Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:9 - Buku Lopatulika

9 Yuda ndi mwana wa mkango, kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera; anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Yuda ndi mwana wa mkango, kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera; anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Yuda ali ngati msona wa mkango. Ukapha, umabwereranso kumalo kumene umabisala. Yuda ali ngati mkango, amatambasuka nagona pansi. Iye ndi mkangodi, ndipo palibe amene angalimbe mtima kuti amdzutse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yuda ali ngati mwana wa mkango; umabwerera ku malo ako ndi zofunkha, mwana wanga. Monga mkango, amadziwongola ndi kugona pansi, ndipo ngati mkango waukazi, ndani angalimbe mtima kumudzutsa?

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:9
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anaimika mikango khumi ndi iwiri mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko lililonse lina simunapangidwe wotere.


Ndi mpando wachifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi chopondapo mapazi chagolide, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo.


Pakuona tsono waukaziwo, kuti unalindirira, ndi kuti chiyembekezo chake chidatha, unatenga wina wa ana ake, numsandutsa msona.


Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.


Machitidwe ao sawalola kubwerera kwa Mulungu wao; pakuti mzimu wa uhule uli m'kati mwao, ndipo sadziwa Yehova.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.


Anaunthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.


Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.


Ndi za Gadi anati, Wodala iye amene akuza Gadi; akhala ngati mkango waukazi, namwetula dzanja, ndi pakati pamutu pomwe.


ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa