku mtengo wamphesa, mwanawabulu ku mpesa wabwino. Zovala zake amazichapa mu vinyo, mu vinyo wofiira ngati magazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndiye amene amamangirira bulu wake wamkazi kumtengo wa mpesa, ndi mwana wa bulu ku nthambi ya mpesa wabwino. Ndi iye amene amachapa zovala zake mu vinyo; ndi mkanjo wake mu vinyo wofiira ngati magazi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:11
15 Mawu Ofanana  

Maso ake adzafiira ndi vinyo, ndipo mano ake adzayera ndi mkaka.


Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.


Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.


mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu.


Taonani, akudza masiku, ati Yehova, akuti wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofetsa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.


Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.


mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa, ndi mafuta a anaankhosa, ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basani, ndi atonde, ndi impso zonenepa zatirigu; ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa.


Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe ndi la maiwe akutuluka m'zigwa, ndi m'mapiri;


dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uchi;


Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mzinda, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.


kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi aang'ono ndi aakulu.


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa