Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 78:5 - Buku Lopatulika

5 Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli, zimene analamulira makolo athu kuphunzitsa ana awo,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:5
21 Mawu Ofanana  

Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.


Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu, kuti munazikhazika kosatha.


Aonetsa mau ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele.


Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.


Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe, pakutuluka iye kudziko la Ejipito. Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.


Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.


Ndipo uziika m'likasamo mboni imene ndidzakupatsa.


Ndipo uziika chotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m'likasamo.


Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;


Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nutchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo.


Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.


Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Zambiri monsemonse: choyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo.


Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.


Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.


ndi kuti ana ao osadziwa amve, naphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu.


nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi.


izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israele, potuluka iwo mu Ejipito;


ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa