Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 78:4 - Buku Lopatulika

4 Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Sitidzabisira ana awo, tidzafotokozera mʼbado wotsatira ntchito zotamandika za Yehova, mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:4
17 Mawu Ofanana  

chimene adachinena anzeru, adachilandira kwa makolo ao, osachibisa;


kuti ndimveketse mau a chiyamiko, ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa.


Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani?


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine mu Ejipito.


Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.


Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina.


Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.


Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.


ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa