Masalimo 4:2 - Buku Lopatulika Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu inu, mudzaleka liti kunyoza ulemu wanga? Bwanji mukukondabe zinthu zachabechabe? Bwanji mukulakalakabe zinthu zonama? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? Sela. |
Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
Mudzaononga iwo akunena bodza; munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.
Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.
Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi?
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; yense wakulumbirira iye adzatamandira; pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa.
Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?
Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.
Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, chifukwa cha Kusi, amene anawatama, ndi Ejipito, amene anawanyadira.
Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.
Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.
Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.
atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?
Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.
Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?
Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.
musapatukire inu kutsata zinthu zachabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza zili zopanda pake.